Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 3

Adamu na Hava Sanamvele Mulungu

Adamu na Hava Sanamvele Mulungu

Tsiku lina, pamene Hava anali yekha, njoka inakamba naye. Inati: ‘Kodi n’zoona kuti Mulungu anakuletsani kudyako zipatso za m’mitengo yonse?’ Hava anayankha kuti: ‘Tingadye zipatso za m’mitengo yonse kusiyapo mtengo umodzi cabe. Tikadya cipatso ca mu mtengo umenewo, tidzafa.’ Njoka inakamba kuti: ‘Simudzafa iyai. Ndipo mukadya, mudzalingana na Mulungu.’ Kodi zinali zoona? Iyai, inali bodza. Koma Hava anakhulupilila. Anaciyang’anitsitsa cipatso cija, ndipo anayamba kucikhumbila kwambili. Basi anathyola na kudya cipatsoco, na kupatsako Adamu. Adamu anali kudziŵa kuti onse adzafa ngati sadzamvela Mulungu. Koma nayenso anadyako cipatso cija.

M’madzulo tsiku limenelo, Yehova anakamba na Adamu na Hava. Anawafunsa cifukwa cake iwo sanamumvele. Hava anapatsa mlandu njoka, naye Adamu anapatsa mlandu Hava. Cifukwa Adamu na Hava sanamvele, Yehova anawacotsa m’munda wa Edeni. Pofuna kuti iwo asabwelelemo, Mulungu anaika angelo na lupanga lamoto lozungulila poloŵela m’mundawo.

Yehova anati uja amene ananamiza Hava, nayeve adzalangiwa. Si njoka yeni-yeni imene inakamba na Hava. Yehova sanapange njoka zimene zinali kukamba. Anali mngelo woipa amene anapangitsa kuti njoka ikambe. Anacita zimenezi kuti anamize Hava. Mngelo ameneyo dzina lake ni Satana Mdyelekezi. Kutsogolo, Yehova adzawononga Satana kuti asakapitilize kunamiza anthu kuti azicita vinthu voipa.

“Mdyelekezi . . . ndi wopha anthu ciyambile kupanduka kwake, ndipo sanakhazikike m’coonadi, cifukwa mwa iye mulibe coonadi.”—Yohane 8:44