Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

10

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?

Kodi Baibulo Lingandithandize Bwanji?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Baibulo limanena kuti “malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Ngati zimenezi zili zoona ndiye kuti Baibulo lingakuthandizeni.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tiyerekeze kuti mnyamata wina dzina lake David akuyendetsa galimoto ndipo wazindikira kuti ali kumalo achilendo. Atayang’ana zikwangwani komanso zinthu zina akuzindikira kuti wasochera. Ayenera kuti anasiya msewu wolondola penapake.

Kodi inuyo mukanakhala David, mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Pali zinthu zingapo zimene mungachite:

  1. Kufunsa anthu ena.

  2. Kuona pamapu kapena kugwiritsa ntchito chipangizo chothandiza kudziwa kumene ukupita chotchedwa GPS.

  3. Kumangopitabe poganiza kuti mwina kutsogoloko mupeza njira yolondola.

N’zodziwikiratu kuti Njira Yachitatuyi ndi yosathandiza kwenikweni.

Pamene Njira Yachiwiriyi ndi yabwino kuposa yoyambayo. Tikutero chifukwa munthu akakhala ndi mapu kapena GPS zimamutsogolera pa ulendo wonsewo.

Chimodzimodzinso ndi Baibulo.

Buku limeneli lingakuthandizeni m’njira izi:

  • Kulimbana ndi mavuto

  • Kudziwa mmene mulili komanso zimene mungachite kuti mukhale munthu wabwino

  • Kudziwa zimene mungachite kuti mukhale ndi moyo wabwino kwambiri

MAYANKHO A MAFUNSO OFUNIKA KWAMBIRI

Mwana akangophunzira kulankhula, amayamba kufunsa mafunso monga

  • N’chifukwa chiyani kumwamba kumaoneka kwa buluu?

  • Kodi nyenyezi zimapangidwa bwanji?

Akakula amayamba kufunsa mafunso okhudza zimene zimachitika padzikoli monga

Mungadabwe kudziwa kuti mayankho a mafunso onsewa alipo m’Baibulo.

Anthu ambiri amati nkhani zimene zili m’Baibulo ndi zabodza kapena ndi nthano chabe. Amatinso Baibulo ndi lachikale kapenanso ndi lovuta kulimvetsa. Koma kodi vuto ndi Baibulo kapena zimene anthuwo anamva zokhudza Baibulo?

Mwachitsanzo, anthu ena amaganiza kuti Baibulo limati Mulungu ndi amene akulamulira dzikoli? Koma kodi zimenezi ndi zoona? Taganizirani zinthu zoipa zomwe zikuchitika. Zinthu monga matenda, imfa, umphawi komanso ngozi zogwa mwadzidzidzi. Kodi Mulungu, yemwe ndi wachikondi, angapange zimenezi?

Kodi mungakonde kudziwa yankho la funso limeneli? Mwina mungadabwe kwambiri mutadziwa kuti Baibulo limati Mulungu si amene akulamulira dzikoli.

Muyenera kuti mwaona kuti malangizo amene ali m’kabukuka ndi ochokera m’Baibulo. A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza kwambiri. Zili choncho chifukwa ‘linauziridwa ndi Mulungu ndipo ndi lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula ndi kuwongola zinthu.’ (2 Timoteyo 3:16, 17) Mungachite bwino kufufuza kuti mutsimikize kuti Baibulo ndi lothandizabe masiku ano ngakhale kuti linalembedwa kalekale.