Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

5

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?

Kodi Ndingatani Anthu Ena Akamandivutitsa Kusukulu?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Zimene mungachite zingapangitse kuti asiye kukuvutitsani kapena azikuvutitsani kwambiri.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Taganizirani izi: Mnyamata wina dzina lake Thomas sakufunanso kupita kusukulu chifukwa chakuti anzake akhala akufalitsa nkhani zabodza zokhudza iyeyo. Izi zapangitsa kuti azimupatsa mayina achipongwe. Ena amamuphumitsa mabuku kenako n’kukhala ngati inali ngozi, kapena kumukankha n’kuthawa iyeyo potembenuka osadziwa kuti wamukankha ndani. Dzulo laliwisili ena analemba zomuopseza pa intaneti.

Kodi inuyo mukanakhala Thomas, mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Musaganize kuti palibe chimene mungachite. Ndipotu mungathe kupangitsa kuti munthu asiye kukuvutitsani popanda kumubwezera. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

  • MUSAMASONYEZE KUTI ZAKUKHUDZANI. Baibulo limati: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzeru amakhala wodekha mpaka pamapeto.” (Miyambo 29:11) Mukayesetsa kuti muoneke ngati sizinakukhudzeni, anthu amene akukuvutitsaniwo akhoza kusiya.

  • MUSAMABWEZERE. Baibulo limati: “Musabwezere choipa pa choipa.” (Aroma 12:17) Kubwezera kungachititse kuti zinthu ziipireipire.

  • MUSAMAPITE PAMALO AMENE ANTHU ANGAKUVUTITSENI. Baibulo limati: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Choncho muziyesetsa kupewa malo amene mukudziwiratu kuti mungakumaneko ndi anthu omwe angakuvutitseni.

  • MUZICHITA ZIMENE SAKUYEMBEKEZERA. Baibulo limati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Mwina mungangoyankha mwanthabwala. Mwachitsanzo, ngati munthu wakunyozani kuti ndinu wonenepa kwambiri, mukhoza kungovomereza moseka n’kunena kuti: “Ndiyesetsa kuti ndiwondeko.”

  • MUZINGOCHOKAPO. Mtsikana wina wazaka 19 dzina lake Nora, anati: “Anthu ena akamakuvutitsa, iwe n’kungochokapo, zimasonyeza kuti ndiwe wanzeru komanso wolimba mtima kuposa iwowo. Zimasonyezanso kuti ndiwe wodziletsa, khalidwe lomwe anthu ovutitsa anzawo sakhala nalo.”—2 Timoteyo 2:24.

  • MUSAMACHITE ZINTHU MODZIKAYIKIRA. Amene amavutitsa anzawo amapezerera anthu amene amadzikayikira chifukwa amadziwa kuti sangawabwezere. Koma akaona kuti simukuwapatsa mpata komanso simukuwaopa, angakusiyeni.

  • MUZIUZA ENA. Munthu wina amene anali mphunzitsi anati: “Ndikulimbikitsa aliyense amene akuvutitsidwa kuti aziuza ena. Kuuza ena n’kothandiza ndipo kungachititse kuti anthu ena asadzavutitsidwenso.”

Kusadzikayikira kungapangitse kuti mukhale olimba mtima kuposa munthu amene akukuvutitsani