Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

4

Niyenela Kucita Ciani Nikacita Colakwa?

Niyenela Kucita Ciani Nikacita Colakwa?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Ngati uvomeleza cimene walakwa udzakhala wanzelu ndi wodalilika.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Ganizila cocitika ici: Poseŵela na anzake, mwangozi Tim aponyela bola ku motoka ya aneba, nophwanya windo.

Kukhala Tim, ungacite ciani?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

UNGACITE CIANI PA ZINTHU ZITATU IZI:

  1. Kuthaŵa.

  2. Kunamizila wina.

  3. Kukamba zoona kwa aneba, na kuwauza kuti udzalipila.

Mtima wako ungafune kucita zili pa A. Koma pali zifukwa zabwino zovomelela cimene walakwitsa—kaya n’kuphwanya windo kapena kulakwitsa cinacake.

ZIFUKWA ZITATU ZOVOMELELA COLAKWA

  1. Ndiye cilungamo.

    Baibo imati: ‘Timafuna kucita zinthu zonse moona mtima.’—Aheberi 13:18.

  2. Kambili, anthu amakhululukila munthu wovomela colakwa cake.

    Baibo imati: “Wobisa macimo ake zinthu sizidzamuyendela bwino, koma woulula n’kuwasiya adzacitilidwa cifundo.”—Miyambo 28:13.

  3. Cofunika kwambili, Mulungu amakondwela.

    Baibo imati: “Munthu wocita zaciphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”—Miyambo 3:32.

Pamene Karina, wa zaka 20, anapatsidwa tiketi ya mlandu wothamangitsa kwambili motoka, anabisa zimenezi kwa makolo ake. Koma m’kupita kwa nthawi nkhaniyo inaululika. Iye anati: “Patapita caka cimodzi, atate anatulukila tiketi ya mlandu ija. Sizinan’thele bwino!”

Phunzilo? Karina anati: “Kubisa colakwa kumaipitsilatu zinthu zikaululika.” Paja mwambi umati, cozemba cinakumana ndi cokwaŵa.

KUPHUNZILAPO KANTHU PA ZOLAKWA ZAKO

Baibo imati: “Tonsefe timapunthwa [timalakwa] nthawi zambili.” (Yakobo 3:2) Ndipo kuvomela colakwa kumaonetsa kuti ndiwe wodzicepetsa ndi wanzelu, maka-maka kuvomela mwamsanga.

Sitepu yotsatila, ufunika kuphunzilapo kanthu pa zolakwa zako. Mtsikana wina, Vera, anati: “Nikacita colakwa ciliconse, nimayesa kuphunzilapo kanthu. Nimaona mmene ningapewele colakwaco, kuti nikacite mwanzelu ulendo wotsatila.” Tiye tione mmene ungacitile zimenezi.

Wabweleka njinga ya atate ŵako, ndiye waiwononga penapake. Ungacite ciani?

  • Kukhala zii, na kupemphelela kuti asadziŵe.

  • Kuwauza cilungamo.

  • Kunamizila wina.

Wafeluka mayeso ndaŵa sunali kuŵelenga. Ungacite ciani?

  • Kuimba mlandu mayeso kuti anali olimba.

  • Kuvomela kuti wafeluka cifukwa cosaikako nzelu.

  • Kupatsa mlandu atica kuti sanaconge bwino ndaŵa sakukonda.

Kumaganizila zolakwa zakumbuyo kuli monga kumangoyang’ana kumbuyo pa gilasi uku ukuyendetsa motoka.

Manje ganizilanso zocitika zimenezi, ndipo yelekeza kuti ndiwe (1) Atate ako (2) atica ako. Uganiza atate ŵako olo atica ako angakuone bwanji ngati wavomela msanga colakwa cako? Nanga angakuone bwanji akadziŵa kuti wangobisa zimene wacita?

Lomba ganizila colakwa ciliconse cimene unacitapo caka catha na kuyankha mafunso aya.

Unalakwitsa ciani? Nanga unacita bwanji?

  • N’nabisa.

  • N’nanamizila wina.

  • N’naulula mwamsanga

Ngati unabisa colakwaco, unamvela bwanji pambuyo pake?

  • Bwino ngako—n’napulumuka!

  • N’namvela kuipa—n’nafunika kuulula.

Ukayang’ana kumbuyo, uona kuti unafunika kucita bwanji?

Unaphunzilapo ciani pa colakwa cako?

UGANIZA BWANJI?

N’cifukwa ciani anthu ena savomela zolakwa zawo?

Uganiza anthu angakuone bwanji ngati nthawi zonse umabisa zolakwa zako? Nanga angakuone bwanji ngati umavomela msanga ukalakwa?—Luka 16:10.