Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 14

Kapolo Amene Ankamvera Mulungu

Kapolo Amene Ankamvera Mulungu

Yosefe anali wachiwiri kwa mwana womaliza wa Yakobo. Azichimwene ake anaona kuti bambo awo ankamukonda kwambiri. Kodi ukuganiza kuti iwo anasangalala ndi zimenezi? Ayi. Ankamuchitira nsanje komanso ankadana naye. Pa nthawi ina Yosefe analota maloto odabwitsa. Atawauza azichimwene akewo, iwo anaganiza kuti malotowo akutanthauza kuti tsiku lina adzamugwadira. Izi zinangowonjezera chidani chija.

Pa nthawi ina azichimwene ake a Yosefe ankadyetsa ziweto pafupi ndi mzinda wotchedwa Sekemu. Ndiyeno Yakobo anatuma Yosefe kuti akawaone ngati ali bwino. Koma iwo atamuona akubwera anayamba kuuzana kuti: ‘Wolota uja suyo akubwera apoyo? Tiyeni timuphe.’ Atatero anamugwira n’kumuponyera m’chitsime chakuya. Koma mmodzi mwa azichimwene akewo dzina lake Yuda, anati: ‘Ayi tisamuphe. Tiyeni tingomugulitsa kuti akhale kapolo.’ Choncho anamugulitsa ndi ndalama zasiliva zokwana 20 kwa amalonda achimidiyani omwe ankapita ku Iguputo.

Kenako azichimwene akewo anatenga mkanjo wa Yosefe n’kuuviika m’magazi a mbuzi. Ndiyeno atafika kunyumba anapatsa bambo awo mkanjowo n’kunena kuti: ‘Kodi mkanjo uwu mungauzindikire? Kapena ndi wa Yosefe?’ Yakobo atauona, anaganiza kuti Yosefe wadyedwa ndi chilombo. Choncho anamva chisoni kwambiri n’kuyamba kulira ndipo sankatonthozeka.

Amalonda aja atafika ku Iguputo, anamugulitsa Yosefe kwa munthu wina waudindo dzina lake Potifara. Choncho Yosefe anali kapolo. Koma Yehova anali naye. Potifara anaona kuti Yosefe anali wolimbikira ntchito komanso wodalirika. Pasanapite nthawi anaikidwa kuti aziyang’anira zinthu zonse za Potifara.

Mkazi wa Potifara anaona kuti Yosefe anali wooneka bwino komanso wamphamvu. Tsiku lililonse ankamuuza kuti agone naye. Koma Yosefe ankakana ndipo anamuuza kuti: ‘Ayi, zimenezo si zabwino. Abwana anga amandikhulupirira ndipo inuyo ndinu mkazi wawo. Ndikagona nanu ndichimwira Mulungu.’

Tsiku lina mkazi wa Potifara anakakamizanso Yosefe kuti agone naye. Moti anamugwira malaya koma Yosefe anathawa. Potifara atabwera, mkaziyo ananama kuti Yosefe amafuna kumugwiririra. Choncho Potifara anakwiya kwambiri ndipo anaika Yosefe m’ndende. Koma Yehova sanamuiwale.

“Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.”​—1 Petulo 5:6