Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 1

Mulungu Anapanga Kumwamba na Dziko Lapansi

Mulungu Anapanga Kumwamba na Dziko Lapansi

Yehova Mulungu ndiye anatilenga ife. Anapanga zinthu zonse, zimene timaona na zimene sitiona. Akalibe kupanga zinthu zimene timaona, anapanga angelo ambili-mbili. Kodi angelo uwadziŵa? Angelo ndi anthu a mzimu okhala kumwamba, ofanana na Yehova. Nawonso Yehova ndiye anawalenga. Angelo sitingawaone, monga mmene sitingaonele Mulungu. Mngelo woyamba amene Yehova anapanga anakhala mthandizi wake. Mngelo ameneyo anathandiza Yehova kupanga nyenyezi, mapulaneti, na zinthu zina zonse. Imodzi mwa mapulaneti amenewo, ni dziko lapansi, limene ni malo okongola okhalapo.

Ndiyeno, Yehova anakonza bwino dziko lapansi kuti pakhale nyama ndi anthu. Anapanga dzuŵa kuti liziunika pa dziko. Anapanganso mapili, nyanja, na mitsinje.

N’ciani cina cimene anapanga? Yehova anati: ‘Nidzapanga maudzu, zomela, na mitengo.’ Panamela mitengo yolekana-lekana ya zipatso, zakudya zamasamba, na maluŵa osiyana-siyana. Kenako, Yehova anapanga zinyama zonse zouluka, zonyaya, zokwaŵa, komanso zoyendela pamimba. Anapanganso tunyama tung’ono-tung’ono monga tukalulu, komanso vikulu-vikulu monga njovu. Nanga iwe, ni nyama iti imene umakonda ngako?

Ndiyeno, Yehova anauza mngelo woyamba kuti: “Tiyeni tipange munthu.” Anthu anakhala osiyana na vinyama. Iwo anakwanitsa kupanga zinthu, kulankhula, kuseka, na kupemphela. Anali kudzasamalila dziko na vinyama. Kodi umudziŵa munthu amene anali woyamba kulengedwa? Tidzaona m’nkhani yotsatila.

“Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1