Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

8

Niyenela Kudziŵa Ciani za Ogona Akazi Mwacikakamizo?

Niyenela Kudziŵa Ciani za Ogona Akazi Mwacikakamizo?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Caka ciliconse akazi mamiliyoni ambili, maka-maka acicepele, amagonewa mwacikakamizo.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Mwadzidzidzi, mwamuna wina anangomuti gwii Annette n’kumugwetsela pansi. Iye anati: “Ninayesa kulimbana naye na mphamvu zanga zonse. N’nakuwa, koma sin’nali kumveka cifukwa ananifina kwambili. N’nayesa kum’kankha, kum’ponda, kum’menya, na kum’kwalaula. Kenako, anangotenga mpeni n’kunilasa. Ine mphamvu zonse zinangoti zii!”

Sembe unali iwe ukanacita ciani?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

N’zoona kuti ungakhale wosamala kwambili, maka-maka poyenda usiku kwinakwake. Koma zinthu zoipa zingakucitikilebe. Baibo imakamba kuti: “Anthu othamanga kwambili sapambana pampikisano [nthawi zonse, nwt], . . . ngakhale odziŵa zinthu sakondedwa, cifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka zimagwela onsewo.”—Mlaliki 9:11.

Mofanana ndi Annette, atsikana ambili amagonewa mwacikakamizo. Ndipo ena amene amawagwila ni anthu odziŵika, ngakhale abululu awo. Pamene Natalie anali na zaka 10 cabe, mnyamata wa paneba anam’gwila na kugona naye. Iye anati: “N’nacita mantha na manyazi kwambili cakuti poyamba sin’nauzeko aliyense.”

SI NDIWE UNACITITSA

Annettee akali kudziimba mlandu pa zimene zinam’citikila. Iye akuti: “Nthawi zambili nimaziganizila zimene zinacitika zija. Nimaona monga sin’nalimbikile kwambili kulimbana naye. Koma coona n’cakuti, pamene analilasa mpeni, n’nacita mantha kwambili. Sin’nakwanitse kucitanso ciliconse. Koma pano niona monga n’nafunika kulimbanabe naye.”

Natalie nayenso amavutika na kudziimba mlandu. Iye akuti: “N’nalakwa kum’dalila kwambili mnyamata uja. Makolo anga anali kutiuza kuti tisamasiyane na mng’ono wanga pokaseŵela kwinakwake, koma ine sin’namvele. Mwa ici, niona kuti ndine n’napeleka mpata kuti mnyamata uja anigwile. Banja lathu lonse linavutika kwambili na cocitikaco, ndipo niona kuti ndine n’nacititsa zonsezo. Zimenezi zimanivutitsa maganizo maningi.”

Ngati na iwe umvela monga Annette na Natalie, uzikumbukila kuti munthu akagonewa mwacikakamizo si kufuna kwake. Anthu ena amayesa kupeputsa nkhani pokamba kuti ni mmene anyamata alili, kapena kuti atsikana ndiwo amacititsa. Koma palibe munthu ayenela kugonewa mwacikakamizo. Ngati zimenezi zinakucitikilapo, sindiwe unacititsa.

Kukamba zoona, n’copepuka kuŵelenga kuti “si ndiwe unacititsa.” Koma kukhulupilila kungakhale kovuta. Ena amabisa mmene amvelela, conco amadziimba mlandu na kungofela mkati. Koma kodi kubisa nkhaniyo kumathandiza ndani—iwe kapena munthu amene anakugwila? Conco, n’cinthu canzelu kuulula.

UZAKO WINA

Baibo imatiuza kuti pamene mavuto a munthu wokhulupilika Yobu anafika pacimake, anati: “Ndilankhula cifukwa ca kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:1) Kucita cimodzi-modzi kungakuthandize. Ungauzeko munthu amene umam’dalila. Ndipo ukacita zimenezi, ungaiŵaleko zimene zinacitika na kusavutika nazo maganizo kwambili.

Osangofela mkati na maganizo. Uzako munthu wina amene angakuthandize

N’zimene Annette anacita. Iye anati: “N’nauzako mzanga wa pamtima amene anan’limbikitsa kukauzako akulu aŵili a mumpingo mwathu. N’nacitadi zimenezo. Iwo anakambilana nane kangapo, ndipo anan’thandiza kumvetsetsa kuti si ndine n’nacititsa. Sunali mlandu wanga.”

Natalie anauzako makolo ake zimene zinam’citikila. Iye anati: “Ananilimbikitsa ngako kuti nimasuke na kuwafotokozela zonse. Zimenezi zinan’thandiza kucepetsako cisoni na mkwiyo mumtima mwanga.”

Cinanso cimene cinathandiza Natalie ni pemphelo. Iye anati: “Kukamba na Mulungu kunan’thandiza ngako, maka-maka pamene cinali kunikanga kuuzako munthu wina. Koma m’pemphelo, nimakamba momasuka, ndipo nimamvelako bwino.”

Monga mmene Baibo imakambila, kuli “nthawi yocilitsa.” (Mlaliki 3:3) Uzicita zinthu zokuthandiza, monga kupumula mokwanila. Koma copambana zonse, uzidalila Mulungu wa citonthozo conse, Yehova. —2 Akorinto 1:3, 4.

NGATI ULI PA MSINKHU WOKHOZA KUKHALA PACIBWENZI

Ngati ndiwe mtsikana, ndipo wina akunyengelela kuti ucite naye zoipa, ufunika kukana mwamphamvu kuti, “Osacita zimenezo!” kapena kuti, “Osanigwila!” Usaope kuti adzakukana. Ngati akukana pa cifukwa cimeneci, ndiye kuti ni gong’a. Ukapeze wina amene angalemekeze thupi yako na makhalidwe ako.

MAFUNSO PA KUVUTITSA MUNTHU PA ZAKUGONANA

Coretta anati: “Kusukulu kwathu, nthawi zina anyamata anali kunidonsa bra yanga kumbuyo na kuniuza zopusa—monga zakuti ningamvele bwino kugona nawo.”

Kodi uganiza zimene anyamatawo anali kucita ni

  1. Kuseka naye cabe?

  2. Kungoceza naye zacikondi?

  3. Kuvutitsa munthu pa zakugonana?

Candice naye anati: “Tili mu basi, mnyamata wina ananigwila pakwanja noyamba kuniuza zinthu zopusa. N’namumenya pakwanja kuti anileke nomuuza kuti ‘coka apa.’ Ananiyang’ana moipidwa kwambili monga ndine wofuntha.”

Uganiza zimene mnyamata uyu anacita kwa Candice zinali ciani?

  1. Kuseka naye cabe?

  2. Kungoceza naye zacikondi?

  3. Kuvutitsa munthu pa zakugonana?

Nayenso Bethany anasimba kuti: “Caka catha, mnyamata wina anali kumangoniuza kuti anikonda, nonipempha kuyenda naye kokaceza. Ngakhale n’nali kukana iye sanali kuleka. Ndipo nthawi zina anali kunisisita pakwanja. Olo nimuletse bwanji sanali kumvela. Ndiyeno tsiku lina pamene n’naŵelama kuti nimange nsapato, anangofika n’kunimenya kumatako.”

Mmene iwe uonela, kodi mnyamata uyu anali:

  1. Kuseka naye cabe?

  2. Kungoceza naye zacikondi?

  3. Kuvutitsa munthu pa zakugonana?

Pa mafunso onse atatu, yankho yoyenela ni C.

Kodi kuvutitsa munthu pa zakugonana kumasiyana bwanji na kungoceza na munthu zacikondi kapena kuseka naye cabe?

Kuvutitsa munthu pa zakugonana m’pamene munthuyo sagwilizana na zimene winayo acita kwa iye. Ndipo wovutitsayo saleka ngakhale winayo amuletse.

Kuvutitsa munthu pa zakugonana n’koopsa. Wina akhoza kugonedwa mwacikakamizo.