Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 10

Kudziŵa Bwino za Angelo

Kudziŵa Bwino za Angelo

1. N’cifukwa ciani tifunika kuphunzila za angelo?

YEHOVA amafuna kuti tilidziŵe banja lake. Angelo ni banja la Mulungu. M’Baibulo, angelo amachedwa ‘ana a Mulungu.’ (Yobu 38:7) Kodi angelo amacita ciani? Kodi anathandiza bwanji anthu kumbuyoku? Ndipo angatithandize masiku ano?—Onani Zakumapeto 8.

2. Kodi angelo anakhalako bwanji? Nanga aliko angati?

2 Tifunika kudziŵa kuti angelo anakhalako bwanji. Pa lemba la Akolose 1:16, timaŵelenga kuti Yehova atalenga Yesu, “zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi.” Pa zinthu zimenezo, palinso angelo. Kodi Mulungu analenga angelo angati? Baibulo imaonetsa kuti angelo alipo mamiliyoni ambili-mbili.—Salimo 103:20; Chivumbulutso 5:11.

3. Kodi lemba la Yobu 38:4-7 limatiuza ciani za angelo?

3 Baibulo imatiphunzitsanso kuti Yehova anayamba kulenga angelo asanalenge dziko lapansi. Kodi angelo anamvela bwanji pamene anaona dziko lapansi? Baibulo imatiuza kuti iwo anakondwela kwambili. Ndipo m’pake, cifukwa anali banja logwilizana potumikila Yehova Mulungu.—Yobu 38: 4-7.

ANGELO AMATHANDIZA ANTHU A MULUNGU

4. Timadziŵa bwanji kuti angelo amafuna kudziŵa zocitika zokhudza anthu?

4 Angelo akhala ofunitsitsa nthawi zonse kudziŵa zocitika zokhudza anthu, ndi colinga ca Yehova ca dziko lapansi. (Miyambo 8:30, 31; 1 Petulo 1:11, 12) Mosakaikila, ayenela kuti anakhumudwa kwambili pamene Adamu ndi Hava anapanduka. Ngakhale masiku ano, iwo amamva cisoni kwambili kuona kuti anthu ambili samumvela Yehova. Koma ngati munthu aliyense alapa ndi kubwelela kwa Mulungu, angelo amakondwela kwambili. (Luka 15:10) Angelo amakonda kwambili anthu amene amatumikila Mulungu. Ndiye cifukwa cake Yehova amawagwilitsila nchito kuteteza atumiki ake pa dziko. (Aheberi 1:7, 14) Tiyeni tione zitsanzo zina.

“Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.” —Danieli 6:22

5. Kodi angelo anathandiza bwanji anthu a Mulungu kumbuyoku?

5 Pamene Yehova anafuna kuwononga mizinda ya Sodomu ndi Gomola, anatumiza angelo aŵili kuti akathandize Loti ndi banja lake kupulumuka ciwonongeko cimeneco. (Genesis 19:15, 16) Patapita zaka mahandiledi ambili, mneneli Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango. Koma mikango siinamudye cifukwa ‘Mulungu anatumiza mngelo wake kukagwila pakamwa pa mikango.’ (Danieli 6:22) Yehova anatumizanso mngelo wake kukamasula mtumwi Petulo m’ndende. (Machitidwe 12:6-11) Angelo anathandizanso Yesu pamene anali pa dziko lapansi. Mwacitsanzo, pamene anabatizika “angelo anam’tumikila.” (Maliko 1:13) Ndiponso, kutatsala pang’ono kuti adani ake amuphe Yesu, mngelo ‘anamulimbikitsa.’—Luka 22:43.

6. (a) Timadziŵa bwanji kuti angelo amathandiza anthu a Mulungu lelo lino? (b) Kodi tifuna kupeza mayankho pa mafunso ati?

6 Masiku ano angelo saonekela kwa anthu. Koma Mulungu akali kuwagwilitsila nchito kuthandiza anthu ake. Baibulo imati: “Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulila onse owopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.” (Salimo 34:7) Nanga n’cifukwa ninji timafunika citetezo ca angelo? Cifukwa tili ndi adani amphamvu amene amafuna kutivulaza. N’ndani amenewo? Nanga anakhalako bwanji? Ndipo amafuna kutivulaza bwanji? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tione zimene zinacitika pamene Adamu ndi Hava analengedwa.

ADANI ATHU OSAONEKA

7. Kodi Satana wakhala akupusitsa anthu kucita ciani?

7 M’Nkhani 3 tinaphunzila kuti mngelo wina anapandukila Mulungu cifukwa cofuna kukhala wolamulila. Baibulo imacha mngelo ameneyo Satana Mdyelekezi. (Chivumbulutso 12:9) Satana anali kufunanso kuti anthu ena apandukile Mulungu. Anakwanitsa kugwila m’maso Hava, ndipo akali kupitiliza kupusitsa anthu ambili-mbili kuti asakhale ku mbali ya Mulungu. Komabe, pali anthu ena monga Abele, Inoki, ndi Nowa amene anakhalabe okhulupilika kwa Yehova.—Aheberi 11:4, 5, 7.

8. (a) Kodi angelo ena anakhala bwanji ziŵanda? (b) Nanga ziŵanda zimenezo zinapulumuka bwanji Cigumula?

8 M’nthawi ya Nowa, angelo ena anapandukila Mulungu. Anasiya malo awo kumwamba kudzakhala monga anthu pa dziko lapansi. Cifukwa ciani? Baibulo imatiuza kuti anafuna kudzakwatila akazi. (Ŵelengani Genesis 6:2.) Koma kunali kulakwa angelo kucita zimenezo. (Yuda 6) Cifukwa ca angelo oipa amenewo, anthu ambili panthawiyo anakhala acinyengo ndi aciwawa kwambili. Yehova poona zimenezi, sanacitile mwina koma kuwononga anthu onse oipa ndi cigumula ca madzi. Koma anapulumutsa atumiki ake okhulupilika. (Genesis 7:17, 23) Angelo oipa aja poona Cigumula ca madzi, anathaŵa kubwelela kumwamba. Baibulo imacha angelo oipa amenewo kuti ziŵanda. Iwo anasankha kukhala ku mbali ya Satana, conco Mdyelekezi anakhala wolamulila wawo.—Mateyu 9:34.

9. (a) Cinacitika n’ciani pamene ziŵanda zinabwelela kumwamba? (b) Nanga lomba tidzaphunzila ciani?

9 Popeza kuti angelo aja anapanduka ndi kukhala ziŵanda, Yehova sanawalole kuti abwelele m’banja lake. (2 Petulo 2:4) Ndipo mpaka lelo, Mulungu sanalole kuti ziŵanda zimenezo zisandukenso kukhala anthu. Koma zikali ‘kusoceletsa dziko lonse lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9; 1 Yohane 5:19) Lomba tiyeni tione mmene ziŵanda zimasoceletsela anthu ambili, kapena mmene zimawapusitsila.—Ŵelengani 2 Akorinto 2:11.

MMENE ZIŴANDA ZIMAPUSITSILA ANTHU

10. Kodi ziŵanda zimapusitsa bwanji anthu?

10 Ziŵanda zimapusitsa anthu m’njila zambili. Anthu ambili amakambitsana ndi ziŵanda mwacindunji kapena kupitila mwa munthu wina, monga sing’anga kapena wamizimu. Kucita zimenezi ndiye kugwilizana ndi ziŵanda, kapena kukhulupilila zamizimu. Koma Baibulo imacenjeza kuti tikhaliletu kutali ndi ciliconse cokhudzana ndi ziŵanda. (Agalatiya 5:19-21) Cifukwa ninji? Monga mmene wosaka nyama amateyela msampha kuti agwile nyama, ziŵanda zimagwilitsila nchito macenjela kuti zigwile anthu ndi kuwalamulila.—Onani Zakumapeto 26.

11. Kodi kuombeza n’ciani? Nanga n’cifukwa ninji tifunika kukupewa?

11 Kuwombeza ni amodzi mwa macenjela a ziŵanda. Kodi kuwombeza n’ciani? Ni njila yoseŵenzetsa mphamvu zamatsenga pofuna kudziŵa zinthu zosadziŵika kapena za kutsogolo. Amacita zimenezi mwa kuyang’ana nyenyezi, kucita maula, kuchova njuga zamatsenga, kuyang’ana pa galasi yamatsenga, kapena kuyang’ana mizela ya kumanja. Anthu ambili amaona kuti kucita zimenezi kulibe vuto. Koma kumeneko n’kudzinamiza, ndipo n’koopsa kwambili. Mwacitsanzo, Baibulo imaonetsa kuti ziŵanda zimaseŵenzela pamodzi ndi anthu olosela za mtsogolo. Pa Machitidwe 16:16-18, timaŵelenga za mtsikana wina amene “ciŵanda colosela zam’tsogolo” cinali kum’thandiza kulosela. Koma pamene mtumwi Paulo anacotsa ciŵanda cimeneco, mtsikana uja sanakwanitsenso kulosela.

12. (a) N’cifukwa ciani kuyesa kukamba ndi anthu amene anafa kale n’kovulaza? (b) N’cifukwa ciani atumiki a Mulungu amapewa miyambo yokhudzana ndi zamizimu?

12 Palinso njila ina imene ziŵanda zimaseŵenzetsa pofuna kupusitsa anthu. Zimafuna tizikhulupilila kuti akufa ali moyo kwina kwake, ndi kuti tingakambitsane nawo, ndi kutinso akhoza kutivulaza. Mwacitsanzo, munthu amene mnzake kapena m’bululu wake anamwalila, angayende kwa sing’anga, kapena kwa wowombeza. Wowombeza angauze munthuyo zinthu zoona zokhudza munthu amene anamwalila, ndipo ngakhale kutengela mau ake. (1 Samueli 28:3-19) Ngakhale miyambo yambili ya malilo, imacitika cifukwa cokhulupilila kuti akufa ali moyo kwina kwake. Miyambo ina imeneyo ni maphwando a malilo, mwambo wokumbukila malemu, kupeleka nsembe kwa azimu, mwambo woloŵa cokolo, ndi miyambo ina yocezela usiku wonse. Akhiristu akakana kucitako miyambo imeneyi, acibanja, kapena anthu a m’mudzi mwawo amawazunza, kuwanyoza, ngakhale kuwapatula. Koma Akhiristu amadziŵa kuti akufa sali ndi moyo kulikonse. Ndiye cifukwa cake n’zosatheka kukamba nawo, ndipo sangativulaze. (Salimo 115:17) Conco, khalani wosamala kwambili. Osayesa kukamba ndi akufa, kapena kucitako miyambo ya zamizimu. Ni ziŵanda zimenezo.—Ŵelengani Deuteronomo 18:10, 11; Yesaya 8:19.

13. Kodi anthu ena ambili amene poyamba anali kuopa ziŵanda acita ciani?

13 Ziŵanda sizimapusitsa cabe anthu, komanso zimawaopseza. Lelo lino, Satana ndi ziŵanda zake amadziŵa kuti angotsala ndi “kanthawi kocepa” kuti Mulungu awacotseletu pa dziko lapansi. Ndiye cifukwa cake ni okwiya ngako, ndipo amacititsa zoipa ndi zaciwawa zambili kuposa kale lonse. (Chivumbulutso 12:12, 17) Ngakhale ni conco, pali anthu ambili amene lomba saopanso ziŵanda. Kodi iwo analeka bwanji kuopa ziŵanda?

KANIZANI ZIŴANDA KUTI MUMASUKE

14. Potengela citsanzo ca Akhiristu oyambilila, kodi tiyenela kucitanji kuti timasuke ku ziŵanda?

14 Baibulo imatiuza mmene tingakanizile ziŵanda ndi kumasuka. Mwacitsanzo, anthu ena mu mzinda wa Efeso anali kugwilizana ndi ziŵanda akalibe kuphunzila coonadi. Nanga anamasuka bwanji? Baibulo imati: “Ambili ndithu amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.” (Machitidwe 19:19) Pofuna kukhala Akhiristu, anawononga mabuku awo onse a zamatsenga. N’zimene nafenso tiyenela kucita lelo lino. Aliyense amene afuna kutumikila Yehova, afunika kuwononga zinthu zilizonse zokhudzana ndi zamizimu zimene ali nazo. Zimenezi ziphatikizapo mabuku, magazini, zopendela nyenyezi, mafilimu, nyimbo, ndi maseŵelo a pakompyuta. Zimaphatikizaponso zithunzi-thunzi zoonetsa zinthu monga zamatsenga, ziŵanda, ndi zocitika zina zodabwitsa. Zonsezi amazionetsa kukhala zosangulutsa zimene zilibe vuto lililonse. Zimaphatikizaponso kuvala zithumwa kapena ulungu pofuna kudziteteza.—1 Akorinto 10:21.

15. Tifunikilanso kucita ciani cina kuti tikanize Satana ndi ziŵanda zake?

15 Patapita zaka zambili kucokela pamene anthu a ku Efeso anawononga mabuku awo a zamatsenga, mtumwi Paulo anawalembela kalata. Anawauza kuti anafunika kupitiliza ‘kulimbana’ ndi “makamu a mizimu yoipa.” (Aefeso 6:12) Inde, ngakhale kuti iwo anali anawononga kale-kale mabuku awo a zamizimu, ziŵanda zinali kuyesabe kuwavutitsa. Nanga n’cianinso cimene anafunikila kucita? Paulo anawauza kuti: “Nyamulani cishango cacikulu ca cikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.” (Aefeso 6:16) Zoona, monga mmene cishango cimatetezela msilikali pa nkhondo, cikhulupililo cikhoza kutiteteza. Ngati tili ndi cidalilo conse cakuti Yehova angatiteteze, tidzakwanitsa kumukaniza Satana ndi ziŵanda zake.—Mateyu 17:20.

16. Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu mwa Yehova?

16 Kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu mwa Yehova? Tiyenela kuŵelenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ndi kudalila Yehova kuti adzatiteteza. Tikaika cidalilo cathu conse mwa Yehova, Satana ndi ziŵanda zake sadzakwanitsa kutivulaza.—1 Yohane 5:5.

17. Nanga cinanso cofunika n’ciani kuti Yehova atiteteze ku ziŵanda?

17 Kodi panalinso cina cimene Akhiristu a ku Efeso anafunika kucita? Inde cinalipo. Mu mzinda wawo zamizimu zinali zofala kwambili. Conco Paulo anawauza kuti: “Muzipemphela pa cocitika ciliconse.” (Aefeso 6:18) Anafunikila kumapempha citetezo ca Yehova nthawi zonse. Nanga bwanji ife? Ngakhale masiku ano, zamizimu n’zofala kwambili m’dziko. Ndiye cifukwa cake ngakhale ife tifunika kumapempha citetezo ca Yehova. Ndipo osaiŵala kuchula dzina lake popemphela. (Ŵelengani Miyambo 18:10.) Ngati tipitiliza kumapempha Yehova kuti atilanditse kwa Satana, adzayankha mapemphelo athu.—Salimo 145:19; Mateyu 6:13.

18, 19. (a) N’ciani cingatithandize kupambana nkhondo yolimbana ndi Satana ndi ziŵanda? (b) Kodi ni funso lanji limene lidzayankhidwa m’nkhani yotsatila?

18 Ngati ticotsa mu umoyo wathu ciliconse cokhudzana ndi zamizimu, ndipo tidalila citetezo ca Yehova, tidzakwanitsa kum’kaniza Satana ndi ziŵanda zake. Osaziopa ziŵanda. (Ŵelengani Yakobo 4:7, 8.) Yehova ni wamphamvu kwambili kupambana ziŵanda. Anazipatsa cilango m’nthawi ya Nowa, ndipo kutsogolo uku adzaziwonongelatu. (Yuda 6) Kumbukilani kuti sitili tokha pa nkhondo imeneyi. Yehova amatiteteza ndi angelo ake. (2 Mafumu 6:15-17) Tili ndi cidalilo conse kuti mwa cithandizo ca Yehova, tidzapambana nkhondo imeneyi, yolimbana ndi Satana ndi ziŵanda zake.—1 Petulo 5:6, 7; 2 Petulo 2:9.

19 Koma tikaona mavuto ambili amene Satana ndi ziŵanda zake acititsa, n’cifukwa ninji Mulungu sawaononga kufikila lelo? Nkhani yotsatila idzatipatsa yankho pa funso limeneli.