Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 7

Akufa Adzauka!

Akufa Adzauka!

1-3. Kodi tonse tili m’jele ya ciani? Nanga Yehova adzaticotsamo bwanji?

YELEKEZANI kuti akuweluzani m’khoti kuti mudzakhala m’ndende umoyo wanu wonse, pa mlandu umene simunacite. Ndipo palibiletu ciyembekezo cakuti mudzacoka mu jele. Kutsogolo mungoonako zaka zamtatakuya za ukaidi. Nzelu zakuthelani, mucitoonelatu kuti palibiletu cimene mungacite. Koma pamene mwatailatu mtima conco, mukumva kuti pali munthu wina amene ali ndi mphamvu zokumasulani. Ndipo walonjeza kuti, zivute zitani, adzakumasulani ndithu! Kodi mungamvele bwanji?

2 Ife tonse tili m’ndende ya imfa. Ciliconse cimene tingacite sitingacoke m’manja mwa imfa. ndipo tiyenela kulandila cilango ca imfa. Koma Yehova ali ndi mphamvu zotimasula ku imfa. Ndipo anacita kulonjeza kuti: “Imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzaonongedwa.”—1 Akorinto 15:26.

3 Ha, ukomelenji ufulu wake! Ganizani cabe! Imfa kudzakhala kulibe. Si izo cabe. Yehova adzaukitsanso anthu amene anafa. Mudzamvela bwanji panthawi imeneyo? Mulungu analonjeza kuti, “anthu amene anafa” adzakhalanso ndi moyo. (Yesaya 26:19) Ndiye kuuka kwa akufa kumene Baibulo imakambapo.

MUNTHU AMENE TIMAKONDA AKAMWALILA

4. (a) N’ciani cingatitonthoze ngati wa m’banja kapena mnzathu wamwalila? (b) Kodi ena mwa mabwenzi a Yesu a pamtima anali ndani?

4 Ngati m’bululu wathu, kapena mnzathu wa pamtima wamwalila, timamvela cisoni kwambili. Timathedwa nzelu cifukwa sitingamuukitse. Koma Baibulo imatipatsa citonthozo ceni-ceni. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Tiyeni titenge citsanzo cimodzi coonetsa kuti Yehova ndi Yesu ni ofunitsitsa kukaukitsa abulu ŵathu ndi mabwenzi amene anamwalila. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anali kukonda kukaceza kwa Lazaro ndi azilongosi ake aŵili, Marita ndi Mariya. Onse atatu anali mabwenzi a Yesu a pamtima. Baibulo imakamba kuti: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” Koma tsiku lina, Lazaro anamwalila.—Yohane 11:3-5.

5, 6. (a) Yesu anacita ciani poona abululu ŵa Lazaro ndi mabwenzi awo akulila? (b) N’cifukwa ciani n’cinthu colimbikitsa mtima kudziŵa mmene imfa inamukhudzila Yesu?

5 Pamene Yesu anamvela za malilo, anayenda kukapeleka citonthozo kwa Marita ndi Mariya. Marita atamvela kuti Yesu akubwela, anayenda kukam’cingamila kunjila. Marita anakondwela kwambili kuona Yesu. Koma anamuuza kuti: “Mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalila.” Marita anaganiza kuti Yesu anacedwa kufika. Pamenepo, Yesu anaona Mariya, m’bale wake wa Marita akulila. Ataona cisoni cawo, cinam’khudza kwambili Yesu, cakuti naye analila. (Yohane 11: 21, 33, 35) Anamvela kuŵaŵa mu mtima, monga mmene tonse timamvelela ngati bululu wathu kapena munthu wina amene timakonda wamwalila.

6 N’cinthu cotonthoza mtima kudziŵa kuti Yesu nayenso imfa ya munthu imamuŵaŵa mu mtima mofanana ndi ife. Ndipo Yesu ni wofanana ndendende ndi Atate wake. (Yohane 14:9) Koma Yehova ali ndi mphamvu zocotsapo imfa kosatha, ndipo adzaicotselatu posacedwa.

“LAZARO, TULUKA!”

7, 8. N’cifukwa ciani Marita sanafune kuti cimwala acicotse pa manda a Lazaro? Nanga Yesu anacita ciani?

7 Pamene Yesu anafika ku manda a Lazaro, anapeza kuti pakhomo pake anaikapo cimwala cikulu kwambili. Ndiyeno Yesu anauza anthu kuti: “Cotsani cimwalaci.” Koma Marita sanafune kuti acite zimenezo, cifukwa mtembo wa Lazaro unali utakhala m’manda masiku anayi. (Yohane 11:39) Iye sanadziŵe zimene Yesu anali kufuna kucitila mlongosi wake.

Ganizani cabe mmene acibanja a Lazaro ndi anzake anasangalalila pamene Yesu anaukitsa Lazaro. —Yohane 11:38-44

8 Yesu anauza Lazaro kuti: “Tuluka!” Ndiyeno Marita ndi Mariya anaona zodabwitsa kwambili. “Wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamalilo.” (Yohane 11:43, 44) Inde, Lazaro anaukitsidwa. A banja ndi anzake anam’landila ndi manja aŵili Lazaro. Anam’gwila-gwila, kum’kumbatila, ndi kukamba naye. Cinali cozizwitsa ca dzaoneni! Ndithu Yesu anaukitsa Lazaro kwa akufa.

“KAMTSIKANA IWE, NDIKUNENA NDI IWE, DZUKA!”

9, 10. (a) N’ndani anapatsa Yesu mphamvu zoukitsa anthu? (b) Kodi nkhani za anthu amene anaukitsidwa ku manda zimatithandiza bwanji?

9 Kodi Yesu anali kuukitsa anthu mwa mphamvu zake? Iyai. Kuti Yesu aukitse Lazaro, coyamba anapemphela kwa Yehova, ndipo Yehova anam’patsa mphamvu zoukitsa Lazaro. (Ŵelengani Yohane 11:41, 42.) Ndipo si Lazaro yekha amene anaukitsidwa kwa akufa. Baibulo imatiuzanso za mtsikana wina wa zaka 12, amene anadwala kwambili. Yairo, tate wake wa mtsikanayo, anavutika mtima kwambili, cakuti anapempha Yesu kuti acilitse mwana wakeyo cifukwa anali mmodzi cabe. Yairo akali kukamba ndi Yesu, panafika amuna ena ndi kumuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalila! Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.” Koma Yesu anauza Yairo kuti: “Usaope, ingokhala ndi cikhulupililo basi, ndipo mwana wako apulumuka.” Ndiyeno anayenda nawo pamodzi ku nyumba kwa Yairo. Pamene anali kufika ku nyumba kwa Yairo, Yesu anapeza kuti anthu akulila. Koma anawauza kuti: “Tontholani, pakuti mwanayu sanamwalile ayi, koma akugona.” Makolo a mtsikanayo sanadziŵe zimene Yesu anali kutanthauza. Yesu anauza anthu onse kutuluka panja. Anatenga makolo a mtsikanayo n’kuloŵa nawo m’cipinda mmene munali mtembo wa mwana wawo. Ndiyeno Yesu anagwila dzanja la mwana uja n’kukamba kuti: “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, ‘Dzuka!’” Ganizilani cabe cisangalalo ca makolo ake, kuona mwana wawo uyo wanyamuka, n’kuyamba kuyenda! Zoona, Yesu anaukitsanso mtsikanayu. (Maliko 5:22-24, 35-42; Luka 8:49-56) Kucokela tsiku limenelo, kungoyang’ana mwana wawo, anali kukumbukila zimene Yehova anawacitila kupitila mwa Yesu. *

10 Koma anthu onse amene Yesu anaukitsa anafanso m’kupita kwa nthawi. Ngakhale n’conco, kuŵelenga nkhani zawo kumatipatsa ciyembekezo ceni-ceni. Yehova ni wofunitsitsa kuutsa anthu kumanda, ndipo adzacita ndithu zimenezi.

ZIMENE TIPHUNZILAPO PA NKHANI ZA ANTHU AMENE ANAUKITSIDWA

Mtumwi Petulo anaukitsa Dorika, mkazi wacikhiristu. —Machitidwe 9:36-42

Eliya anaukitsa mwana wa mkazi wamasiye. —1 Mafumu 17:17-24

11. Malinga ndi Mlaliki 9:5, tiphunzilapo ciani za Lazaro?

11 Baibulo imakamba mosapita m’mbali kuti “akufa sadziŵa ciliconse.” N’cimodzi-modzi ndi Lazaro, pamene anafa sanali kudziŵa ciliconse. (Mlaliki 9:5) Monga mwa mau a Yesu, cinali monga kuti Lazaro anali m’tulo. (Yohane 11:11) Pamene Lazaro anali m’manda, sanali ‘kudziŵa ciliconse.’

12. Kodi timadziŵa bwanji kuti Lazaro anaukitsidwa zoona?

12 Anthu ambili anaona pamene Yesu anaukitsa Lazaro. Ngakhale adani a Yesu nawo anadziŵa ndithu kuti Yesu anacita cozizwitsa cimeneco. Umboni wake unali wosatsutsika, cifukwa Lazaro anali wamoyo. (Yohane 11:47) Anthu ambili anayenda kukamuona Lazaro, ndipo anayamba kukhulupilila kuti zoona Yesu anatumidwa ndi Mulungu. Koma zimenezi zinakwiyitsa kwambili adani a Yesu, cakuti anayamba kupangana za kupha Yesu pamodzi ndi Lazaro.—Yohane 11:53; 12:9-11.

13. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalila?

13 Yesu anakamba kuti “onse ali m’manda acikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28) Mau amenewa atanthauza kuti anthu onse amene Yehova akumbukila adzauka. Koma kuti Yehova akaukitse wakufa aliyense, afunika kukumbukila mbali iliyonse ya munthu ameneyo. Kodi zimenezi n’zotheka kwa Mulungu? Ganizilani citsanzo ici. Kumwamba kuli nyenyezi mabiliyoni ambili-mbili. Koma Baibulo imakamba kuti Yehova amadziŵa dzina la nyenyezi iliyonse. (Ŵelengani Yesaya 40:26.) Conco, ngati Mulungu amakumbukila maina a nyenyezi zonse, ndiye kuti ni nkhani ing’ono kwa iye kukumbukila mbali zonse za anthu amene afuna kukaukitsa. Ndipo cikulu cofunika kukumbukila n’cakuti, Yehova ndiye analenga zinthu zonse. Conco, sitingakaike ngakhale pang’ono, kuti ali ndi mphamvu zoukitsa anthu amene anafa.

14, 15. Kodi mau a Yobu amatiphunzitsa ciani za kuuka kwa akufa?

14 Yobu munthu wokhulupilika, anali ndi cikhulupililo cakuti akufa adzaukitsidwa. Iye anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Ndiyeno anauza Yehova kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka nchito ya manja anu.” Zoona, Yobu anali kudziŵa kuti Yehova amafunitsitsa kuti akaukitse anthu amene anafa.—Yobu 14:13-15.

15 Nanga inu mumvela bwanji ndi nkhani yakuti akufa adzauka? Mwina muganizila za abululu ŵanu kapena anzanu amene anamwalila. Kodi nawo adzauka? Khazikani mtima pansi. Dziŵani kuti, Yehova amacita kulaka-laka kuti aukitse akufa. Koma ni anthu ati maka-maka amene adzaukitsidwa? Ndipo adzakhala kuti? Tiyeni tione mmene Baibulo iyankhila mafunso amenewa.

“ADZAMVA MAU AKE NDIPO ADZATULUKA”

16. Kodi anthu amene adzaukitsidwa pa dziko lapansi adzakhala ndi umoyo wabwanji?

16 Anthu amene anaukitsidwa m’nthawi zakale, abululu awo ndi anzawo anawalandila ndi manja aŵili pa dziko lapansi pano. Izi n’zimene zidzacitikanso mtsogolo, koma zidzapambana mmene zinacitikila kale. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa anthu amene adzaukitsidwa mtsogolo sadzafanso, adzalandila moyo wosatha. Cina n’cakuti, adzakhala m’dziko losiyana kwambili ndi limene tikhalamo lelo lino. M’dziko limenelo, mudzakhala mulibe nkhondo, ciwawa, ndi matenda.

17. Kodi ni anthu ŵati amene adzaukitsidwa?

17 Kodi n’ndani amene adzaukitsidwa? Yesu anakamba kuti “onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake.” (Yohane 5:28, 29) Ndipo pa Chivumbulutso 20:13 pakamba kuti: “Nyanja inapeleka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapeleka akufa amene anali mmenemo.” Inde, anthu mabiliyoni ambili adzaukitsidwa. Naye mtumwi Paulo anakamba kuti anthu “olungama ndi osalungama” adzaukitsidwa. (Ŵelengani Machitidwe 24:15.) Kodi zimenezi zitanthauza ciani?

M’Paradaiso, akufa adzauka, ndipo a banja ndi anzawo adzakondwela kuwalandila

18. Kodi “olungama” amene adzaukitsidwa n’ndani?

18 “Olungama” amene adzaukitsidwa aphatikizapo atumiki onse a Yehova okhulupilika amene anakhalako Yesu akalibe kubwela pa dziko lapansi. Ena mwa anthu amenewo ni Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute, ndi Esitele. Onse aŵa adzakhalanso ndi moyo pa dziko lapansi. Mungaŵelenge za iwo mu Aheberi caputala 11. Nanga bwanji za atumiki a Yehova okhulupilika amene amafa masiku ano? Nawonso ni “olungama,” ndipo adzaukitsidwa.

19. Kodi “osalungama” n’ndani? Ndipo Yehova adzawapatsa mwayi wanji?

19 “Osalungama” amaphatikizapo anthu mabiliyoni ambili amene sanakhalepo ndi mwayi wodziŵa za Yehova. Ngakhale kuti anafa, Yehova sanawaiŵale. Adzawaukitsa ndi kuwapatsa mwayi wakuti akaphunzile za iye ndi kum’tumikila.

20. N’cifukwa ciani anthu ena sadzaukitsidwa?

20 Kodi ndiye kuti munthu aliyense cabe amene anamwalila adzaukitsidwa? Iyai. Yesu anakamba kuti anthu ena sadzaukitsidwa. (Luka 12:5) Nanga n’ndani adzasankha kuti uje adzauka, uje sadzauka? Yehova ndiye woweluza mkulu. Koma anapatsako Yesu mphamvu ‘zoweluza anthu amoyo ndi akufa.’ (Machitidwe 10:42) Ngati munthu adzaweluzidwa kuti ni woipilatu cifukwa cokanilatu kusintha, akafa wafelatu sadzaukitsidwa.—Onani Zakumapeto 19.

KUUKITSIDWA KOYENDA KUMWAMBA

21, 22. (a) Kodi amene amaukitsidwa kuti ayende kumwamba amaukitsidwa bwanji? (b) Nanga n’ndani anali woyamba kuukitsidwa kuti ayende kumwamba?

21 Baibulo imatiuza kuti anthu ena adzayenda kukakhala kumwamba. Ngati munthu waukitsidwa kuti ayende kumwamba, saukitsidwa ndi thupi lanyama. Amaukitsidwa ndi thupi lamzimu.

22 Yesu ndiye anali woyamba kuukitsidwa ndi thupi lamzimu. (Yohane 3:13) Yesu atagona m’manda masiku atatu, Yehova anamuukitsa. (Salimo 16:10; Machitidwe 13:34, 35) Sanamuukitse ndi thupi laumunthu. Mtumwi Petulo anakamba kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” (1 Petulo 3:18) Yesu anaukitsidwa monga munthu wamphamvu wamzimu. (1 Akorinto 15:3-6) Ndipo Baibulo inakambilatu kuti padzakhalanso ena amene adzaukitsidwa mwa njila imeneyi.

23, 24. Kodi “kagulu ka nkhosa” kamene Yesu anakamba n’ndani? Ndipo adzakhala angati?

23 Yesu ali pafupi kuphedwa, anauza ophunzila ake okhulupilika kuti: “Ndikupita kukakukonzelani malo.” (Yohane 14:2) Cimene anatanthauza n’cakuti, otsatila ake ena adzaukitsidwa kuti akakhale naye kumwamba. Kodi anafunikila kukhala angati? Yesu anakamba kuti ni anthu ocepa, kapena kuti “kagulu ka nkhosa.” (Luka 12:32) Mtumwi Yohane anacita kuchula ciŵelengelo ceni-ceni. Iye anakamba kuti anaona Yesu “ataimilila pa Phili la Ziyoni [kumwamba]. Limodzi naye panali enanso 144,000.”—Chivumbulutso 14:1.

24 Kodi Akhiristu okwana 144,000 amenewa anafunikila kuyamba liti kuukitsidwa? Baibulo imaonetsa kuti ni pambuyo pakuti Khiristu wayamba kulamulila kumwamba. (1 Akorinto 15:23) Ife tili mkati mwa nthawi imeneyo, cifukwa Yesu anayamba kale kulamulila. Ndipo pano tikamba, unyinji wa Akhiristu 144,000 amenewo anaukitsidwa kale ali kumwamba. Awo amene akali ndi moyo pa dziko lapansi, amati akamwalila, pa nthawi imeneyo amaukitsidwa ndi kuyenda kumwamba. Koma anthu ena onse, amene sali m’kagulu kameneka, adzaukitsidwa mtsogolo kuti akakhale ndi moyo m’Paradaiso pa dziko lapansi.

25. Kodi tidzaphunzila za ciani m’nkhani yotsatila?

25 Posacedwa, Yehova adzamasula anthu onse ku imfa, ndipo imfa idzacotsedwapo kothelatu. (Ŵelengani Yesaya 25:8.) Nanga aja amene apita kumwamba, kodi ayenda kukacita ciani? Baibulo imakamba kuti ayenda kukalamulila pamodzi ndi Yesu m’boma la Ufumu wa Mulungu. Tidzaphunzila zambili za boma limeneli m’nkhani yotsatila.

^ ndime 9 Baibulo imatiuzanso za anthu ena amene anaukitsidwa, acicepele ndi acikulile, amuna ndi akazi, ndiponso Aisiraeli ndi anthu akunja. Mungaŵelenge za iwo pa malemba aya: 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Mateyu 28:5-7; Luka 7:11-17; 8:40-56; ndi Machitidwe 9:36-42; 20:7-12.