Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 14

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala

Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala

1, 2. Kodi Yehova amafuna kuti mabanja akhale otani?

YEHOVA MULUNGU ndi amene anayambitsa ukwati. Baibulo limatiuza kuti Mulungu atalenga mkazi woyamba, ‘anamubweretsa kwa Adamu.’ Iye ataona mkaziyo anasangalala kwambiri n’kunena kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Genesis 2:22, 23) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amafuna kuti mabanja azisangalala.

2 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sasangalala m’banja. Komatu m’Baibulo muli mfundo zambirimbiri zopita kwa onse m’banja ndipo aliyense akamatsatira mfundozi, zingathandize kuti banja lawo liziyenda bwino komanso kuti onse azikhala mosangalala.—Luka 11:28.

ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI AMUNA OKWATIRA AZICHITA

3, 4. (a) Kodi mwamuna ayenera kuchita bwanji zinthu ndi mkazi wake? (b) N’chifukwa chiyani mwamuna ndi mkazi ayenera kumakhululukirana?

3 Baibulo limanena kuti mwamuna wabwino ayenera kukonda komanso kulemekeza mkazi wake. (Werengani Aefeso 5:25-29.) Nthawi zonse mwamuna afunika kumachita zinthu mwachikondi ndi mkazi wake. Ayeneranso kumutetezera, kumusamalira ndiponso kusachita chilichonse chimene chingamuvulaze.

4 Koma kodi mwamuna ayenera kuchita chiyani ngati mkazi wake walakwitsa zinthu zina? Amuna akuuzidwa kuti: “Musaleke kukonda akazi anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.” (Akolose 3:19) Amuna ayenera kukumbukira kuti nawonso amalakwitsa zinthu zina. Choncho ngati akufuna kuti Mulungu aziwakhululukira, ayenera kumakhululukiranso akazi awo. (Mateyu 6:12, 14, 15) Ngati mwamuna ndi mkazi amakhululukirana, akhoza kukhala ndi banja losangalala.

5. N’chifukwa chiyani mwamuna ayenera kulemekeza mkazi wake?

5 Yehova amafuna kuti amuna azilemekeza akazi awo. Mwamuna ayenera kuganizira zinthu zimene mkazi wake amafunikira ndipo sayenera kuiona nkhani imeneyi mopepuka. Ngati mwamuna sasamalira bwino mkazi wake, Yehova sangamve mapemphero ake. (1 Petulo 3:7) Kukonda Yehova ndi kumene kumachititsa kuti munthu akhale wamtengo wapatali kwa Yehovayo. Ndipo iye saona kuti amuna ndi ofunika kwambiri kuposa akazi.

6. Kodi mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuchitirana zinthu zotani posonyeza kuti ndi “thupi limodzi”?

6 Yesu anafotokoza kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana sakhalanso awiri, koma “thupi limodzi.” (Mateyu 19:6) Iwo sayenera kuchita zinthu zosakhulupirika zomwe zingakhumudwitse wina. (Miyambo 5:15-21; Aheberi 13:4) Aliyense ayenera kuonetsetsa kuti akukwaniritsa zosowa za mnzake pa nkhani yogonana. (1 Akorinto 7:3-5) Mwamuna azikumbukira kuti “palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.” Choncho mwamuna ayenera kusamalira ndi kukonda mkazi wake. Chimene akazi amafuna kwambiri ndi kuona amuna awo akuwachitira zinthu mokoma mtima komanso mwachikondi.—Aefeso 5:29.

ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI AKAZI OKWATIWA AZICHITA

7. N’chifukwa chiyani banja limafunikira kuti likhale ndi wina woti azilitsogolera?

7 Banja lililonse limafunikira kukhala ndi wina woti azilitsogolera n’cholinga choti onse m’banjamo azichita zinthu mogwirizana. Pa 1 Akorinto 11:3, Baibulo limati: “Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”

8. Kodi mkazi angasonyeze bwanji kuti amalemekeza kwambiri mwamuna wake?

8 N’zoona kuti mwamuna aliyense amalakwitsa zinthu zina koma mkazi wake akamamuthandiza ndiponso kugwirizana ndi zimene mwamunayo wasankha, banja lonse limayenda bwino. (1 Petulo 3:1-6) Baibulo limati: “Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Nanga bwanji ngati mwamunayo sakhulupirira zimene mkazi wakeyo amakhulupirira? Akufunikabe kumulemekeza kwambiri. Baibulo limati: “Inu akazi, muzigonjera amuna anu kuti ngati ali osamvera mawu akopeke, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu, poona okha ndi maso awo khalidwe lanu loyera ndi ulemu wanu waukulu.” (1 Petulo 3:1, 2) Makhalidwe abwino a mkazi angathandize kuti mwamuna wake azilemekeza zimene mkaziyo amakhulupirira.

9. (a) Kodi mkazi azitani ngati sakugwirizana ndi maganizo a mwamuna wake pa nkhani inayake? (b) Kodi palemba la Tito 2:4, 5 pali malangizo otani opita kwa akazi okwatiwa?

9 Kodi mkazi azichita chiyani ngati sakugwirizana ndi maganizo a mwamuna wake? Ayenera kufotokoza maganizo ake mwaulemu. Mwachitsanzo, nthawi ina Sara ananena zinthu zimene Abulahamu sanagwirizane nazo koma Yehova anamuuza kuti: “Mvera mawu ake.” (Genesis 21:9-12) Nthawi zambiri zimene mwamuna yemwe ndi Mkhristu angasankhe kuchita zimakhala zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, choncho mkazi wake ayenera kugwirizana ndi zimene mwamunayo wasankha. (Machitidwe 5:29; Aefeso 5:24) Mkazi wabwino amasamalira banja lake. (Werengani Tito 2:4, 5.) Ana ake komanso mwamuna wake amayamba kumukonda ndiponso kumulemekeza kwambiri akaona mmene amayesetsera kuwasamalira.—Miyambo 31:10, 28.

Kodi Sara anapereka chitsanzo chotani kwa akazi okwatiwa?

10. Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kupatukana ndiponso kuthetsa banja?

10 Nthawi zina mwamuna ndi mkazi wake akayambana amaona kuti chidule ndi kungopatukana kapena kuthetsa banja. Koma Baibulo limanena kuti “mkazi asasiye mwamuna wake,” ndipo “mwamunanso asasiye mkazi wake.” (1 Akorinto 7:10, 11) N’zoona kuti pakhoza kukhala mavuto ena aakulu omwe angapangitse kuti anthu apatukane, komabe sayenera kuiona nkhaniyi mopepuka. Nanga bwanji nkhani yothetsa banja? Baibulo limasonyeza kuti pali chinthu chimodzi chokha chimene chingapangitse kuti banja lithe. Banja lingathe ngati mwamuna kapena mkazi wagonana ndi munthu wina yemwe si mwamuna kapena mkazi wake.—Mateyu 19:9.

ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI MAKOLO AZICHITA

Yesu ndi chitsanzo chabwino kwa aliyense m’banja

11. Kodi ana amafunikira kwambiri chiyani?

11 Makolo muyenera kumapeza nthawi yokwanira yocheza ndiponso kuchitira limodzi zinthu ndi ana anu. Ana anu amafuna kuti muzicheza nawo ndipo chinthu china chimene amafunikira kwambiri n’kuwaphunzitsa za Yehova.—Deuteronomo 6:4-9.

12. Kodi makolo ayenera kuchita chiyani kuti ateteze ana awo?

12 Dziko la Satanali likuipiraipirabe ndipo muli anthu ena omwe amafuna kuvulaza ana athu, mwinanso kuwagwiririra. Makolo ena amaona kuti n’zovuta kukambirana ndi ana awo za nkhani ngati imeneyi. Komatu makolo ayenera kuchenjeza ana awo za anthu amenewa ndiponso kuwaphunzitsa mmene angawapewere. Makolo ayenera kudziwa kuti ndi udindo wawo kuteteza ana awo. *1 Petulo 5:8.

13. Kodi makolo ayenera kupewa chiyani akamalangiza ana awo?

13 Makolo alinso ndi udindo wophunzitsa ana awo makhalidwe abwino. Kodi angachite bwanji zimenezi? Ndi zoona kuti ana amafunika kuphunzitsidwa komanso kulangizidwa, koma simuyenera kuchita zimenezi mwaukali kapena mwankhanza. (Yeremiya 30:11) Musamalangize ana anu mutakwiya. Mawu anu sayenera kukhala “olasa ngati lupanga” chifukwa akhoza kuvulaza anawo. (Miyambo 12:18) Makolo muyenera kuthandiza ana anu kuti azidziwa chifukwa chake ayenera kukhala omvera.—Aefeso 6:4; Aheberi 12:9-11; onani Mawu Akumapeto 30.

ZIMENE MULUNGU AMAFUNA KUTI ANA AZICHITA

14, 15. N’chifukwa chiyani ana ayenera kumvera makolo awo?

14 Yesu ankamvera Atate wake pa chilichonse ngakhale pamene kuchita zimenezi kunali kovuta. (Luka 22:42; Yohane 8:28, 29) Yehova amafunanso kuti ana azimvera makolo awo.—Aefeso 6:1-3.

15 Ananu, muzikumbukira kuti mukamamvera makolo anu, ngakhale pamene kuchita zimenezi kuli kovuta, mumasangalatsa Yehova komanso makolo anuwo. *Miyambo 1:8; 6:20; 23:22-25.

N’chiyani chingathandize achinyamata kukhalabe okhulupirika anzawo akamawanyengerera kuti achite zoipa?

16. (a) Kodi Satana amanyengerera bwanji achinyamata kuti achite zinthu zoipa? (b) N’chifukwa chiyani ndi bwino kusankha anthu ocheza nawo omwe amatumikira Yehova?

16 Mdyerekezi angagwiritse ntchito anzanu komanso achinyamata ena kuti akunyengerereni kuchita zinthu zoipa. Iye amadziwa kuti n’zovuta kwambiri kuti mukane kuchita zimene anzanu akukuuzani kuti muchite. Mwachitsanzo, mwana wa Yakobo dzina lake Dina anali ndi anzake amene sankatumikira Yehova. Kucheza ndi anthu amenewo kunachititsa kuti iyeyo komanso anthu a m’banja lake akumane ndi mavuto. (Genesis 34:1, 2) Ngati mumakonda kucheza ndi anthu amene satumikira Yehova, angakupangitseni kuchita zinthu zimene Yehova amadana nazo. Kuchita zimenezi kungaike inuyo komanso anthu a m’banja lanu m’mavuto ndiponso kungamvetse chisoni Yehova. (Miyambo 17:21, 25) Choncho anzanu amene mungasankhe ayenera kukhala anthu amene amatumikira Yehova.—1 Akorinto 15:33.

BANJA LANU LIKHOZA KUKHALA LOSANGALALA

17. Kodi aliyense m’banja ayenera kuchita chiyani kuti banjalo likhale losangalala?

17 Aliyense m’banja akamatsatira malangizo a Mulungu, banjalo limapewa mavuto ambiri. Choncho ngati ndinu mwamuna wokwatira, muyenera kukonda kwambiri mkazi wanu. Ngati ndinu mkazi wokwatiwa, muyenera kulemekeza ndi kugonjera mwamuna wanu komanso muyenera kutengera chitsanzo cha mkazi wotchulidwa pa Miyambo 31:10-31. Ngati ndinu kholo, muziphunzitsa ana anu kukonda Mulungu. (Miyambo 22:6) Ngati ndinu bambo, muyenera ‘kuyang’anira bwino’ banja lanu. (1 Timoteyo 3:4, 5; 5:8) Ndipo ananu, muzimvera makolo anu. (Akolose 3:20) Muzikumbukira kuti aliyense m’banja angalakwitse zinthu zina, choncho mukalakwitsa muyenera kudzichepetsa n’kupempha munthu amene mwamulakwirayo kuti akukhululukireni. Zimenezi zikusonyezadi kuti m’Baibulo muli malangizo ochokera kwa Yehova omwe angathandize aliyense m’banja.

^ ndime 12 Mungapeze mfundo zokuthandizani kuteteza ana anu m’Mutu 32 m’buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 15 Ngati makolo akufuna kuti mwana achite zinthu zosemphana ndi malamulo a Mulungu, mwanayo sayenera kuwamvera.—Machitidwe 5:29.