Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 16

Sankhani Kulambila Mulungu

Sankhani Kulambila Mulungu

1, 2. Kodi tiyenela kudzifunsa funso lakuti ciani? Ndipo cifukwa ciani?

MWA kuphunzila Baibulo, mwafika podziŵa kuti anthu ambili amene amati amalambila Mulungu, amaphunzitsa ndi kucita zinthu zimene Mulungu amadana nazo. (2 Akorinto 6:17) Ndiye cifukwa cake Yehova amatilamula kuti ticoke m’zipembedzo zonama, kapena kuti mu “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 18:2, 4) Kodi inu mudzasankha kucita ciani? Aliyense ayenela kupanga cosankha. Tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi nifuna kulambila Mulungu m’njila imene iye afuna, kapena nifuna kum’lambila m’njila imene n’najaila?’

2 Ngati munacoka kale m’cipembedzo conama, kapena ngati munalayila, munacita bwino kwambili. Koma mwina pakali zinthu zina kapena miyambo ina ya cipembedzo conama imene mukali kucitako. Tiyeni tikambilane zina mwa zinthu zimenezo kuti tione cifukwa cake tiyenela kuziona mmene Yehova amazionela.

ZIFANIZILO NDI KULAMBILA MIZIMU YA MAKOLO

3. (a) N’cifukwa ciani cingakhale covuta kwa anthu ena kuti aleke kuseŵenzetsa zifanizilo polambila? (b) Nanga Baibulo imakambapo ciani pa kugwilitsila nchito zifanizilo polambila Mulungu?

3 Kwa zaka zambili, anthu ena akhala akugwilitsila nchito zifanizilo ndi tuakacisi polambila Mulungu m’nyumba zawo. Ngati inunso mumaseŵenzetsa zinthu zimenezi polambila, mungaone ngati kulambila Mulungu popanda zinthu zimenezi n’kosakwanila kapena n’kulakwa. Koma musaiŵale kuti Yehova amatiphunzitsa njila yomulambilila. Ndipo Baibulo imatiuza mosapita m’mbali kuti Yehova safuna kuti tiziseŵenzetsa zifanizilo pom’lambila.—Ŵelengani Ekisodo 20:4, 5; Salimo 115:4-8; Yesaya 42:8; 1 Yohane 5:21.

4. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kulambila makolo athu amene anamwalila? (b) N’cifukwa ciani Yehova analetsa anthu ake kuyesa kukamba ndi anthu amene anafa?

4 Anthu ena amacita zinthu zambili mwakhama kuti akondweletse makolo awo amene anamwalila, ngakhale kuwalambila. Koma tinaphunzila kuti akufa sangatithandize kapena kutivulaza. Iwo sali ndi moyo kwina kwake iyai. Ndipo kuyesa kukamba ndi anthu amene anafa n’koopsa kwambili, cifukwa mawu alionse amene angaoneke monga acokela kwa wacibanja amene anafa, amacokela kwa ziŵanda. Ndiye cifukwa cake Yehova analamula Aisiraeli kuti asayese kukambitsana ndi akufa, kapena kucita zinthu zilizonse zogwilizana ndi ziŵanda.—Deuteronomo 18:10-12; onani Zakumapeto 26 ndi 31.

5. N’ciani cingakuthandizeni kuleka kuseŵenzetsa zifanizilo polambila Mulungu, ndi kulambila makolo anu akufa?

5 N’ciani cingakuthandizeni kuti muleke kuseŵenzetsa zifanizilo polambila Mulungu, kapena kulambila makolo anu amene anafa? Mufunika kuŵelenga Baibulo ndi kusinkha-sinkha mmene Yehova amaonela zinthu zimenezi. Amaziona kukhala ‘zonyansa,’ kapena kuti zocititsa mselu. (Deuteronomo 27:15) Muzipemphela kwa Yehova masiku onse kuti akuthandizeni kumaona zinthu mmene iye amazionela, ndi kuti muzim’lambila m’njila imene iye amavomeleza. (Yesaya 55:9) Dziŵani kuti Yehova adzakupatsani mphamvu kuti mukwanitse kucotsa ciliconse cokhudzana ndi kulambila konama.

KODI TIYENELA KUKONDWELELA KHIRISMASI?

6. N’cifukwa ciani a cipembedzo anasankha December 25 kukhala tsiku lokondwelela kubadwa kwa Yesu?

6 Anthu ambili pa dziko lapansi amakondwelela Khirismasi. Ambili amaganiza kuti Khirismasi ni cikondwelelo ca kubadwa kwa Yesu. Komabe, cikondwelelo ca Khirismasi cimagwilizana ndi kulambila konama. Buku ina imafotokoza kuti Aroma acikunja anali kukondwelela kubadwa kwa dzuŵa pa December 25. Ndiye atsogoleli a cipembedzo pofuna kutembenuza anthu ambili acikunja kuti akhale Akhiristu, anasankha December 25 imeneyo kukhala tsiku lokondwelela kubadwa kwa Yesu. Anacitabe zimenezi ngakhale kuti Yesu sanabadwe pa December 25. (Luka 2:8-12) Koma ophunzila a Yesu sanali kukondwelela Khirismasi. Buku inanso inakamba kuti patapita zaka 200 kucokela pamene Yesu anabadwa, palibenso munthu anali kudziŵa tsiku leni-leni limene Yesu anabadwa. (Sacred Origins of Profound Things) Anthu anayamba kukondwelela Khirismasi patapita zaka mahandeledi angapo ndithu, apo Yesu anabwelela kale kumwamba.

7. N’cifukwa ciani Akhiristu oona sakondwelela Khirismasi?

7 Anthu ambili amadziŵa kuti Khirismasi inacokela ku cikunja, pamodzi ndi miyambo yake monga kupatsana mphatso. Mwacitsanzo, pa nthawi ina ku England ndi ku madela ena a ku America, boma linali kuletsa kucita zikondwelelo za Khirismasi cifukwa cakuti inacokela ku cikunja. Aliyense wopezeka kuti akondwelela Khirismasi anali kum’patsa cilango. Koma m’kupita kwa nthawi, anthu anayambanso kukondwelela Khirismasi. Nanga n’cifukwa ciani Akhiristu oona sakondwelela Khirismasi? Cifukwa amafuna kukondweletsa Mulungu pa ciliconse cimene amacita.

KODI TIYENELA KUKONDWELELA TSIKU LA KUBADWA?

8, 9. N’cifukwa ciani Akhiristu oyambilila sanali kukondwelelako masiku a kubadwa?

8 Cocitika cina cimene anthu ambili amakondwelela ni tsiku lawo la kubadwa. Kodi Akhiristu ayenela kukondwelela tsiku la kubadwa? Baibulo imangochula cabe zikondwelelo za tsiku la kubadwa za anthu amene sanali kulambila Yehova. (Genesis 40:20; Maliko 6:21) Ku nthawi zakale, anthu anali kucita zikondwelelo zimenezi polemekeza milungu yonama. Ndiye cifukwa cake Akhiristu a m’nthawi za atumwi, anali kuona “cikondwelelo ca tsiku la kubadwa ca munthu aliyense kukhala mwambo wacikunja.”—The World Book Encyclopedia.

9 Aroma ndi Agiriki akale anali kukhulupilila kuti munthu akabadwa panali kubwela mzimu winawake. Ndipo mzimu umenewo unali kuteteza munthuyo kwa umoyo wake wonse. Buku ina imakamba kuti “mzimuwo unali kukhala pa unansi winawake ndi mulungu amene nayenso anabadwa pa tsiku limene munthuyo anabadwa.”—The Lore of Birthdays.

10. N’cifukwa ciani Akhiristu sayenela kukondwelela masiku a kubadwa?

10 Kodi muganiza kuti Yehova amavomeleza zikondwelelo zocokela ku cipembedzo conama? (Yesaya 65:11, 12) Kutalitali! Ndiye cifukwa cake ife siticita zikondwelelo za masiku a kubadwa, kapena maholide alionse ocokela ku cipembedzo conama.

KODI ZILI NDI KANTHU KWENI-KWENI?

11. Kodi cimene anthu ena amacitila zikondwelelo za maholide n’ciani? Koma n’ciani ciyenela kukhala cacikulu kwa inu?

11 Anthu ena amadziŵa ndithu kuti Khirismasi ndi maholide ena zinacokela ku cikunja, koma safuna kuleka zikondwelelo zimenezo. Amaona kuti maholide amenewa amawapatsa mipata yabwino yosanguluka pamodzi ndi acibanja. Kodi inunso mumaona conco? Si kulakwa kupatula nthawi yosanguluka ndi a pabanja panu. Yehova ndiye anayambitsa mabanja, ndipo amafuna kuti tizikhala nawo pa ubale wabwino. (Aefeso 3:14, 15) Ngakhale n’conco, tiyenela kuika patsogolo unansi wathu ndi Yehova, m’malo mokondweletsa abululu ŵathu mwa kucita nawo maholide ogwilizana ndi cipembedzo conama. Ndiye cifukwa cake mtumwi Paulo anakamba kuti: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti covomelezeka kwa Ambuye n’citi.”—Aefeso 5:10.

12. Ni maholide abwanji amene Yehova sakondwela nawo?

12 Anthu ena amaona kuti kumene holide inacokela si vuto. Koma Yehova saona conco. Iye sakondwela ndi maholide amene anacokela ku zipembedzo zonama, kapena amene amatamanda anthu, mbendela, kapena zizindikilo zina za maiko. Mwacitsanzo, Aiguputo anali kucita zikondwelelo zambili za milungu yawo yonama. Aisiraeli atatuluka mu Iguputo, anatengela cikondwelelo cina ca cikunja ndi kucicha “cikondwelelo ca Yehova.” Koma Yehova anawalanga cifukwa ca zimenezo. (Ekisodo 32:2-10) Mogwilizana ndi mau a Yesaya, sitiyenela kukhudza ciliconse codetsedwa.’—Ŵelengani Yesaya 52:11.

KHALANI OGANIZILA ENA

13. Ni mafunso akuti ciani amene mungakhale nawo mukasankha kuleka kukondwelela maholide?

13 Mwina mukaganiza zoleka kukondwelela maholide mumakhala ndi mafunso ambili. Mwacitsanzo, mungafunse kuti: Niziwauza ciani anzanga a kunchito akanifunsa cimene sinikondwelela Khirismasi? Nanga wina akanipatsa mphatso ya Khirismasi niyenela kucita ciani? Nanga ngati mnzanga wa m’cikwati afuna kuti tikondwelele pamodzi holide, n’zacita bwanji? Ningathandize bwanji ana anga kuti asamakhumudwe pamene siticita cikondwelelo ca holide inayake, kapena masiku awo a kubadwa?

14, 15. Muyenela kucita ciani ngati munthu wina akupatsani moni wa holide kapena mphatso?

14 M’pofunika kuganizila bwino zimene mungayankhe ndi kucita pa cocitika ciliconse. Mwacitsanzo, ngati munthu wina akupatsani moni wa holide, musamunyalanyaze. Mukhoza kungoyankha kuti, “Zikomo.” Koma ngati wina afuna kudziŵa zambili, mungam’fotokozele cimene simukondwelela holide imeneyo. Koma osaiŵala kuti nthawi zonse muyenela kukhala wokoma mtima, woganizila ena, ndi waulemu. Baibulo imati: “Nthawi zonse mau anu azikhala acisomo, okoma ngati kuti mwawathila mcele, kuti mudziŵe mmene mungayankhile wina aliyense.” (Akolose 4:6) Mwina mungamuuze munthu ameneyo kuti mumakondwela kukhala ndi nthawi yosanguluka ndi ena, ndi kupatsana mphatso. Koma simukonda kucita zimenezo cabe cifukwa ca holide.

15 Nanga mungacite bwanji ngati wina akupatsani mphatso? Baibulo siipeleka malamulo pa ciliconse cimene tiyenela kucita. Koma imatiuza kuti tiyenela kukhala ndi cikumbumtima coyela. (1 Timoteyo 1:18, 19) Mwina munthu amene akupatsani mphatso imeneyo sadziŵa kuti simukondwelela holideyo. Kapena angakambe kuti: “Nidziŵa kuti simukondwelela holide, koma ningofuna kukupatsankoni mphatso cabe.” Zikakhala conco, mungasankhe kulandila mphatsoyo kapena iyai. Cabe mutsimikizile kuti cosankha cimene mungapange cikusiyeni ndi cikumbumtima coyela. Tiyenela kupewa kucita ciliconse cimene cingawononge unansi wathu ndi Yehova.

MMENE MUNGACITILE NDI A M’BANJA MWANU

Anthu amene amatumikila Yehova amakhala acimwemwe

16. Mungacite ciani ngati abululu ŵanu afuna kuti mucite nawo cikondwelelo ca holide?

16 Mungacite ciani ngati a m’banja mwanu afuna kukondwelela holide inayake? Simuyenela kulimbana nawo. Musaiŵale kuti nawonso ali ndi ufulu wosankha zimene afuna kucita. Muyenela kukhala wokoma mtima ndi kulemekeza zosankha zawo, monga mmene inunso mumafunila kuti azilemekeza zosankha zanu. (Ŵelengani Mateyu 7:12.) Nanga bwanji ngati abululu ŵanu afuna kuti mukakhale nawo pa holide? Mukalibe kusankha cocita, pemphelani kwa Yehova kuti akuthandizeni kupanga cosankha canzelu. Fufuzani mfundo zimene zingathandize pa cocitikaco. Musaiŵale kuti colinga canu nthawi zonse ni kukondweletsa Yehova.

17. Mungawathandize bwanji ana anu kuti asamakhumbile pamene aona anzawo acita zikondwelelo za maholide?

17 Nanga mungathandize bwanji ana anu pamene aona kuti anthu ena amakondwelela maholide? Ni bwino kuti nthawi ndi nthawi muzikonzako kaphwando kapadela. Nthawi zina muziwadabwitsako ndi mphatso. Ndipo mphatso ina yabwino kwambili imene mungapatse ana anu ni kupatula nthawi yoceza nawo, ndi kuwaonetsa kuti muwakonda.

CITANI ZINTHU ZOGWILIZANA NDI KULAMBILA KOONA

18. N’cifukwa ciani tiyenela kupezeka ku misonkhano?

18 Kuti tikondweletse Yehova, tiyenela kucoka ku cipembedzo conama, ndiponso kusiya miyambo ndi maholide ogwilizana ndi cipembedzo conama. Tiyenelanso kugwilizana ndi cipembedzo coona. Koma tingacite bwanji zimenezo? Njila imodzi ni kupezeka pa misonkhano ya Cikhiristu. (Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.) Misonkhano ni mbali yofunika kwambili pa kulambila koona. (Salimo 22:22; 122:1) Tikafika ku misonkhano, timakhala ndi mwayi wolimbikitsana wina ndi mnzake.—Aroma 1:12.

19. N’cifukwa ciani mufunika kuuzako ena za coonadi ca m’Baibulo cimene muphunzila?

19 Cinthu cina cimene muyenela kucita mukasankha cipembedzo coona, ni kuuzako ena zimene mumaphunzila m’Baibulo. Anthu oculuka amavutika mtima kwambili akaona zinthu zoipa zimene zicitika pa dziko lapansi. (Ezekieli 9:4) Ndipo mwina mudziŵako ena. Muziwauzako za ciyembekezo cabwino cimene muli naco. Pamene mupezeka ku misonkhano ya Cikhiristu ndi kuuzako anzanu coonadi ca m’Baibulo, simudzafunanso kugwilizana ndi cipembedzo conama, kapena kucitako miyambo yake. Kukamba zoona mudzakhala wokondwela, ndipo Yehova adzakudalitsani kwambili cifukwa ca khama lanu posankha kum’lambila m’njila yoyenela.—Malaki 3:10.