Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 8

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

1. Kodi tidzakambilana pemphelo liti lodziŵika kwambili?

ANTHU ambili amalidziŵa pemphelo la Atate Wathu Wakumwamba, kapena kuti Pemphelo la Ambuye. Yesu anapeleka pemphelo limeneli monga citsanzo pophunzitsa otsatila ake mopemphelela. Kodi Yesu anapempha ciani m’pemphelo limenelo? Ndipo n’cifukwa ciani pemphelo limeneli n’lofunika kwa ife?

2. N’zinthu zofunika zitatu ziti zimene Yesu anatiphunzitsa kupempha m’mapemphelo athu?

2 Yesu anati: “Koma inu muzipemphela motele: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe. Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.’” (Ŵelengani Mateyu 6:9-13.) N’cifukwa ciani Yesu anatiphunzitsa kupempha zinthu zitatu zimenezi?—Onani Zakumapeto 20.

3. Kodi m’nkhani ino tidzaphunzila ciani za Ufumu wa Mulungu?

3 Tinaphunzila kuti dzina la Mulungu ni Yehova. Tinaphunzilanso colinga ca Mulungu kwa anthu ndi dziko lapansi. Koma kodi Yesu anatanthauzanji pamene anapemphela kuti “Ufumu wanu ubwele”? Tidzaphunzila kuti kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Nanga udzacita ciani? Ndipo udzayeletsa bwanji dzina la Mulungu?

KODI UFUMU WA MULUNGU N’CIANI?

4. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciani? Nanga Mfumu yake n’ndani?

4 Yehova anakhazikitsa boma lake kumwamba, ndipo anasankha Yesu kukhala Mfumu ya boma limenelo. Baibulo imatiuza kuti boma limeneli ni Ufumu wa Mulungu. Yesu ni “Mfumu ya olamulila monga mafumu ndi Mbuye wa olamulila monga ambuye.” (1 Timoteyo 6:15) Yesu adzakonza zinthu kupambana munthu aliyense wolamulila. Ndipo ngakhale olamulila aumunthu onse kuwaika pamodzi, amacepelatu mphamvu kwa Yesu.

5. Kodi likulu la boma la Mulungu lidzakhalila kuti? Nanga bomalo lidzalamulila kuti?

5 Patapita masiku 40 Yesu ataukitsidwa, anabwelela kumwamba. M’kupita kwa nthawi, Yehova anamuika kukhala Mfumu ya Ufumu wake. (Machitidwe 2:33) Ngakhale kuti likulu la boma la Mulungu lidzakhalila kumwamba, bomalo lidzalamulila dziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 11:15) Ndiye cifukwa cake Baibulo imachula bomalo kuti ‘Ufumu wakumwamba.’—2 Timoteyo 4:18.

6, 7. N’cifukwa ciani Yesu ni mfumu yopambana mfumu iliyonse yaumunthu?

6 Baibulo imatiuza kuti Yesu ni mfumu ikulu kupambana mfumu iliyonse yaumunthu cifukwa iye “ali ndi moyo wosakhoza kufa.” (1 Timoteyo 6:16) Olamulila onse aumunthu amafa m’kupita kwa nthawi, koma Yesu sadzafa. Conco, zabwino zonse zimene Yesu adzaticitila zidzakhala kwamuyaya.

7 Ulosi wa m’Baibulo umalonjeza kuti Yesu adzakhala Mfumu ya cilungamo ndi ya cifundo. Baibulo imati: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzelu, womvetsa zinthu, wolangiza, wamphamvu, wodziŵa zinthu ndi woopa Yehova. Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova. Sadzaweluza potengela zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengela zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweluza mwacilungamo anthu onyozeka.” (Yesaya 11:2-4) Kodi simungakonde kukhala ndi mfumu ngati imeneyi?

8. Tidziŵa bwanji kuti Yesu sadzalamulila yekha?

8 Mulungu wasankha anthu ena kuti akalamulile ndi Yesu m’boma lakumwamba. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti: “Tikapitiliza kupilila, tidzalamulilanso limodzi ndi iye monga mafumu.” (2 Timoteyo 2:12) Nanga ni anthu angati amene adzalamulila pamodzi ndi Yesu monga mafumu?

9. Ni angati amene adzalamulila ndi Yesu? Nanga Mulungu anayamba liti kuwasankha?

9 M’Nkhani 7, tinaphunzila kuti mtumwi Yohane anapatsidwa masomphenya. Anaona Yesu ali Mfumu kumwamba pamodzi ndi mafumu ena okwana 144,000. Kodi okwana 144,000 amenewo n’ndani? Mtumwi Yohane anafotokoza kuti iwo ni “olembedwa dzina [la Yesu] ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.” Ndipo anati: “Amenewa ndiwo amatsatila Mwanawankhosa [kutanthauza Yesu] kulikonse kumene akupita. Iwowa anagulidwa kucokela mwa anthu.” (Ŵelengani Chivumbulutso 14:1, 4.) Conco, a 144,000 amenewa ni Akhiristu okhulupilika amene Mulungu wasankha kuti iwo pamodzi ndi Yesu, akakhale “mafumu olamulila dziko lapansi.” Anthu amenewa akamwalila amaukitsidwa ndi kuyenda kumwamba. (Chivumbulutso 5:10) Kuyambila m’nthawi ya atumwi, Yehova wakhala akusankha Akhiristu okhulupilika kukhala m’gulu limeneli la mafumu okwana 144,000.

10. N’cifukwa ciani cili cikondi ca Yehova kusankha Yesu ndi a 144,000 kuti akalamulile anthu?

10 Yehova amatikonda kwambili. Ndiye cifukwa cake anakonza zakuti anthu akalamulile pamodzi ndi Yesu. Yesu adzakhala wolamulila wabwino cifukwa amatimvetsetsa. Iye anakhalapo munthu ndipo kuvutika amakudziŵa bwino. Paulo anakamba kuti Yesu ‘amatimvelela cisoni pa zofooka zathu, ndipo anayesedwa m’zonse ngati ife.’ (Aheberi 4:15; 5:8) A 144,000 amadziŵa mavuto amene ife anthu timakumana nawo. Nawonso akhala akuvutika ndi matenda ndi kupanda ungwilo. Conco, sitipeneka ngakhale pang’ono, kuti Yesu ndi a 144,000 amamvetsetsa mavuto amene timakumana nawo.

KODI UFUMU WA MULUNGU UDZACITA CIANI?

11. N’cifukwa ciani Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kuti cifunilo ca Mulungu cicitike kumwamba?

11 Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kuti cifunilo ca Mulungu cicitike kumwamba. Cifukwa ciani? M’Nkhani 3, tinaphunzila kuti Satana Mdyelekezi anapandukila Yehova. Satana atapanduka, Yehova anamulola pamodzi ndi angelo amene anapanduka naye, kapena kuti ziŵanda, kukhala kumwamba kwa kanthawi. Conco, si onse anali kucita cifunilo ca Mulungu kumwamba. M’Nkhani 10 tidzaphunzila zambili za Satana ndi ziŵanda.

12. Kodi pa Chivumbulutso 12:10, amasimbapo zocitika ziŵili ziti zofunika kwambili?

12 Baibulo inakambilatu kuti pamene Yesu adzangoikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzamenyana nkhondo ndi Satana. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:7-10.) Vesi 10 imasimba zocitika ziŵili zofunika kwambili. Coyamba, Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulila, ndipo Mfumu yake ni Yesu. Caciŵili, Satana aponyedwa ku dziko lapansi. Pamene tiphunzila, mudzaona kuti zonse ziŵili zimenezi zinacitika kale.

13. N’ciani cinacitika kumwamba pamene Satana anam’pilikitsako?

13 Baibulo imafotokoza kuti pamene Satana ndi ziŵanda zake anaponyedwa pa dziko, angelo anali pa cisangalalo cadzaoneni! Baibulo imati: “Kondwelani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko.” (Chivumbulutso 12:12) Pali pano kumwamba kuli mtendele ndi umodzi, cifukwa aliyense kumeneko amacita cifunilo ca Mulungu.

Kucokela pamene Satana ndi ziŵanda zake anawathamangitsa kumwamba, pa dziko lapansi pakhala mavuto okha-okha. Koma mavuto onsewo adzatha lomba apa

14. Kodi zinthu zili bwanji pa dziko lapansi cimuthamangitsileni Satana kumwamba?

14 Koma pa dziko lapansi pano umoyo ni wovuta kwambili. Pamacitika zinthu zoipa kwambili ‘cifukwa Mdyelekezi anatsikila’ ku dziko lapansi. Ndiponso, iye “ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.” (Chivumbulutso 12:12) Satana ni wolusa ndi mkwiyo. Zili zonco cifukwa anam’pilikitsa kumwamba n’kumuponyela ku dziko lapansi, ndipo adziŵa kuti lomba apa, adzawonongedwa. N’cifukwa cake manje ali pakaliki-liki kusokoneza zinthu, kuwonjezela mavuto, ndi kuvutitsa anthu kulikonse pa dziko lapansi.

15. Kodi Mulungu ali nalo colinga canji dziko lapansi?

15 Ngakhale n’conco, colinga ca Mulungu ca dziko lapansi sicinasinthe. Iye akali kufuna kuti anthu angwilo akakhale ndi moyo kwamuyaya m’paradaiso pa dziko lapansi. (Salimo 37:29) Kodi Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa bwanji zimenezi?

16, 17. Lemba la Danieli 2:44 limatiuzanji za Ufumu wa Mulungu?

16 Ulosi wa pa Danieli 2:44 umati: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” Kodi ulosi umenewu utiphunzitsa ciani za Ufumu wa Mulungu?

17 Coyamba, umatiuza kuti Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila “m’masiku a mafumu amenewo.” Zimenezi zinatanthauza kuti pamene Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila, maboma ena adzakhala akalipo pa dziko lapansi. Caciŵili, utiuza kuti Ufumu wa Mulungu ni wamuyaya, ndipo palibe boma lina limene lidzaloŵa m’malo mwake. Ndipo cacitatu, ulosiwu utiuza kuti padzakhala nkhondo pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a pa dziko lapansi. Koma Ufumu wa Mulungu udzapambana, ndipo udzakhala boma lokha cabe limene lidzalamulila pa dziko lonse lapansi. Pamenepo, anthu adzakhala ndi boma labwino kupambana onse amene akhalapo.

18. Kodi nkhondo yotsilizila ya pakati pa Ufumu wa Mulungu ndi maboma a pa dziko lapansi ni nkhondo yanji?

18 Kodi Ufumu wa Mulungu udzacotsapo bwanji maulamulilo ali pa dziko lapansi? Ikalibe kucitika nkhondo yotsilizila nkhondo ya Aramagedo, ziŵanda zidzasoceletsa ‘mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti zikawasonkhanitsile pamodzi ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Inde, maboma a anthu adzalimbana ndi Ufumu wa Mulungu.—Chivumbulutso 16:14, 16; onani Zakumapeto 10.

19, 20. N’cifukwa ciani timafunika Ufumu wa Mulungu kuti ulamulile dziko lapansi?

19 Kodi n’cifukwa ciani tifunika Ufumu wa Mulungu? Pali zifukwa zikulu-zikulu zitatu. Coyamba, ndife anthu ocimwa, n’cifukwa cake timadwala ndi kufa. Koma Baibulo imatiuza kuti mu Ufumu wa Mulungu, tonse tidzakhala ndi moyo wamuyaya. Lemba la Yohane 3:16 limati: “Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

20 Cifukwa caciŵili n’cakuti anthu oipa ali kulikonse. Anthu ambili amanama, kuba, kucita zaciwelewele, zaciwawa, ndi zoipa zina zambili-mbili. Palibe munthu amene angakwanitse kuwacotsapo anthu amenewo, koma Mulungu yekha cabe. Conco, anthu onse amene apitiliza kucita zoipa, Mulungu adzawawononga pa nkhondo ya Aramagedo. (Ŵelengani Salimo 37:10.) Cifukwa cacitatu cimene tifunikila Ufumu wa Mulungu n’cakuti maboma a anthu akangiwa. Alibenso mphamvu zeni-zeni pa anthu awo, ni ankhanza, ndiponso kolapushoni ili paliponse. Iwo salimbikitsa anthu kumvela Mulungu. N’cifukwa cake Baibulo imati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.”—Mlaliki 8:9.

21. Kodi Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa bwanji cifunilo ca Mulungu pa dziko lapansi?

21 Aramagedo ikapita, Ufumu wa Mulungu udzaonetsetsa kuti cifunilo ca Mulungu cacitika pa dziko lapansi. Mwacitsanzo, udzacotsa Satana ndi ziŵanda zake. (Chivumbulutso 20:1-3) M’kupita kwa nthawi, kudzakhala kulibe kudwala kapena kufa. Cifukwa ca dipo la Yesu, anthu onse okhulupilika adzakhala ndi moyo kwamuyaya m’Paradaiso. (Chivumbulutso 22:1-3) Pamenepo Ufumuwo udzayeletsa dzina la Mulungu. Kutanthauza ciani? Kutanthauza kuti, boma la Mulungu likadzayamba kulamulila dziko lapansi, anthu onse adzalemekeza dzina la Yehova.—Onani Zakumapeto 21.

KODI YESU ANAKHALA LITI MFUMU?

22. Tidziŵa bwanji kuti Yesu sanakhale Mfumu pamene anali pa dziko lapansi, kapena pamene anangouka kwa akufa?

22 Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele.” Conco, kunali koonekelatu kuti boma la Mulungu lidzabwela kutsogolo. Coyamba, Yehova anali kudzakhazikitsa boma ndi kuika Yesu kukhala Mfumu. Kodi pamene Yesu anabwelela kumwamba, anaikidwa kukhala Mfumu pa nthawi imeneyo? Ayi. Iye anafunika kuyembekezela. Petulo ndi Paulo anaimveketsa bwino mfundo imeneyi patapita nthawi, pambuyo pakuti Yesu anaukitsidwa. Pogwilitsila nchito ulosi wa pa Salimo 110:1, iwo anaonetsa kuti Yesu sanayambe kulamulila pamene anangobwelela kumwamba. Mu ulosi umenewu, Yehova anati: “Khala kudzanja langa lamanja kufikila nditaika adani ako monga copondapo mapazi ako.” (Machitidwe 2:32-35; Aheberi 10:12, 13) Kodi Yesu anafunika kuyembekeza kwa utali wanji kuti Yehova amuike kukhala Mfumu?

Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa cifunilo ca Mulungu pa dziko lapansi

23. (a) Kodi Yesu anayamba liti kulamulila monga Mfumu m’boma la Mulungu? (b) Nanga tidzaphunzilanji m’nkhani yotsatila?

23 Caka ca 1914 cisanafike, Akhiristu oona anadziŵilatu kuti caka cimeneco cidzakhala capadela, malinga ndi ulosi wa m’Baibulo. Kungocokela m’caka ca 1914, zocitika za pa dziko lapansi zionetsa kuti Akhiristuwo anakamba zoona. M’caka cimeneco ca 1914, Yesu anayamba kulamulila monga Mfumu. (Salimo 110:2) Pasanapite nthawi, Satana anaponyedwa ku dziko lapansi, cakuti pano tikamba Satana “wangotsala ndi kanthawi kochepa” cabe. (Chivumbulutso 12:12) M’nkhani yotsatila, tidzaona umboni wina woonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Tidzaphunzilanso kuti lomba apa, Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa cifunilo ca Mulungu pa dziko lapansi.—Onani Zakumapeto 22.