Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 14

Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe

Mmene Banja Lanu Lingakhalile Lacimwemwe

1, 2. Kodi Yehova amafuna kuti anthu azikhala bwanji m’banja?

YEHOVA MULUNGU ndiye anamangitsa cikwati coyamba. Baibulo imatiuza kuti Mulungu atalenga mkazi woyamba, ‘anamubweletsa kwa mwamuna.’ Mwamunayo, Adamu, anakondwela ngako, mpaka kukamba kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Genesis 2:22, 23) Izi zitionetsa kuti Yehova amafuna kuti anthu azikhala okondwela m’cikwati.

2 N’comvetsa cisoni kuti pali mabanja ambili amene sanakhalepo ndi cimwemwe ceni-ceni. Koma nkhani yabwino ni yakuti, m’Baibulo muli mfundo zabwino zimene zingathandize aliyense m’banja kucita mbali yake, kuti banja lonse lizikhala logwilizana ndi lokondana.—Luka 11:28.

MALANGIZO A MULUNGU KWA AMUNA

3, 4. (a) Kodi mwamuna ayenela kukhala naye bwanji mkazi wake? (b) N’cifukwa ninji kuli kofunika kuti mwamuna ndi mkazi wake azikhululukilana?

3 Baibulo imakamba kuti mwamuna wabwino ayenela kukonda mkazi wake ndi kumulemekeza. (Ŵelengani Aefeso 5:25-29.) Nthawi zonse, mwamuna ayenela kukhala naye mwacikondi mkazi wake. Afunika kum’cinjiliza, kum’samalila, ndipo asam’citile nkhanza m’njila iliyonse.

4 Nanga mkazi akalakwa, kodi mwamuna ayenela kucita ciani? Baibulo imauza amuna kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsele mtima.” (Akolose 3:19) Inu amuna, musaiŵale kuti ngakhale inu mumalakwa. Conco, ngati mufuna kuti Mulungu azikukhululukilani, inunso muyenela kumakhululukila akazi anu. (Mateyu 6:12, 14, 15) Ngati mwamuna ndi mkazi amakonda kukhululukilana, banja lawo lidzakhala lacimwemwe.

5. N’cifukwa ninji mwamuna ayenela kulemekeza mkazi wake?

5 Yehova amafuna kuti mwamuna azilemekeza mkazi wake. Conco, mwamuna ayenela kuganizila bwino zimene mkazi wake amafunikila. Iyi ni nkhani ikulu kwambili. Ngati mwamuna sasamalila bwino mkazi wake, Yehova angaleke kumvela mapemphelo ake. (1 Petulo 3:7) Kukonda Mulungu n’kumene Yehova amayang’ana mwa anthu. Sikuti Iye amakonda amuna kuposa akazi iyai.

6. Kodi mau akuti mwamuna ndi mkazi ni “thupi limodzi,” amatanthauza ciani?

6 Yesu anafotokoza kuti mwamuna ndi mkazi wake “salinso aŵili, koma thupi limodzi.” (Mateyu 19:6) Afunika kukhala okhulupilika kwa wina ndi mnzake nthawi zonse. (Miyambo 5:15-21; Aheberi 13:4) Mwamuna ndi mkazi afunika kupatsana mangawa a m’cikwati mwaufulu. (1 Akorinto 7:3-5) Ndiponso, mwamuna azikumbukila kuti “palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” Conco, ayenela kukonda mkazi wake ndi kumusamalila bwino. Cikulu cimene mkazi amafuna kwa mwamuna wake, n’cakuti azimusamalila ndi kum’konda.—Aefeso 5:29.

MALANGIZO A MULUNGU KWA AKAZI

7. N’cifukwa ninji banja limafunika mutu?

7 Banja lililonse limafunika mutu, kutanthauza munthu wotsogolela kuti zinthu ziziyenda bwino. Pa 1 Akorinto 11:3, Baibulo imati: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khiristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khiristu ndiye Mulungu.”

8. Kodi mkazi angaonetse bwanji kuti amalemekeza kwambili mwamuna wake?

8 Mwamuna aliyense amalakwa. Koma ngati mkazi amacilikiza zosankha za mwamuna wake ndi mtima wonse, banja limayenda bwino. (1 Petulo 3:1-6) Baibulo imati: “Mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Nanga bwanji ngati mwamuna ni wa cipembedzo cina? Mkazi afunikabe kumulemekeza mwamunayo. Baibulo imati: “Inu akazi, muzigonjela amuna anu kuti ngati ali osamvela mau akopeke, osati ndi mau, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyela ndi ulemu wanu waukulu.” (1 Petulo 3:1, 2) Khalidwe labwino la mkazi lingathandize mwamuna kuyamba kumvetsetsa ndi kulemekeza cipembedzo ca mkazi wake.

9. (a) Kodi mkazi ayenela kucita bwanji ngati sagwilizana ndi maganizo a mwamuna wake? (b) Kodi pa Tito 2:4, 5, pali malangizo anji kwa akazi okwatiwa?

9 Kodi mkazi ayenela kucita bwanji ngati sagwilizana ndi maganizo a mwamuna wake? Ayenela kukamba maganizo ake m’njila yaulemu. Mwacitsanzo, Sara anakamba zimene anali kufuna, zimene Abulahamu sanakondwele nazo. Koma Yehova anauza Abulahamu kuti: “Mvela mau ake.” (Genesis 21:9-12) Nthawi zambili, mwamuna wa Cikhiristu amapanga zosankha zogwilizana ndi Baibulo. Conco, ni bwino kuti mkazi azicilikiza zosankha za mwamuna wake. (Machitidwe 5:29; Aefeso 5:24) Mkazi wabwino amasamalila banja lake. (Ŵelengani Tito 2:4, 5.) Mwamuna wake ndi ana ake akaona khama lake powasamalila, amam’konda ndi kum’lemekeza kwambili.—Miyambo 31:10, 28.

N’cifukwa ciani Sara ali citsanzo cabwino kwa akazi?

10. Kodi Baibulo imati ciani za kupatukana ndi cisudzulo?

10 Nthawi zina, mwamuna ndi mkazi amafulumila kugamula kuti angopatukana, kapena kusudzulana. Komabe, Baibulo imati: ‘Mkazi asasiye mwamuna wake, mwamunanso asasiye mkazi wake.’ (1 Akorinto 7:10, 11) Inde, alipo mavuto ena akulu amene angapangitse mwamuna ndi mkazi kupatukana. Koma nkhaniyi ni ikulu, sifunika kuitenga mopepuka. Nanga bwanji za kusudzulana? Baibulo imalola cisudzulo pa cifukwa cimodzi cabe, cigololo.—Mateyu 19:9.

MALANGIZO A MULUNGU KWA MAKOLO

Yesu ni citsanzo cabwino kwa aliyense m’banja

11. N’ciani maka-maka cimene ana amafuna?

11 Inu makolo, muzipatula nthawi yokwanila yoceza ndi ana anu. Ana anu amafuna inu, ndipo cimene amafuna kwambili n’cakuti muziwaphunzitsa za Yehova.—Deuteronomo 6:4-9.

12. Kodi makolo ayenela kucita ciani kuti acinjilize ana awo?

12 Dziko la Satana likungoipila-ipila. Ndipo pali anthu ena amene angafune kuvulaza ana anu, kapena kugona nawo mwacikakamizo. Kwa makolo ena, cimakhala covuta kuti akambilane nkhani imeneyi ndi ana awo. Lomba zikakhala conco, kodi makolo adzawacenjeza bwanji za anthu oipa amenewo. Nanga adzawakonzekeletsa bwanji za mmene angawapewele? Conde makolo, kambilanani ndi ana anu kuti muwacinjilize. *1 Petulo 5:8.

13. Kodi makolo ayenela kuphunzitsa bwanji ana awo?

13 Makolo alinso ndi udindo wophunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Kodi cofunika n’ciani kuti ana anu muwaphunzitse? Ana amafunikila malangizo ndi uphungu. Ndipo akalakwitsa zinthu, muwawongolele moyenelela, osati mwaukali kapena mwankhanza. (Yeremiya 30:11) Conco, pamene mukali wokwiya, si nthawi yolanga ana, kuopela kuti mungauze ana anu mau “olasa ngati lupanga,” kuwavulaza mu mtima. (Miyambo 12:18) Athandizeni ana anu kumvetsetsa zifukwa zimene ayenela kukhalila omvela.—Aefeso 6:4; Aheberi 12:9-11; onani Zakumapeto 30.

MALANGIZO A MULUNGU KWA ANA

14, 15. N’cifukwa ciani ana ayenela kumvela makolo?

14 Yesu nthawi zonse anali kumvela Atate wake, ngakhale pa nthawi yovuta. (Luka 22:42; Yohane 8:28, 29) Yehova amafuna kuti ana nawo azimvela makolo.—Aefeso 6:1-3.

15 Inu ana, tidziŵa kuti nthawi zina mungaone kuti n’covuta kumvela makolo anu. Koma dziŵani kuti mukakhala ana omvela, Yehova ndi makolo anu adzakukondani kwambili. *Miyambo 1:8; 6:20; 23:22-25.

N’ciani cingathandize acicepele kukhala okhulupilika kwa Mulungu pamene ayesedwa kucita zoipa?

16. (a) Kodi Satana amacita ciani pofuna kunyengelela acicepele kucita zoipa? (b) N’cifukwa ciani n’cinthu canzelu kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova?

16 Mdyelekezi angaseŵenzetse acicepele anzanu pokunyengelelani kuti mucite zinthu zoipa. Iye amadziŵa kuti cikoka ca mabwenzi n’camphamvu kwambili. Mwacitsanzo, Dina, mwana wa Yakobo, anali ndi anzake amene sanali kukonda Yehova. Izi zinabweletsa mavuto akulu kwa iye ndi onse m’banja. (Genesis 34:1, 2) Ngati anzanu sakonda Yehova, angakunyengeleleni kucita zinthu zimene Yehova amazonda. Ndipo zimenezi zingabweletse mavuto pa inu, a m’banja mwanu, ndi kukwiitsa Mulungu. (Miyambo 17:21, 25) Cifukwa ca zimenezi, mufunika kupeza mabwenzi amene amakonda Yehova.—1 Akorinto 15:33.

N’ZOTHEKA NDITHU BANJA LANU KUKHALA LACIMWEMWE

17. Kodi aliyense m’banja afunika kucita mbali yanji?

17 Ngati onse m’banja amatsatila malangizo a Mulungu, amapewa mavuto ambili. Conco ngati ndinu mwamuna, muzikonda mkazi wanu ndi kum’samalila bwino. Ngati ndinu mkazi, muzilemekeza mwamuna wanu ndi kumugonjela. Tengelani citsanzo ca mkazi wochulidwa pa Miyambo 31:10-31. Ngati ndinu kholo, phunzitsani ana anu kukonda Mulungu. (Miyambo 22:6) Ngati ndinu tate, muzitsogolela “bwino” banja lanu. (1 Timoteyo 3:4, 5; 5:8) Ndipo inu ana, muzimvela makolo anu. (Akolose 3:20) Muzikumbukila kuti aliyense m’banja amalakwa. Conco, aliyense akalakwa azikhala wodzicepetsa ndi kupepesa. Ndipo nonse muzikhululukilana. Inde, m’Baibulo muli malangizo a Yehova kwa aliyense m’banja.

^ ndime 12 Kuti mudziŵe zambili pa nkhani imeneyi, onani mutu 32 m’buku yakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, yolembedwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 15 Koma mwana safunika kumvela makolo ngati amuuza kucita cinthu cophwanya malamulo a Mulungu.—Machitidwe 5:29.