Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 6

Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano

Anthu 8 Anapulumuka na Kulowa m’Dziko Latsopano

Nowa na banja lake, komanso vinyama, anangena m’cingalawa. Yehova anavala citseko, ndipo mvula inayamba kugwa. Mvulayo inagwa maningi cakuti combo cimeneco cinayamba kuyandama pamadzi. M’kupita kwa nthawi, dziko lonse lapansi linamila m’madzi. Anthu onse oipa amene anali kunja kwa cingalawa anafa. Koma Nowa na banja lake anali otetezeka mkati mwa cingalawa. Iwo anakondwela ngako kuti anamvela zimene Yehova anawauza.

Cimvula cinagwa kwa masiku 40 usana na usiku. Kenako cinaleka. Ndiyeno, pang’ono-pang’ono madzi anayamba kucepa. Potsilizila, combo cija cinakhazikika pa phili. Koma pansi panali madzi kulikonse. Conco Nowa na banja lake sakanatuluka m’cingalawa pa nthawiyo.

Pang’ono-pang’ono, madzi anayamba kuphwila. Nowa pamodzi na banja lake anakhala m’cingalawa kuposa caka cimodzi. Ndiyeno Yehova anawauza kuti atuluke m’cingalawa kuti akhale m’dziko looneka monga latsopano. Iwo anamuyamikila ngako Yehova cifukwa cowapulumutsa. Cakuti anapeleka nsembe yowonga zikomo kwa Yehova.

Yehova anakondwela nayo nsembe imene iwo anapeleka. Nakulonjeza kuti sadzawononganso ciliconse pa dziko lapansi na cigumula ca madzi. Ndipo anaika utawaleza m’mwamba monga cikumbutso ca lonjezo limenelo. Kodi unauonapo utawaleza?

Pambuyo pa zonsezi, Yehova anauza Nowa na banja lake kuti ayambe kubala ana na kudzaza dziko lapansi.

“Nowa analowa m’cingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka Cigumula cinafika n’kuwaseselatu onsewo.”—Mateyu 24:38, 39