Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 10

Zimene Tiyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

Zimene Tiyenera Kudziwa Zokhudza Angelo

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira za angelo?

YEHOVA amafuna kuti tidziwe banja lake. Ndipo ena amene ali m’banja limeneli ndi angelo. Baibulo limawafotokoza kuti ndi ‘ana a Mulungu.’ (Yobu 38:7) Koma kodi angelo amagwira ntchito zotani? Kodi achitapo zinthu zotani pothandiza anthu m’mbuyomu? Nanga kodi ifeyo angatithandize?—Onani Mawu Akumapeto 8.

2. Kodi angelo anachokera kuti, nanga alipo angati?

2 Tikufunika kudziwa kuti angelo anachokera kuti. Lemba la Akolose 1:16 limanena kuti Yehova analenga Yesu, kenako “zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” Zinthu zimene zinalengedwazo zikuphatikizapo angelo. Koma kodi ndi angelo angati amene analengedwa? Baibulo limasonyeza kuti Mulungu analenga angelo mamiliyoni ambiri.—Salimo 103:20; Chivumbulutso 5:11.

3. Kodi lemba la Yobu 38:4-7 limatiuza chiyani za angelo?

3 Baibulo limatiuzanso kuti Yehova analenga angelo dziko lapansili lisanalengedwe. Kodi angelo anamva bwanji dzikoli litalengedwa? Buku la Yobu limatiuza kuti iwo anasangalala kwambiri. Iwo ankatumikira Yehova mogwirizana.—Yobu 38:4-7.

ANGELO AMATHANDIZA ATUMIKI A MULUNGU

4. Kodi tikudziwa bwanji kuti angelo amachita chidwi ndi zochita za anthu?

4 Kuyambira kale angelo akhala akuchita chidwi ndi zimene anthu amachita komanso cholinga chimene Yehova anali nacho pamene ankalenga dziko lapansi ndi anthu. (Miyambo 8:30, 31; 1 Petulo 1:11, 12) Ziyenera kuti zinawakhumudwitsa kwambiri pamene Adamu ndi Hava anasiya kumvera Mulungu. Panopa ayenera kuti ndi okhumudwanso kwambiri chifukwa anthu ambiri samvera Yehova. Koma munthu akalapa n’kuyambiranso kuchita zimene Mulungu amafuna, angelo amasangalala kwambiri. (Luka 15:10) Angelo amachita chidwi kwambiri ndi anthu amene amatumikira Mulungu ndipo Yehova amagwiritsira ntchito angelowo pothandiza komanso kuteteza atumiki ake padziko lapansi. (Aheberi 1:7, 14) Tiyeni tione zitsanzo zingapo pa nkhaniyi.

“Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.”—Danieli 6:22

5. Kodi angelo anathandiza bwanji atumiki a Mulungu m’mbuyomu?

5 Yehova anatumiza angelo awiri kuti akathandize Loti ndi banja lake kuthawa pamene Mulungu ankafuna kuwononga mizinda ya Sodomu ndi Gomora. (Genesis 19:15, 16) Patapita zaka zambirimbiri, mneneri Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango koma sanavulazidwe chifukwa ‘Mulungu anatumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikangoyo.’ (Danieli 6:22) Patapita nthawi mtumwi Petulo anatsekeredwa m’ndende ndipo Yehova anatumiza mngelo kuti akam’masule. (Machitidwe 12:6-11) Angelo ankamuthandizanso Yesu pamene anali padziko lapansi. Mwachitsanzo, atabatizidwa “angelo anam’tumikira.” (Maliko 1:13) Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, mngelo ‘anamulimbikitsa.’—Luka 22:43.

6. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti angelo amathandizabe atumiki a Mulungu masiku ano? (b) Kodi tikambirana mayankho a mafunso ati?

6 Angelo saonekeranso kwa anthu masiku ano koma Mulungu amawagwiritsabe ntchito pothandiza atumiki ake. Baibulo limati: “Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.” (Salimo 34:7) Kodi n’chifukwa chiyani timafunika kutetezedwa? Chifukwa chakuti tili ndi adani amphamvu kwambiri amene akufuna kutivulaza. Kodi adani amenewa ndi ndani? Kodi amakhala kuti? Nanga akufuna kutivulaza motani? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tikambirane zimene zinachitika pasanadutse nthawi yaitali Adamu ndi Hava atalengedwa.

ADANI ATHU OMWE SITINGAWAONE

7. Kodi anthu ena achita chiyani chifukwa chopusitsidwa ndi Satana?

7 M’Mutu 3 tinaphunzira kuti mngelo wina amene ankafuna kuti azilamulira ena, anapandukira Mulungu. Baibulo limanena kuti dzina la mngelo ameneyu ndi Satana Mdyerekezi. (Chivumbulutso 12:9) Satana amafuna kuti anthu enanso asiye kuchita zimene Mulungu amafuna. Iye anakwanitsa kupusitsa Hava, ndipo kuchokera nthawi imeneyo wakhala akupusitsa anthu enanso ambirimbiri. Komabe anthu ena, monga Abele, Inoki ndi Nowa, anapitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova.—Aheberi 11:4, 5, 7.

8. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti angelo ena akhale ziwanda? (b) Kodi ziwanda zinachita chiyani kuti zipulumuke pa nthawi ya Chigumula?

8 M’nthawi ya Nowa, angelo ena anasiya kuchita zimene Mulungu amafuna ndipo anachoka kumwamba n’kuyamba kukhala padziko lapansi pano ngati anthu. Kodi anachita zimenezi chifukwa chiyani? Baibulo limanena kuti iwo anachita zimenezi chifukwa ankafuna kukwatira akazi apadziko lapansi. (Werengani Genesis 6:2.) Koma zimenezi si zoyenera kuti angelo azichita. (Yuda 6) Anthu ambiri pa nthawiyo anatengera makhalidwe oipa a angelo amenewo moti anayamba kuchita zachinyengo komanso zachiwawa. Yehova ataona zimenezi anaganiza zobweretsa Chigumula, kapena kuti mvula yambiri. Chigumulachi chinachititsa kuti madzi asefukire padziko lonse lapansi n’kuwononga anthu onse oipa. Koma anapulumutsa atumiki ake okhulupirika. (Genesis 7:17, 23) Kuti asafe, angelo oipa aja anabwerera kumwamba. M’Baibulo angelo oipa amenewa amadziwika ndi dzina lakuti ziwanda. Angelo amenewa anasankha kugwirizana ndi zochita za Satana, ndipo zimenezi zinachititsa kuti Mdyerekezi akhale wolamulira wawo.—Mateyu 9:34.

9. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira ziwanda, zitabwerera kumwamba? (b) Kodi tikambirana chiyani?

9 Chifukwa choti ziwandazi zinaukira ulamuliro wake, Yehova sanazilole kukhalanso m’banja lake. (2 Petulo 2:4) Panopa ziwandazi sizingathenso kusintha n’kukhala anthu, komabe zikupitiriza ‘kusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’ (Chivumbulutso 12:9; 1 Yohane 5:19) Tiyeni tikambirane njira zimene zimagwiritsa ntchito kuti zisocheretse, kapena kuti kupusitsa, anthu ambiri.—Werengani 2 Akorinto 2:11.

MMENE ZIWANDA ZIMAPUSITSIRA ANTHU

10. Kodi ziwanda zimapusitsa bwanji anthu?

10 Ziwanda zili ndi njira zambiri zopusitsira anthu. Anthu ena amalankhulana ndi ziwanda kudzera mwa asing’anga kapena anthu ena amatsenga, ndipo nthawi zina amalankhulana nazo okha. Kulankhulana ndi ziwanda kumeneku, ndi komwe Baibulo limakutchula kuti kukhulupirira mizimu. Komatu Baibulo limatilamula kuti tisamachite chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. (Agalatiya 5:19-21) Kodi limaletsa zimenezi chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti kukhulupirira mizimu ndi msampha umene ziwanda zimagwiritsa ntchito pofuna kupusitsa anthu komanso kuti zizilamulira zochita za anthuwo.—Onani Mawu Akumapeto 26.

11. Kodi kuwombeza n’kutani, nanga n’chifukwa chiyani sitiyenera kuwombeza?

11 Njira imodzi imene ziwanda zimagwiritsa ntchito pofuna kupusitsa anthu ndi kuwombeza. Kuwombeza kumatanthauza kugwiritsa ntchito matsenga pofuna kudziwa zinthu zam’tsogolo kapena zinthu zina zovuta kuzizindikira. Ena amachita zimenezi poona pagalasi la matsenga, kutanthauzira mizere ya m’manja, kutanthauzira kulira kwa mbalame, kumasulira maloto kapena kukhulupirira nyenyezi. Anthu ambiri amaona kuti kuchita zimenezi kulibe vuto lililonse, koma zimenezi si zoona. Kuwombeza n’koopsa kwambiri. Mwachitsanzo, Baibulo limasonyeza kuti anthu olosera zam’tsogolo amathandizidwa ndi ziwanda. Lemba la Machitidwe 16:16-18 limatiuza za “chiwanda cholosera zam’tsogolo” chimene chinkachititsa mtsikana wina kuti azilosera zinthu. Koma mtumwi Paulo atachotsa chiwandacho, mtsikanayo sankathanso kulosera zam’tsogolo.

12. (a) Kodi kulankhula ndi akufa n’koopsa bwanji? (b) N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu sachita nawo miyambo iliyonse yogwirizana ndi ziwanda?

12 Pali njira inanso imene ziwanda zimagwiritsa ntchito pofuna kupusitsa anthu. Zimafuna kuti tizikhulupirira kuti n’zotheka kulankhulana ndi anthu amene anamwalira. Zimafunanso kuti tizikhulupirira kuti anthu amene anamwalira adakali ndi moyo kwinakwake ndipo akhoza kulankhula nafe kapena kutichitira zinazake zoopsa. Mwachitsanzo, anthu ena mnzawo kapena m’bale wawo akamwalira, amapita kwa munthu wamatsenga yemwe amawauza kuti akhoza kulankhulana ndi munthu amene anamwalirayo. Wamatsengayo akhoza kuwauza nkhani yosangalatsa yokhudza munthu womwalirayo kapenanso akhoza kulankhula mawu omveka ngati mmene munthu womwalirayo ankalankhulira. (1 Samueli 28:3-19) Miyambo yambiri imene imachitika pa maliro imasonyezanso kuti anthu amakhulupirira kuti wakufayo adakali ndi moyo kwinakwake. Miyambo imeneyi ikuphatikizapo kukonza phwando pa tsiku lamaliro, kuchita mwambo wokumbukira tsiku limene munthu winawake anamwalira, kupereka nsembe kwa akufa, kulondera maliro ndiponso miyambo ya mmene munthu ayenera kulirira maliro a mwamuna kapena mkazi wake. Akhristu akakana kuchita nawo zimenezi, abale awo komanso anthu ena a m’mudzi amayamba kuwanena, kuwakayikira kapenanso kuwasala. Komabe Akhristu amadziwa kuti munthu akamwalira sakhalanso ndi moyo kwinakwake moti n’zosatheka kulankhula naye ndipo sangachite chilichonse choopsa. (Salimo 115:17) Muyenera kusamala kwambiri ndipo musamayese kulankhulana ndi akufa kapena ziwanda kapena kuchita miyambo iliyonse yokhudzana ndi ziwanda.—Werengani Deuteronomo 18:10, 11; Yesaya 8:19.

13. Kodi panopa zinthu zili bwanji kwa anthu ambiri amene poyamba ankaopa ziwanda?

13 Sikuti ziwanda zimangopusitsa anthu, koma zimawaopsezanso. Masiku ano, Satana ndi ziwanda zake akudziwa kuti angotsala ndi “kanthawi kochepa” kuti awonongedwe ndi Mulungu, choncho ndi okwiya kwambiri komanso ankhanza kuposa kale. (Chivumbulutso 12:12, 17) Komabe, anthu ambiri omwe poyamba ankaopa ziwanda panopa anamasuka moti saziopanso. Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti asamaopenso ziwanda?

MMENE TINGAPEWERE ZIWANDA

14. Potengera zimene Akhristu akale anachita, kodi ifeyo tiyenera kuchita chiyani kuti ziwanda zisiye kutivutitsa?

14 Baibulo limatiuza mmene tingapewere ziwanda komanso zimene tingachite kuti timasuke ngati tinayamba kale kuzikhulupirira. Mwachitsanzo, anthu ena a mumzinda wa Efeso ankakhulupirira ziwanda asanakhale Akhristu. Kodi anatani kuti asiye zimenezi? Baibulo limati: “Ambiri ndithu amene anali kuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” (Machitidwe 19:19) Pamene ankafuna kukhala Akhristu, anthu amenewa anawononga mabuku onse a zamatsenga amene anali nawo. Zimenezi ndi zimene nafenso tiyenera kuchita. Aliyense amene akufuna kuyamba kutumikira Yehova ayenera kutaya kapena kuwononga chinthu chilichonse chimene ali nacho chogwirizana ndi ziwanda. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo mabuku, magazini, mafilimu, nyimbo, kapena zithunzi zilizonse zimene zimapangitsa munthu kuona kuti zinthu zamatsenga zilibe vuto lililonse komanso n’zosangalatsa. Zikuphatikizaponso zinthu zilizonse zimene anthu amavala pofuna kudziteteza ku zinthu zoopsa.—1 Akorinto 10:21.

15. Kodi tiyenera kuchitanso chiyani kuti tithe kulimbana ndi Satana ndiponso ziwanda?

15 Patapita zaka zingapo kuchokera pa nthawi imene anthu a ku Efeso aja anawotcha mabuku a zamatsenga, mtumwi Paulo analemba kuti ankafunikabe ‘kulimbana’ ndiponso kumenyana ndi “makamu a mizimu yoipa.” (Aefeso 6:12) Zimenezi zikusonyeza kuti, ngakhale kuti anawotcha mabuku a zamatsenga amene anali nawo, ziwanda zinkayesetsabe kuti ziwavulaze. Ndiye kodi anachitanso chiyani kuwonjezera pa kuwotcha mabukuwo? Paulo anawauza kuti: “Nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro, chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.” (Aefeso 6:16) Chikhulupiriro chingatiteteze mofanana ndi mmene chishango chimatetezera msilikali pa nthawi ya nkhondo. Tikamakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova akhoza kutiteteza, tingathe kulimbana ndi Satana komanso ziwanda zake.—Mateyu 17:20.

16. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova?

16 Kodi tingatani kuti chikhulupiriro chathu chikhale cholimba? Tiyenera kumawerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso tiyenera kudalira Mulungu kuti atiteteza. Tikamakhulupirira kwambiri Yehova, Satana ndi ziwanda zake sadzatha kutivulaza.—1 Yohane 5:5.

17. Kodi ndi chinthu chinanso chiti chimene chingatiteteze ku ziwanda?

17 Kodi Akhristu a ku Efeso ankafunika kuchitanso chiyani? Akhristuwa ankakhala mumzinda womwe munkachitika zinthu zambiri zamizimu. Choncho Paulo anawauza kuti: “Muzipemphera pa chochitika chilichonse.” (Aefeso 6:18) Ankafunika kuti nthawi zonse azipempha Yehova kuti aziwateteza. Nanga bwanji ifeyo? Nafenso tikukhala m’dziko limene anthu ake amakonda kuchita zamizimu. Choncho tiyenera kupempha Yehova kuti azititeteza, ndipo popempherapo tiyenera kugwiritsa ntchito dzina lake lenileni. (Werengani Miyambo 18:10.) Tikamapemphera kwa Yehova nthawi zonse kuti atipulumutse kwa Satana, Yehova adzayankha mapemphero athuwo.—Salimo 145:19; Mateyu 6:13.

18, 19. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kupambana pa nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziwanda? (b) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana yankho la funso liti?

18 Ngati titataya chinthu chilichonse chimene tili nacho chogwirizana ndi kukhulupirira mizimu ndiponso ngati titamadalira Yehova kuti atiteteze, tikhoza kulimbana ndi Satana ndi ziwanda zake. Sitikuyenera kuwaopa. (Werengani Yakobo 4:7, 8.) Yehova ali ndi mphamvu kwambiri kuposa ziwandazo. Iye analanga ziwandazi m’nthawi ya Nowa ndipo m’tsogolo muno aziwonongeratu. (Yuda 6) Tizikumbukira kuti sitili tokha pa nkhondoyi, Yehova akugwiritsa ntchito angelo ake kuti atiteteze. (2 Mafumu 6:15-17) Tisamakayikire kuti ndi thandizo la Yehova, tikhoza kupambana pa nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziwanda zake.—1 Petulo 5:6, 7; 2 Petulo 2:9.

19 Komano ngati Satana ndi ziwanda zake ndi amene akuchititsa mavuto padzikoli, n’chifukwa chiyani Mulungu sakuwawononga mpaka pano? Funso limeneli liyankhidwa m’mutu wotsatira.