Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 12

Yakobo Analandila Coloŵa

Yakobo Analandila Coloŵa

Isaki anali na zaka 40 pamene anakwatila Rabeka. Anali kum’konda ngako mkazi wake. M’kupita kwanthawi, anabala ana aŵili aamuna—amphundu.

Wamkulu anali Esau, ndipo wamng’ono anali Yakobo. Esau anali kukonda kuyenda m’thengo, anali nkhumbalume wosaka nyama. Koma Yakobo anali kukonda kukhala pa nyumba.

M’masiku amenewo, mwana wamkulu ndiye anali kupatsidwa malo aakulu na ndalama zambili ngati atate ake amwalila. Zimenezo zinali kuchedwa coloŵa. M’banja la Isaki, coloŵa cinaphatikizapo malonjezo amene Yehova analonjeza Abulahamu. Esau sanaikileko nzelu kwambili ku malonjezo amenewo, koma Yakobo anadziŵa kuti malonjezowo anali ofunika ngako.

Tsiku lina, Esau anafika pa nyumba ali wolema kwambili cifukwa cosaka nyama tsiku lonse. Pamene anamvela kununkhila kwa cakudya cimene Yakobo anali kuphika, anamuuza kuti: ‘Njala yanipha! Nipatseko cakudya cofiilaco!’ Yakobo anati: ‘Nidzakupatsa, koma coyamba lumbila kwa ine kuti udzanipatsa coloŵa cako.’ Esau anati: ‘Coloŵaco nilibe naco nchito! Ungacitenge. Ine nifuna cakudya basi.’ Kodi uganiza kuti Esau anacita cinthu canzelu? Iyai. Esau anagulitsa cinthu ca mtengo wapatali na mbale imodzi ya cakudya.

Isaki atakalamba, inali nthawi yakuti adalitse mwana wake wamkulu. Koma Rabeka anathandiza mwana wamng’ono Yakobo, kuti alandile dalitsolo. Pamene Esau anamvela zimenezo, anakalipa kwambili, ndipo anaganiza zakuti aphe mphundu mnzake. Isaki na Rabeka anafuna kuteteza Yakobo. Conco, anamuuza kuti: ‘Pita ukakhale kwa amalume ako, a Labani, mpaka Esau atabweza mkwiyo wake.’ Yakobo anamvelela makolo ake, ndipo anathaŵa kuti apulumutse moyo wake.

“Pali phindu lanji ngati munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake? N’ciani kweni-kweni cimene munthu angapeleke cosinthanitsa ndi moyo wake?”—Maliko 8:36, 37