Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 14

Kapolo Amene Anamvela Mulungu

Kapolo Amene Anamvela Mulungu

Yosefe anali mmodzi mwa ana aang’ono a Yakobo. Azikulu ake anaona kuti atate awo anali kum’konda ngako Yosefe. Kodi uganiza iwo anali kumvela bwanji? Anali kum’citila nsanje na kumuzonda. Pamene Yosefe analota maloto acilendo, anauzako abale ake za malotowo. Malotowo anaonetsa kuti tsiku lina, iwo adzamugwadila Yosefe. Apa lomba anamuzondelatu kwambili!

Tsiku lina, abale a Yosefe anali kuŵetela nkhosa pafupi na mzinda wa Sekemu. Yakobo anatuma Yosefe kuti akaone ngati abale akewo anali bwino. Pomuona akubwela capatali, iwo anayamba kukambilana kuti: ‘Onani wamaloto uja akubwela. Tiyeni timuphe!’ Basi anam’gwila na kum’ponya m’dzenje lonoka. Koma Yuda, mmodzi wa abale ake anati: ‘Osamupha! Koma tiyeni timugulitse monga kapolo.’ Conco, anagulitsa Yosefe na ndalama 20 za siliva kwa amalonda acimidiyani amene anali kupita ku Iguputo.

Ndiyeno, abale a Yosefe anaviika covala cake m’magazi a mbuzi na kucipeleka kwa atate awo, nowafunsa kuti: ‘Kodi ici si covala ca mwana wanu?’ Poona izi, Yakobo anaganiza kuti cilombo colutsa camupha Yosefe. Anayamba kulila kwambili, cakuti palibe anakwanitsa kumutonthoza.

Ku Iguputo kuja, Yosefe anam’gulitsa monga kapolo kwa nduna yolemekezeka, dzina lake Potifara. Koma Yehova anali na Yosefe. Potifara anaona kuti Yosefe anali wolimbika pa nchito, komanso kuti anali wodalilika. Pa cifukwa cimeneci, Yosefe anasankhidwa kuti aziyang’anila zinthu zonse za Potifara.

Mkazi wa Potifara anaona kuti Yosefe anali wokongola komanso wamphamvu. Tsiku na tsiku anali kunyengelela Yosefe kuti agone naye. Kodi Yosefe anacita ciani? Anakana ndipo anati: ‘Siningacite zimenezo cifukwa n’kulakwa. Abwana anga amanidalila, ndipo ndimwe mkazi wawo. Nikagona na imwe, nidzacimwa kwa Mulungu!’

Tsiku lina, mkazi wa Potifara anayesa kukakamiza Yosefe kuti agone naye. Anam’gwila covala cake, koma iye anathaŵa. Potifara atabwela ku nyumba, mkazi wake anamuuza kuti Yosefe anafuna kumugwila kuti agone naye. Koma iye anali kunama. Potifara anakalipa kwambili, cakuti anaponya Yosefe m’ndende. Koma Yehova sanamuiŵale Yosefe.

“Dzicepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.”—1 Petulo 5:6.