Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 16

Kodi Yobu Anali Ndani?

Kodi Yobu Anali Ndani?

M’dziko la Uzi, munali kukhala munthu wina wolambila Yehova. Dzina lake anali Yobu. Iye anali wolemela kwambili, komanso anali na banja lalikulu. Anali wokoma mtima, ndipo anali kuthandiza anthu osauka, akazi amasiye, komanso ana amasiye. Popeza Yobu anali kucita zabwino, kodi nayenso anakumanapo na mavuto?

Nthawi zonse maso a Satana Mdyelekezi anali pa Yobu, koma Yobu sanadziŵe zimenezo. Ndiyeno Yehova anati kwa Satana: ‘Kodi waona mtumiki wanga Yobu? Palibe wina wolingana naye pa dziko lapansi. Amanimvela na kucita zabwino.’ Satana anayankha kuti: ‘N’zoona kuti Yobu amakumvelani. Si paja mumam’teteza na kumudalitsa. Mwam’patsa malo okhalapo na zinyama. Zicotseni zonse, ndipo adzaleka kukulambilani.’ Yehova anati: ‘Ungamuyese Yobu, koma suyenela kumupha.’ N’cifukwa ciani Yehova analola Satana kuyesa Yobu? Cifukwa anali na cidalilo conse kuti Yobu sadzagonja.

Satana anayamba kumuyesa Yobu pomubweletsela matsoka osiyana-siyana. Coyamba, anatuma anthu ochedwa Asabeya kukaba ng’ombe komanso abulu a Yobu. Kenako, moto unawononga mbelele zonse za Yobu. Kunabwelanso anthu ena, Akasidi, amene anaba ngamila zake. Ndipo aciŵeta olishila nyama zimenezo anaphedwa. Koma tsoka lotsatila ndiye linali loipitsitsa kwambili. Ana a Yobu onse anafa pamene nyumba imene anali kucitilamo phwando inagwa. Ici cinamuŵaŵa kwambili Yobu, koma sanaleke kulambila Yehova.

Satana anafuna kuti Yobu apitilize kuvutika. Conco, anadwalitsa Yobu vilonda thupi lake lonse. Yobu anali kumvela kuŵaŵa kosaneneka. Koma sanadziŵe kuti n’cifukwa ciani zonsezi zinali kum’citikila. Ngakhale n’telo, Yobu sanaleke kulambila Yehova. Mulungu anali kuona zonsezi, ndipo anakondwela kwambili na Yobu.

Ndiyeno Satana anatuma amuna atatu kuti akamuyese Yobu. Iwo anamuuza kuti: ‘Uyenela kuti unacimwa, ndipo ufuna kubisa chimo lako. N’cifukwa cake Mulungu akukulanga.’ Yobu anati: ‘Sin’nacite chimo lililonse.’ Ndiyeno iye anayamba kuganiza kuti Yehova ndiye anali kumubweletsela mavuto. Mpaka anakamba kuti Mulungu sanamucitile cilungamo.

Koma mwamuna wamng’ono pa onse, dzina lake Elihu, anangokhala cete kumvetsela zimene iwo anali kukambilana. Pothela pake anakambapo, ndipo anati: ‘Zimene nonse mwakamba n’zolakwika. Yehova ni wamkulu ndipo amamvetsa zinthu kuposa ife. Iye sangacite cinthu coipa ciliconse. Iye amaona zonse, ndipo amathandiza anthu pa mavuto.’

Ndiyeno, Yehova anafunsa Yobu mafunso akuti: ‘Unali kuti pamene n’nali kupanga kumwamba na dziko lapansi? N’cifukwa ciani ukamba kuti sin’nacite cilungamo? Iwe sudziŵa cifukwa cake zoipa zimacitika.’ Yobu anavomeleza kulakwa kwake. Anati: ‘Ni nalakwa. N’nali kungomvela za inu, koma lomba nakudziŵani. Palibe zimene simungakwanitse kucita. Pepani kuti sin’nakambe bwino.’

Pamene mayeselo a Yobu anatha, Yehova anam’poletsa na kum’patsa zambili kuposa zimene anali nazo poyamba. Anakhalanso na moyo wautali komanso wacimwemwe. Yehova anadalitsa Yobu cifukwa comvela, ngakhale kuti zinali zovuta. Kodi na iwe udzakhala monga Yobu, na kupitiliza kulambila Yehova, olo zinthu zivute bwanji?

“Munamva za kupilila kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa.”—Yakobo 5:11