Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 15

Yehova Sanamuiŵalepo Yosefe

Yehova Sanamuiŵalepo Yosefe

Pamene Yosefe anali mu jele, Farao mfumu ya Iguputo, inalota maloto amene palibe anakwanitsa kuyamasulila. Koma mmodzi mwa anchito a Farao anamuuza kuti Yosefe angakwanitse kuyamasulila malotowo. Pamenepo Farao anatuma anthu kukam’bweletsa Yosefe.

Ndiyeno Farao anam’funsa kuti: ‘Kodi ungamasulile maloto anga?’ Yosefe anafotokozela Farao kuti: ‘Dziko la Iguputo lidzakhala na cakudya cambili kwa zaka 7. Zaka zina 7 zokonkhapo zidzakhala za njala. Sankhani munthu wanzelu kuti asonkhanitse cakudya kuti anthu anu asakafe na njala.’ Farao anayankha kuti: ‘Ine nasankha iwe! Udzakhala munthu wamphamvu kwambili waciŵili mu Iguputo!’ Kodi Yosefe anadziŵa bwanji tanthauzo la maloto a Farao? Yehova ndiye anam’thandiza.

Kwa zaka 7 zokonkhapo, Yosefe anali kusonkhanitsa cakudya. Ndiyeno pa dziko lonse panagwa njala monga anakambila Yosefe. Anthu anali kucokela kumadela osiyana-siyana kudzagula cakudya kwa Yosefe. Kenako Yakobo, atate ake Yosefe, anamvela kuti ku Iguputo kunali cakudya. Conco, anatuma ana ake 10 kukagula cakudya kumeneko.

Ana a Yakobo anapitadi kwa Yosefe. Atangofika kumeneko, Yosefe anawadziŵa. Koma iwo sanamudziŵe. Ndipo anam’gwadila Yosefe, monga mmene analotela akali wacicepele. Yosefe anafuna kudziŵa ngati abale akewo akali kumuzonda. Conco, anawauza kuti: ‘Ndimwe akazitape. Mwabwela kudzaona mmene dziko lathu lilili.’ Koma iwo anati: ‘Iyai! M’banja mwathu tilimo ana aamuna 12, ndipo timakhala ku Kanani. Mmodzi mwa abale athu anafa, ndipo wamng’ono ngako ali na atate wathu.’ Pamenepo Yosefe anati: ‘Mukabwele naye m’bale wanu wamng’onoyo kwa ine, kuti nikakhulupilile kuti mukamba zoona.’ Motelo, iwo anabwelela ku nyumba kwa atate awo.

Cakudya cawo citatha kaciŵili, Yakobo anatumanso ana ake kupita ku Iguputo. Apa manje, iwo anatenganso Benjamini m’bale wawo wamng’ono. Pofuna kuwayesa abale ake, Yosefe anabisa kapu yake ya siliva m’thumba limene Benjamini ananyamulilamo cakudya. Anacita izi kuti abale akewo awapeze na mlandu wakuba kapu. Anchito a Yosefe atapeza kapu m’thumba la Benjamini, abale ake anadabwa kwambili. Anapapatila Yosefe kuti iwo alangiwe m’malo mwa Benjamini.

Tsopano Yosefe anadziŵa kuti abale ake anasinthadi. Apa manje, Yosefe analephela kudzigwila. Analila kwambili, na kukamba kuti: ‘Ndine m’bale wanu Yosefe. Kodi atate anga akali moyo?’ Abale ake anadabwa kwambili. Anawauza kuti: ‘Musadziimbe mlandu cifukwa ca zimene munanicitila. Mulungu ndiye ananituma kuno kuti nidzapulumutse miyoyo yanu. Lomba pitani mwamsanga, katengeni atate mukabwele nawo kuno.’

Iwo anabwelela ku nyumba kukauza atate awo nkhani yabwino imeneyo, na kuti akapite nawo ku Iguputo. Patapita zaka zambili, Yosefe na atate ake anakhalanso pamodzi.

“Ngati simukhululukila anthu macimo awo, Atate wanu sadzakukhululukilani macimo anu.”—Mateyu 6:15