Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 2

Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba

Mulungu Anapanga Mwamuna na Mkazi Woyamba

Yehova anakonza malo okongola, na kuwacha kuti munda wa Edeni. M’mundamo munali maluŵa ambili, mitengo, na vinyama. Ndiyeno Mulungu anapanga munthu woyamba, Adamu, kucokela ku dothi, na kufuzilila mpweya m’mphuno mwake. Udziŵa cimene cinacitika? Munthu uja anakhala wamoyo! Kenako, Yehova anapatsa Adamu nchito yoyang’anila munda uja, na kumuuza kuti apatse vinyama vonse maina.

Ndiyeno Yehova anapatsa Adamu lamulo lofunika kwambili. Anamuuza kuti: ‘Ungadye zipatso za m’mitengo yonse kusiyapo cabe mtengo umodzi wapadela. Ukadzadya cipatso ca mu mtengo umenewo, udzafa.’

M’kupita kwa nthawi, Yehova anati: ‘Adamu nidzamupangila womuthandiza.’ Pamenepo Mulungu anagoneka Adamu tulo tofa nato. Ndiyeno anatengako nthiti imodzi kwa Adamu na kumupangila mkazi. Dzina lake anali Hava. Adamu na Hava anakhala banja loyamba. Kodi Adamu anamvela bwanji ataona mkazi wake? Anakondwela ngako, cakuti anakamba kuti: ‘Ha, Yehova wanipangila mkazi kucokela ku nthiti yanga! Uyu lomba, ndiye wofanana na ine.’

Yehova anauza Adamu na Hava kuti abale ana na kudzaza dziko lapansi. Anali kufuna kuti iwo azikondwela pogwila nchito pamodzi yokonza dziko lonse kukhala lokongola. Inde, kuti dziko lonse likhale monga munda wa Edeni. Koma zinthu sizinayende bwino. Cifukwa ciani? Tidzaphunzila m’nkhani yotsatila.

“Amene analenga anthu pa ciyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi.”—Mateyu 19:4