Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

6

Ningakane Bwanji Kutunthiwa na Anzanga?

Ningakane Bwanji Kutunthiwa na Anzanga?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Ngati umadziimila pawekha, umadziŵa zimene ucita, m’malo moleka anzako kulamulila umoyo wako.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Ganizila cocitika ici: Pamene Brian aona anzake aŵili kusukulu akubwela kwa iye, acita kumvela cinthu m’mimba. Kaŵili konse mu wiki imeneyi ayesa kumunyengelela kuti apepe fwaka. Aka manje n’kacitatu.

Mnyamata woyamba akuti:

“Na lelo uli wekha? Wamuona uyu, ni mnzanga.”

Pochula kuti “mnzanga,” achaila diso mnzake pamene atulutsa kanthu kena m’thumba n’kutambasula dzanja kupatsila Brian.

Brian aona kuti ni fwaka. Poona zimenezi, Brian ca m’mimba cacita kumangilatu.

Ndiyeno akuti: “Koma n’nakuuzani kale kuti ine sini . . . ”

Mnyamata waciŵili am’dula mau, amvekele: “Iwe nawe, osacita mantha!”

Brian modzilimbitsa ayankha kuti: “Iyai, simantha!”

Pamenepo mnyamatayo afungatila Brian. Ndiyeno amuuza mwaubwenzi kuti: “Ni kafwaka cabe aka, pang’ono cabe.”

Kenako mnyamata woyamba uja abweletsa fwaka ija kukamwa kwa Brian, na kum’nong’oneza kuti: “Sitidzauza aliyense. Palibe adzadziŵa.”

Kukhala Brian, ungacite ciani?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

Kodi anzake a Brian anayamba aganizila bwino-bwino pa zimene akucita? Kodi amacitadi zimene anasankha kucokela pansi pa mtima? Osati kweni-kweni. Iwo anangotunthiwa cabe na anzawo. Poopa kusekewa, amalola anzawo kulamulila umoyo wawo.

Ngati zimenezi zingacitilike iwe, kodi ungacite bwanji kuti ukane kutunthiwa na anzako?

  1. ONELATU PATALI

    Baibo imacenjeza kuti: “Wocenjela ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziŵa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” —Miyambo 22:3.

    Kambili, vuto ungaioneletu ikali patali. Mwacitsanzo, bwanji ngati waona kagulu ka anzako akusukulu akubwela kutsogoko kwako, ndipo waona kuti akoka fodya. Poonelatu vuto imeneyo, umakonzekela mocitila nayo.

  2. UFUNIKA KUGANIZA BWINO

    Baibo ikamba kuti: “Khalani ndi cikumbumtima cabwino.”—1 Petulo 3:16.

    Udzifunse kuti, ‘Nidzamvela bwanji m’tsogolo nikatsatila anzanga?’ N’zoona kuti anzako adzakukonda. Koma pambuyo pake udzamvela bwanji? Kodi ndiwe wokonzeka kutaya khalidwe lako labwino kuti cabe ukondweletse anzako akusukulu?—Ekisodo 23:2.

  3. PANGA COSANKHA

    Baibo imati: “Munthu wanzelu amacita mantha.”—Miyambo 14:16.

    Munthu aliyense afunika kupanga zosankha na kuyembekezela zotulukapo zake. Baibo imatiuza za anthu amene anapanga zosankha zanzelu, monga Yosefe, Yobu, na Yesu. Komanso, imatiuza za anthu amene anapanga zosankha zoipa, monga Kaini, Esau, na Yudasi. Nanga iwe udzapanga zosankha zabwanji?

Baibo imakamba kuti: “Khala wokhulupilika m’zocita zako zonse.” (Salimo 37:3) Ngati unaganizilapo kale pa zotulukapo, ndipo sufuna kuti zikakucitikile, kukana kucita cinthu sikuvuta—ndipo kumapindulitsa.

Usade nkhawa—sufunikila kucita kuwafotokozela zambili anzako. Ungawauze cabe molimba mtima kuti SINIFUNA. Kapena, pofuna kuwaonetsa kuti wakanilatu kwa mtu wa galu, ungakambe kuti:

  • “Osaniŵelengelako!”

  • “Sinicita zimenezo!”

  • “Na imwe mudziŵa kuti siningacite zimenezo!”

Cofunika ni kuyankha mosawaya-waya, komanso molimba mtima. Ndipo ungadabwe mmene anzako angakulekele mwamsanga.

NGATI ANZAKO AKUSEKA

Ngati ugonja pamene anzako akutuntha, udzakhala monga ciloboti cawo

Kodi ungacite bwanji ngati anzako akuseka? Bwanji ngati akamba kuti, “Ndiwe camantha?” Ufunika kudziŵa colinga cokuuzila zimenezi. Angofuna kukuzunza. Nanga ungayankhe bwanji? Pali zinthu ziŵili zimene ungacite.

  • Ukhoza kuvomeleza zimene akamba. (N’zoona n’namantha! Ndiyeno peleka cifukwa mwacidule.)

  • Amvetse nsoni. Coyamba kana zimene afuna kuti ucite na kuwauza cifukwa cokanila. Ndiyeno asoŵetse cokamba. (“Nadabwa, anthu anzelu monga imwe kupepa fwaka!”)

Ngati anzako apitiliza kukuvutitsa, cokapo! Cifukwa ngati sucokapo, adzapitiliza kukuvutitsa kuti ucite zimene afuna. Koma ukacokapo, adzaona kuti sangakusinthe.

N’zoona kuti sungapeweletu kuvutitsiwa m’njila zinazake. Koma ukhoza kukhala wokonzeka kukamba zimene sufuna, na kusalola anzako kulamulila umoyo wako. Koma zonse zidalila iwe kucitapo kanthu.—Yoswa 24:15.