Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 8

Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu

Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu

Cakufupi na mzinda wa Babele, panali mzinda wina wochedwa Uri. Anthu a mu mzindawu anali kulambila milungu ina yambili osati Yehova. Koma munali munthu wina amene anali kulambila Yehova yekha. Dzina lake anali Abulahamu.

Yehova anauza Abulahamu kuti: ‘Siya nyumba yako ndi abale ako. Upite kudziko limene ndidzakusonyeza.’ Ndiyeno Mulungu anamulonjeza kuti: ‘Iwe udzakhala mtundu waukulu, ndipo anthu ambili pa dziko lapansi ndidzawacitila zabwino cifukwa ca iwe.’

Abulahamu sanadziŵe kumene Yehova anamuuza kuti apite. Koma anadalila Yehova na mtima wonse. Conco, Abulahamu, mkazi wake Sara, atate ake a Tera, komanso Loti mwana wa m’bale wake, analonga katundu wawo wonse na kuyamba ulendo wautali.

Abulahamu anali na zaka 75 pamene anakafika na banja lake ku dziko limene Yehova anafuna kuwaonetsa. Linali dziko la Kanani. Ali kumeneko, Mulungu analonjeza Abulahamu kuti: ‘Ndidzapeleka dziko ili kwa ana ako.’ Koma pa nthawiyi, Abulahamu na Sara anali okalamba, ndipo analibe mwana aliyense. Nanga Yehova anakakwanilitsa bwanji lonjezo lake?

“Mwa cikhulupililo, Abulahamu . . . anamvela ndi kupita kumalo amene anali kuyembekezela kuwalandila monga colowa. Iye anapitadi, ngakhale sanadziŵe kumene anali kupita.”—Aheberi 11:8