Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 7

Nsanja ya Babele

Nsanja ya Babele

Pambuyo pa Cigumula, ana a Nowa pamodzi na akazi awo anabala ana ambili. Mabanja awo anakula, ndipo mogwilizana na zimene Yehova anawauza, iwo anapita kukakhala kumalo osiyana-siyana pa dziko lapansi.

Koma mabanja ena sanamvele Yehova. Iwo anati: ‘Tiyeni timange mzinda kuti tizikhala pano, ndipo nsanja yake ikafike kumwamba kweni-kweni. Tikacita zimenezi tidzachuka.’

Yehova sanakondwele na zimene anthuwo anali kucita. Conco, anawalepheletsa colinga cawo. Kodi udziŵa mmene anacitila zimenezi? Mwadzidzidzi anawapangitsa kuyamba kukamba vitundu vosiyana-siyana. Popeza kuti sanali kumvelana zimene anali kukamba, analeka nchito yomangayo. Mzinda umene iwo anali kumanga unachedwa Babele. Dzina limeneli litanthauza “Msokonezo.” Pamenepo, anthu anayamba kucoka kukakhala kumalo osiyana-siyana pa dziko lonse lapansi. Koma anapitiliza kucita vinthu voipa kumene anapita kukakhala. Kodi pali ena amene anapitiliza kukonda Yehova? Tidzaona m’nkhani yokonkhapo.

“Aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzicepetsa adzamukweza.”—Luka 18:14