Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 10

Kumbukilani Mkazi wa Loti

Kumbukilani Mkazi wa Loti

Loti anali kukhala na Abulahamu, atate ake aang’ono, m’dziko la Kanani. M’kupita kwa nthawi, Abulahamu na Loti anakhala na ziweto zambili cakuti kunalibe malo okwanila odyetselako ziweto zawo. Conco, Abulahamu anauza Loti kuti: ‘Sitingapitilize kukhalila pamodzi. Sankha malo amene ungakonde kukhalako, ndipo ine ndidzapita kumbali ina.’ Abulahamu anacita zinthu mosadzikonda, si conco?

Ndiyeno, Loti anaona malo abwino ngako kufupi na mzinda wa Sodomu. Kunali madzi ambili komanso udzu wobiliŵila. Anasankha malowo na kukukila kumeneko na banja lake. Pambuyo pake, anakukila mkati mwa mzinda wa Sodomu.

Anthu a mu Sodomu, komanso a mumzinda woyandikana nawo wa Gomora, anali oipa kwambili. Ndiye cifukwa cake Yehova anaganiza zowononga mizinda imeneyo. Koma Mulungu anafuna kupulumutsa Loti na banja lake. Conco, anatuma angelo aŵili kukawacenjeza. Angelowo anati: ‘Fulumilani! Tulukani mu mzinda uno, cifukwa Yehova adzauwononga.’

Koma Loti sanacoke pa nthawi imeneyo. Anali kungowaya-waya. Pamenepo angelowo anagwila pa dzanja Loti, mkazi wake, komanso ana ake aŵili aakazi na kuwatulutsa mumzindawo. Kenako anawauza kuti: ‘Thaŵani kuti mupulumutse moyo wanu, ndipo musayang’ane kumbuyo. Mukayang’ana kumbuyo, mudzafa!’

Atafika ku mzinda wa Zowari, Yehova anagwetsa moto na sulufule pa Sodomu na Gomora. Mizinda iŵili imeneyo inanyekelatu. Mkazi wa Loti sanamvele Yehova. Anayang’ana kumbuyo na kusanduka culu camcele! Koma Loti na ana ake aakazi anapulumuka cifukwa comvela Yehova. Anali acisoni kwambili cifukwa mkazi wa Loti sanamvele. Titengapo phunzilo lakuti kumvela Yehova ni cinthu cofunika kwambili.

“Kumbukilani mkazi wa Loti.”—Luka 17:32