Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

5

Ningacite Bwanji Ngati Ena Anivutitsa ku Sukulu?

Ningacite Bwanji Ngati Ena Anivutitsa ku Sukulu?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Zimene ungacite zingapangitse zinthu kukhalako bwino kapena kuipilatu.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Ganizila cocitika ici: Thomas safuna kuyenda kusukulu lelo, mailo, kapena tsiku lililonse. Papita miyezi itatu pamene vuto iyi inayamba, pamene anzake kusukulu anafalitsa mabodza oipa onena za iye. Ndiyeno, anzake anayamba kum’patsa maina onyoza. Komanso, zinali kucitika kuti wina anamizila kum’guda mwangozi n’kugwetsela mabuku ake pansi. Nthawi zinanso wina m’gulu anali kumukankha, koma akaceuka osaona kuti n’ndani. Mailo zomuvutitsa zinafika poipa kwambili, wina anam’tumizila meseji yomuopseza kuti akam’menya kusukulu.

Ukanakhala Thomas ukanacita bwanji?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

Sikuti palibiletu zimene ungacite! Ndipo kukamba zoona, ungagonjetse munthu wokuvutitsa popanda kumenyana naye. Motani?

  • OSAYANKHA MOKALIPA. Baibo imakamba kuti: “Wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse, koma wanzelu amakhala wodekha mpaka pamapeto.” (Miyambo 29:11) Ngati uonetsa kuti sunakalipe, ngakhale kuti mumtima cakuŵaŵa, amene akuvutitsa angamvele ulesi na kukuleka.

  • OSABWEZELA. Baibo imakamba kuti: “Musabwezele coipa pa coipa.” (Aroma 12:17) Kubwezela kudzangoipitsilatu zinthu.

  • OSADZINGENETSA DALA M’MAVUTO. Baibo imanena kuti: “Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala.” (Miyambo 22:3) Ngati zingatheke, uzipewa anthu ovutitsa anzawo, na malo kumene angapezeke.

  • YESA KUCITA ZIMENE SAYEMBEKEZELA. Baibo imakamba kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Nthabwala nazo zimathandiza. Mwacitsanzo, ngati munthu wokuvutitsa akamba kuti ndiwe dugude, kapena dumbo, ukhoza kungoseka n’kunena kuti, “Owo, mwina nifunika kuyondako pang’ono!”

  • COKAPO. “Nora wa zaka 19 anakamba kuti: “Kusayankha na kucokapo kumaonetsa kuti una nzelu ndipo ndiwe wolimba kuposa munthu amene akuvutitsa.” Anatinso: “Kumaonetsa kuti ndiwe wodziletsa—khalidwe limene munthu wokuvutitsa alibe.”—2 Timoteyo 2:24.

  • KHALA NA CIDALILO. Anthu ovutitsa anzawo amadziŵa kuti uyu munthu ni wosadzidalila ndipo ni wamantha. Koma akaona kuti sucita mantha ndipo suwaikako nzelu, ambili amakusiya.

  • UZAKO MUNTHU WINA. Munthu wina amene anakhalapo tica pa sukulu anakamba kuti: “N’nali kulimbikitsa ana a sukulu kuti wina akawavutitsa azimunenela. Ndiye zofunika kucita kuti ena aziopa kuvutitsa anzawo.”

Kudzidalila kudzakupatsa mphamvu zimene wokuvutitsa alibe