Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 4

Kukwiya Mpaka Kupha Munthu

Kukwiya Mpaka Kupha Munthu

Adamu na Hava atacotsedwa m’munda wa Edeni, anabala ana ambili. Mwana wawo woyamba, Kaini, anali mlimi. Waciŵili, Abele, anali m’busa.

Tsiku lina, Kaini na Abele anapeleka nsembe kwa Yehova. Kodi udziŵa kuti nsembe n’ciani? Nsembe ni mphatso yapadela. Yehova anakondwela na nsembe ya Abele, koma sanakondwele na nsembe ya Kaini. Pa cifukwa ici, Kaini anakalipa ngako! Yehova anacenjeza Kaini kuti mkwiyo wake udzamupangitsa kucita cinthu coipa. Koma sanamvele.

M’malomwake, Kaini anauza Abele kuti: “Tiye tipite kumunda.” Pamene anali aŵili-ŵili kumunda kuja, Kaini anamenya mng’ono wake uja na kumupha. Kodi Yehova anacita ciani poona izi? Anamulanga Kaini pomupilikitsila kutali ngako na banja lawo. Ndipo sanamulole kubwelanso.

Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Nthawi zina, tingakalipe ngati zimene tifuna sizicitika. Tikamvela kuti mkwiyo wayamba kukula mu mtima mwathu, kapena ngati anthu ena aticenjeza poona mkwiyo wathu, mwamsanga tikhazike mtima pansi kuti tisacite coipa.

Cifukwa cakuti Abele anali kukonda ngako Yehova na kucita zabwino, Yehova sadzamuiŵala. Ndipo adzamuukitsa pamene adzasintha dziko lapansi kukhala paradaiso.

“Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba, ndipo ukabwelako, peleka mphatso yako.”—Mateyu 5:24