Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

4

Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Mukamavomereza zimene mwalakwitsa, anthu amakulemekezani komanso kukudalirani.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tiyerekeze kuti Tim akusewera mpira ndi anzake ndipo iye ataumenya, waswa galasi la galimoto ya eni.

Kodi inuyo mukanakhala Tim mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

PALI NJIRA ZITATU ZIMENE MUNGATSATIRE:

  1. YOYAMBA. Kuthawa.

  2. YACHIWIRI. Kuimba mlandu munthu wina.

  3. YACHITATU. Kupita kwa eniake a galimoto, kuwauza zimene zachitika n’kulonjeza kuti mulipira.

Mwina mungaganize kuti Njira Yoyambayo ndi yabwino. Koma ndi bwino kuvomereza chilichonse chimene mwalakwitsa.

N’CHIFUKWA CHIYANI MUYENERA KUVOMEREZA ZIMENE MWALAKWITSA?

  1. Baibulo limasonyeza kuti tikalakwitsa tiyenera kuvomereza.

    Baibulo limati: “Tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.

  2. Nthawi zambiri anthu amakhululukira munthu amene amavomereza zolakwa zake.

    Baibulo limati: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma woulula n’kuwasiya adzachitiridwa chifundo.”—Miyambo 28:13.

  3. Chofunika kwambiri n’chakuti, zimasangalatsa Yehova.

    Baibulo limati: “Pakuti munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”—Miyambo 3:32.

Mtsikana wina wazaka 20 dzina lake Karina anayesetsa kubisira bambo ake lisiti losonyeza kuti apolisi anamulipiritsa chifukwa chothamangitsa kwambiri galimoto. Koma iye anati: “Patadutsa chaka, bambo anga anapeza lisitilo ndipo zinavuta kwabasi.”

Kodi tikuphunzirapo chiyani? Karina anati: “Ukabisa zimene walakwitsa, umapangitsa kuti zinthu ziipe kwambiri. Ndipo pakapita nthawi umakumanabe ndi zotsatira zake.”

MUZIPHUNZIRAPO KANTHU PA ZIMENE MWALAKWITSA

Baibulo limati: “Paja tonsefe timapunthwa [kapena kuti timalakwitsa] nthawi zambiri.” (Yakobo 3:2) Choncho malinga ndi zimene takambiranazi, ndi nzeru kuvomereza mwamsanga zimene talakwitsa.

Chinthu china chofunika ndi kuphunzirapo kanthu pa zimene mwalakwitsa. Mtsikana wina dzina lake Vera anati: “Ndimayesetsa kuphunzira kanthu pa chilichonse chimene ndalakwitsa. Ndimachita zimenezi kuti ndikhale munthu wabwino komanso kuti ndidzachite mwanzeru ndikadzakumananso ndi zinthu zofanana ndi zimene ndalakwitsazo.” Tiyeni tione mmene nanunso mungachitire zimenezi.

Tiyerekeze kuti mwabwereka njinga ya bambo anu ndiye yawonongeka. Kodi mungatani?

  • Osanena kalikonse n’kumaganiza kuti sazindikira.

  • Kuwauza zonse zimene zachitika.

  • Kuwauza zimene zachitika koma n’kusonyeza kuti munthu wina ndi amene analakwitsa.

Mwalephera mayeso chifukwa simumawerenga. Kodi mungatani?

  • Kunena kuti mayeso anali ovuta kwambiri.

  • Kuvomereza kuti mwalepheradi.

  • Kunena kuti aphunzitsi amadana nanu.

Kuganizira kwambiri zimene munalakwitsa, kuli ngati kumangoyang’anitsitsa pagalasi loonera kumbuyo pamene mukuyendetsa galimoto

Tiyerekeze kuti pa zitsanzo zimene tatchulazi, inuyo ndinu (1) bambo kapena (2) mphunzitsi. Kodi mungamve bwanji ngati mwana wanu kapena mwana wa m’kalasi mwanu atavomereza zimene walakwitsa? Nanga mwanayo atabisa zimene walakwitsa, mungaganize kuti ndi wotani?

Tsopano ganizirani zimene mwalakwitsa chaka chathachi, ndipo yankhani mafunso otsatirawa.

Kodi ndinalakwitsa chiyani? Kodi ndinatani?

  • Ndinabisa.

  • Ndinaimba mlandu munthu wina.

  • Ndinavomereza kuti ndinalakwitsa.

Kodi munamva bwanji mutabisa zimene munalakwitsa?

  • Ndinasangalala poganiza kuti ndapulumuka.

  • Ndinadandaula kuti ndinayenera kunena zoona.

Kodi mukuganiza kuti mukanayenera kuchita chiyani?

Kodi munaphunzirapo chiyani pa zimene munalakwitsa?

MUKUGANIZA BWANJI?

N’chifukwa chiyani anthu ena savomereza zimene amalakwitsa?

Ngati inuyo simuvomereza zimene mwalakwitsa, kodi anthu ena angaganize kuti ndinu otani? Nanga ngati mumavomereza zimene mwalakwitsa, kodi anthu ena angaganize kuti ndinu otani?—Luka 16:10.