Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 13

Yakobo ndi Esau Anagwirizananso

Yakobo ndi Esau Anagwirizananso

Yehova analonjeza Yakobo kuti amuteteza ngati mmene anatetezera Abulahamu ndi Isaki. Yakobo ankakhala ku Harana ndipo anali ndi banja lalikulu komanso chuma chambiri.

Ndiyeno Yehova anauza Yakobo kuti: ‘Bwerera kwanu.’ Choncho Yakobo ndi banja lake ananyamuka ulendo wautali wobwerera kwawo. Ali m’njira, anthu ena anamuuza kuti, ‘Esau akubwera ndipo ali ndi anthu 400.’ Yakobo anaganiza kuti m’bale wakeyo akubwera kudzamupha iyeyo limodzi ndi banja lake. Choncho anapemphera kwa Yehova kuti: ‘Chonde ndithandizeni kuti m’bale wanga asandiphe.’ Tsiku lotsatira, Yakobo anatumizira Esau mphatso zambiri monga nkhosa, mbuzi, ng’ombe, ngamila ndi abulu.

Ndiyeno usiku wa tsiku limenelo, Yakobo ali yekhayekha, anaona mngelo. Nthawi yomweyo anayamba kulimbana naye ndipo sanasiyane mpaka kunayamba kucha. Ngakhale kuti Yakobo anavulala, sanamusiye mngeloyo. Kenako mngeloyo anati: ‘Iwe ndisiye ndizipita.’ Koma Yakobo anamuyankha kuti: ‘Sindikusiya mpaka utandidalitsa.’

Choncho mngeloyo anadalitsa Yakobo. Apa tsopano Yakobo anadziwa kuti Yehova salola kuti Esau amuphe.

Ndiyeno kutacha, Yakobo anaona Esau akubwera chapatali limodzi ndi anthu 400. Yakobo anatsogola ndipo asanakumane ndi m’bale wakeyo anamugwadira ka 7. Esau anathamanga n’kukamukumbatira. Onse anayamba kulira ndipo anagwirizananso. Kodi ukuganiza kuti Yehova anamva bwanji ndi zimene Yakobo anachita pofuna kuti agwirizanenso ndi m’bale wake?

Kenako Esau anabwerera kwawo ndipo Yakobo anapitiriza ulendo wake. Yakobo anali ndi ana aamuna 12. Mayina awo anali Rubeni, Simiyoni, Levi, Yuda, Dani, Nafitali, Gadi, Aseri, Isakara, Zebuloni, Yosefe ndi Benjamini. Yehova anagwiritsa ntchito Yosefe pofuna kupulumutsa anthu ake. Kodi ukudziwa zimene zinachitika? Tikambirana zimenezi m’mutu wotsatira.

“Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani, kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.”—Mateyu 5:44, 45