Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 13

Muzilemekeza Mphatso ya Moyo

Muzilemekeza Mphatso ya Moyo

1. Kodi n’ndani anatipatsa moyo?

YEHOVA ‘ni Mulungu wamoyo.’ (Yeremiya 10:10) Iye ni Mlengi wathu, ndipo anatipatsa moyo. Baibulo imakamba kuti: “Munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.” (Chivumbulutso 4:11) Inde, Yehova anafuna kuti tikhale ndi moyo. Ndipo moyo ni mphatso ya mtengo wapatali.—Ŵelengani Salimo 36:9.

2. Cofunika n’ciani kuti zinthu zitiyendele bwino mu umoyo?

2 Yehova amatipatsa zonse zimene tifunikila kuti tikhale ndi moyo, monga cakudya ndi madzi. (Machitidwe 17:28) Iye safuna kuti tingokhala ndi moyo cabe iyayi, komanso kuti tizikondwela nawo. (Machitidwe 14:15-17) Koma kuti zinthu zitiyendele bwino mu umoyo, tifunika kumvela malamulo a Mulungu.—Yesaya 48:17, 18.

MMENE MULUNGU AMAONELA MOYO

3. Kodi Yehova anacita ciani pamene Kaini anapha Abele?

3 Baibulo imatiphunzitsa kuti kwa Yehova, moyo wathu ndi wa anthu ena ni cinthu ca mtengo wapatali. Mwacitsanzo, pamene Kaini, mwana wa Adamu ndi Hava, anapsela mtima mng’ono wake, Abele, Yehova anam’cenjeza kuti aletse mkwiyo wake. Koma Kaini sanamvele. M’malo mwake, anakalipa kwambili cakuti ‘anakantha Abele, m’bale wake n’kumupha.’ (Genesis 4:3-8) Yehova anamulanga Kaini cifukwa ca kupha Abele. (Genesis 4:9-11) Kodi mwaona kuti mkwiyo ndi cidani ni makhalidwe oopsa? Inde, angapangitse munthu kukhala wankhaza ndi waciwawa. Munthu waconco sangalandile moyo wamuyaya. (Ŵelengani 1 Yohane 3:15.) Koma kuti tikondweletse Yehova, tifunika kukonda anthu onse.—1 Yohane 3:11, 12.

4. Kodi lamulo limene Mulungu anapatsa Aisiraeli pa nkhani ya kupha munthu litiphunzitsa ciani za moyo?

4 Ngakhale pambuyo pa zaka masauzande, Yehova anaonetsa kuti anali kuonabe moyo kukhala wa mtengo wapatali. Anaonetsa zimenezi popeleka malamulo khumi (10) kwa Mose. Limodzi la malamulo amenewo limati: “Usaphe munthu.” (Deuteronomo 5:17) Ngati munthu wapha munthu mnzake mwadala, nayenso anali kuphedwa.

5. Kodi nkhani yocotsa mimba Mulungu amaiona bwanji?

5 Nanga nkhani yocotsa mimba, Mulungu amaiona bwanji? Kwa Yehova, ngakhale moyo wa mwana amene akali m’mimba ni wa mtengo wapatali. M’Cilamulo cimene Yehova anapatsa Aisiraeli, iye analamula kuti, ngati munthu avulaza mzimayi wapakati, ndipo mwana uja n’kufa m’mimba, munthu ameneyo anafunika kuphedwa. (Ŵelengani Ekisodo 21:22, 23; Salimo 127:3.) Ici citiphunzitsa kuti kucotsa mimba n’kulakwa.—Onani Zakumapeto 28.

6, 7. Tingacite ciani pofuna kuonetsa Yehova kuti timaona moyo kukhala wa mtengo wapatali?

6 Nanga ife tingamuonetse bwanji Yehova kuti timaona moyo wathu, ndi wa anthu ena, kukhala wa mtengo wapatali? Mwa kupewa kucita ciliconse cimene cingaike pa ciwopsezo moyo wathu ndi wa anthu ena. Mwa ici, tiyenela kupewa zinthu monga fodya, camba, ndi mankhwala osokoneza ubongo. Zinthu zimenezi zimawononga thupi ndipo zimapha.

7 Mulungu anatipatsa moyo ndi thupi lathu, conco tiyenela kuzisamalila bwino mmene iye amafunila. Ngati siticita zimenezi, Mulungu adzationa kukhala onyansa. (Aroma 6:19; 12:1; 2 Akorinto 7:1) Yehova amene anatipatsa moyo, sangalandile kulambila kwathu ngati sitiona moyo kukhala wa mtengo wapatali. N’zoona kuti kuleka zizoloŵezi zoipa kungakhale kovuta kwambili. Koma Yehova adzatithandiza ngati tilimbikila kucita zinthu zoonetsa kuti moyo ni wa mtengo wapatali.

8. Tiyenela kucita ciani kuti tisaike pa ciwopsezo moyo wathu ndi wa anthu ena?

8 Taphunzila kuti moyo ni mphatso ya mtengo wapatali. Yehova amatidalila kuti tidzapewa ciliconse cimene cingaike pa ciwopsezo moyo wathu kapena wa anthu ena. Mwa ici, tifunika kusamala poyendetsa motoka, honda, kapena coyendela ciliconse. Tiyenelanso kupewa maseŵela oopsa ndi aciwawa. (Salimo 11:5) Ndiponso, pa nyumba pathu pasakhale ciliconse cimene cingabweletse ngozi. Yehova analamula Aisiraeli kuti: “Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopela kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kucokela padengapo.”—Deuteronomo 22:8.

9. Nanga nyama tiyenela kucita nazo bwanji?

9 Yehova safuna kuti tizicitila nkhanza ngakhale nyama. Inde amatilola kupha nyama kuti tipezeko cakudya ndi zovala. Ndiponso amalola kupha nyama ngati iwopseza moyo wathu. (Genesis 3:21; 9:3; Ekisodo 21:28) Koma ni nkhanza kupha nyama popanda cifukwa ceni-ceni, kapena mwa kucita maseŵela opikisana.—Miyambo 12:10.

MUZIONA MOYO KUKHALA CINTHU COPATULIKA

10. Tidziŵa bwanji kuti magazi amaimila moyo?

10 Magazi ni opatulika kwa Yehova cifukwa amaimila moyo. Kaini atapha Abele, Yehova anamuuza kuti: “Magazi a m’bale wako akundililila munthaka.” (Genesis 4:10) Magazi a Abele anaimila moyo wake, ndipo Yehova analanga Kaini cifukwa ca kupha Abele. Pambuyo pa Cigumula ca m’nthawi ya Nowa, Yehova anapitiliza kuonetsa kuti magazi amaimila moyo. Inde, Yehova anauza Nowa ndi banja lake kuti azidya nyama. Iye anati: “Nyama yamoyo iliyonse ikhale cakudya canu. Komanso ndikukupatsani zamasamba zonse kuti zikhale cakudya canu.” Koma panali cinthu cimodzi cimene Mulungu anawaletsa kudya. Mulungu anawalamula kuti: “Koma musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.”—Genesis 1:29; 9:3, 4.

11. Kodi Mulungu anapatsa Aisiraeli lamulo lanji pa nkhani ya magazi?

11 Patapita zaka ngati 800 kucokela pamene Yehova anauza Nowa kuti asadye magazi, Iye analamulanso anthu ake kuti: “Munthu aliyense mwa ana a Isiraeli kapena mlendo amene akukhala pakati panu akapita kosaka nyama, ndipo wapha nyama kapena mbalame yololeka kudya, azithila magazi ake pansi ndi kuwafotsela ndi dothi.” Ndiyeno anati: “Musamadye magazi.” (Levitiko 17:13, 14) Yehova anali kufunabe kuti anthu ake aziona magazi kukhala opatulika. Anawauza kudya nyama, koma osati magazi. Akapha nyama yakudya, anafunika kuthila magazi ake pansi ndi kuwafocela.

12. Kodi Akhiristu amawaona bwanji magazi?

12 Patapita zaka ndithu kucokela pamene Yesu anafa, atumwi ndi akulu mu mpingo wa Cikhiristu ku Yerusalemu anacita msonkhano. Anafuna kuona kuti ni mbali ziti za Cilamulo ca Aisiraeli zimene zinali zofunikabe kwa Akhiristu. (Ŵelengani Machitidwe 15:28, 29; 21:25.) Yehova anawathandiza kuzindikila kuti ngakhale pa nthawi imeneyo, magazi anali cinthu ca mtengo wapatali ndi copatulika. Mwa ici, Akhiristu oyambilila sanali kudya kapena kumwa magazi. Ngakhale nyama yosakhetsa magazi sanali kudya. Kuphwanya lamulo limeneli kunali kofanana ndi chimo la kulambila mafano kapena kucita ciwelewele. Kucokela nthawi imeneyo, Akhiristu oona amakana kudya kapena kumwa magazi. Nanga bwanji masiku ano? Yehova sanasinthe. Afuna tiziona magazi kuti ni opatulika.

13. N’cifukwa ciani Akhiristu amakana kuwaika magazi?

13 Kodi izi zitanthauza kuti Akhiristu ayenela kukana ngakhale kuwaika magazi? Inde, ndiye tanthauzo lake. Ngakhale ife, Yehova amatilamula kuti tisadye kapena kumwa magazi. Tifunse conco. Ngati dokota akuuzani kuti muleke kumwa moŵa, kodi atanthauza kuti palibe vuto ngati muika moŵa m’nyeleti n’kudzilasa? Kutali-tali! N’cimodzi-modzi ndi lamulo la magazi. Sitiyenela kulandila magazi ngakhale kupitila m’nyeleti.—Onani Zakumapeto 29.

14, 15. N’cifukwa ninji Mkhiristu ayenela kulemekeza moyo ndi kumvela Yehova?

14 Nanga bwanji ngati dokota atiuza kuti tidzafa ngati sadzatiika magazi? Zikafika apa lomba ni nkhani ya chikhulupililo. Munthu aliyense afunika kusankha, kumvela kapena kuphwanya lamulo la Mulungu loletsa magazi. Sikuti ife Akhiristu sitifuna moyo iyai. Timayamikila ndi kulemekeza ngako mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa. Ndipo timayesa-yesa kupempha kapena kupeza mitundu ina ya mankhwala m’malo mwa magazi. Timacita zonsezi cifukwa moyo timaufuna.

15 Timayesa kucita khama kuti tikhale ndi thanzi labwino. Koma cifukwa magazi amaimila moyo, ndipo moyo ni wopatulika kwa Mulungu, sitilola kuikidwa magazi. Kwa ife, kumvela Yehova ni cinthu cofunika kwambili, kupambana kutalimphitsako moyo mwa kuphwanya lamulo la Mulungu. Yesu anakamba kuti: “Aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine adzaupeza.” (Mateyu 16:25) Timafuna kumvela Yehova cifukwa timam’konda. Iye ndiye amadziŵa zimene zili zabwino kwambili kwa ife. Ndipo nafenso timaona moyo mmene Yehova amauonela, kuti ni wa mtengo wapatali ndi wopatulika.—Aheberi 11:6.

16. N’cifukwa ciani atumiki a Mulungu amamvela iye?

16 Olo zivute bwanji, Akhiristu okhulupilika amamvelabe lamulo la Mulungu pa nkhani ya magazi. Iwo salola kudya kapena kumwa magazi. Ngakhale pamene adwala, savomela kuwaika magazi kuti acile. * Koma cifukwa amafuna kuti apulumutse moyo wawo, amavomela mitundu ina ya mankhwala osafuna magazi. Iwo amadziŵa kuti Mulungu amene anapanga moyo ndi magazi ndiye adziŵa bwino. Kodi inu simukhulupilila zimenezi?

YEHOVA ANALOLA NJILA IMODZI CABE YOSEŴENZETSA MAGAZI

17. Pa nthawi ya Aisiraeli, kodi njila imodzi cabe imene Yehova analola kuseŵenzetsa magazi inali iti?

17 M’Cilamulo cimene Mulungu anapatsila Mose, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Moyo wa nyama uli m’magazi ndipo ine ndakuikilani magazi paguwa lansembe kuti azikuphimbilani macimo. Zili conco popeza magazi ndiwo amaphimba macimo.” (Levitiko 17:11) Aisiraeli akacimwa, anali ndi mwayi wopempha cikhululukilo kwa Yehova. Kuti acite zimenezi, anali kupeleka nsembe ya nyama, ndi kupempha wansembe kuti athile magazi ena a nyama imeneyo pa guwa la nsembe pakacisi. Ndiyo inali njila imodzi cabe imene Yehova analola Aisiraeli kuseŵenzetsa magazi.

18. Kodi nsembe ya Yesu inatipatsa mwayi wanji?

18 Pamene Yesu anabwela pa dziko lapansi, anapeleka moyo wake, kapena kuti magazi ake, monga nsembe ya macimo athu. Mwa ici, iye anathetsa lamulo lopeleka nsembe za nyama. (Mateyu 20:28; Aheberi 10:1) Moyo umene Yesu anapeleka unali wa mtengo wapatali kwambili. Cifukwa ca ici, pamene Yehova anaukitsa Yesu kuyenda kumwamba, Yehova anapatsa anthu onse mwayi wokakhala ndi moyo wosatha.—Yohane 3:16; Aheberi 9:11, 12; 1 Petulo 1:18, 19.

Mmene mungaonetsele kuti mumalemekeza moyo ndi magazi

19. Tiyenela kucitanji kuti tikhale ‘oyela pa mlandu wa magazi a anthu onse’?

19 Kukamba zoona, tiyenela kuyamikila kwambili Yehova cifukwa ca mphatso ya mtengo wapatali, ya moyo umene tili nawo. Ndipo tifunika kuuzako anthu ena kuti ngati akhulupilila mwa Yesu, adzapeza moyo wosatha. Ife timakonda anthu anzathu. Conco, tiyenela kucita khama kuwaphunzitsa za mmene angapezele moyo weni-weni. (Ezekieli 3:17-21) Tikacita zimenezi, tidzakamba mmene mtumwi Paulo anakambila kuti: “Ndine woyela pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisileni kanthu, koma ndinakuuzani cifunilo conse ca Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27) Inde, ife timalemekeza kwambili moyo ndi magazi. Timacita zimenezi mwa kuuzako ena za Yehova, ndi mmene iye amaonela moyo.

^ ndime 16 Kuti mudziŵe zambili pa nkhani yoikidwa magazi, onani tsamba 77 mpaka 79 m’buku yakuti “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu,” yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.