Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 5

Cingalawa ca Nowa

Cingalawa ca Nowa

M’kupita kwa nthawi anthu anaculuka pa dziko lapansi. Koma ambili anali oipa. Ngakhale angelo ena kumwamba anakhala oipa. Iwo anacoka kwawo kumwamba na kubwela pano pa dziko lapansi. Udziŵa cimene anabwelela pa dziko? Kuti adzavale matupi a anthu na kukwatila akazi.

Angelo amenewo anabala ana kwa akazi amene anakwatila. Koma viŵana vawo vinali vamphamvu komanso vankhanza. Vinali kumenya anthu. Koma Yehova sanalekelele vinthu voipa kupitiliza. Conco, anaganiza zowononga anthu oipa na cigumula ca madzi.

Koma munthu wina anali wosiyana. Anali kukonda Yehova. Dzina lake anali Nowa. Anali na mkazi komanso ana aamuna atatu. Maina a ana ake anali Semu, Hamu, na Yafeti. Ndipo aliyense wa ana amenewo anali na mkazi wake. Lomba Yehova anauza Nowa kupanga cingalawa cacikulu, kapena kuti combo, kuti iye pamodzi na banja lake akapulumukilemo pa Cigumula ca madzi. Cingalawa cili monga cibokosi cacikulu coyandama pamadzi. Yehova anauzanso Nowa kuti angenetse vinyama vambili m’combo cimeneco kuti navo vikapulumuke.

Pamenepo Nowa anayamba kupanga combo. Zinawatengela zaka pafupi-fupi 50 kuti Nowa na banja lake atsilize kupanga cingalawa. Iwo anacipanga nde-nde-nde mmene Yehova anawauzila. Pa nthawi imodzi-modzi, Nowa anali kucenjeza anthu za Cigumula ca madzi. Koma palibe amene anamumvelela.

Nthawi tsopano inafika yongena m’cingalawa. Tidzaona zimene zinakonkhapo.

“Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalile.”—Mateyu 24:37