Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 17

Mose Anasankha Kuti Azilambira Yehova

Mose Anasankha Kuti Azilambira Yehova

Ku Iguputo, anthu a m’banja la Yakobo anayamba kudziwika kuti Aisiraeli. Yakobo ndi Yosefe atamwalira, Farao wina anayamba kulamulira. Iye ankachita mantha chifukwa Aisiraeli ankachuluka kuposa Aiguputo. Choncho anachititsa kuti Aisiraeli akhale akapolo. Anawalamula kuti aziumba njerwa komanso kugwira ntchito zotopetsa kumunda. Koma ngakhale kuti ankazunzidwa kwambiri ndi Aiguputo, Aisiraeli anapitirizabe kuchulukana. Popeza Farao sankafuna zimenezi, analamula kuti ana onse aamuna a Aisiraeli aziphedwa akangobadwa. Ukuganiza kuti Aisiraeli anamva bwanji lamuloli litaperekedwa?

Izi zitachitika, mayi wina wachiisiraeli, dzina lake Yokebedi anabereka mwana wamwamuna wokongola kwambiri. Pofuna kuteteza mwanayo, mayiyo anamuika m’basiketi n’kukamubisa m’mabango, mumtsinje wa Nailo. Mchemwali wake wa mwanayo, dzina lake Miriamu, anakhala chapafupi kuti azimuyang’anira.

Ndiyeno mwana wamkazi wa Farao anabwera kuti adzasambe ndipo anaona basiketi ija. Atatsegula basiketiyo anapeza kuti munali mwana. Mwanayo ankalira ndipo anamumvera chisoni. Miriamu anafunsa mwana wamkazi wa Faraoyo kuti: ‘Kodi mungakonde kuti ndikakufufuzireni munthu woti azimusamalira?’ Mwana wa Farao atavomera, Miriamu anapita n’kukauza amayi ake. Atabwera, mwana wa Faraoyo anawauza kuti: ‘Tengani mwanayu, muzikamusamalira ndipo ndizikulipirani.’

Mwana uja atakula, Yokebedi anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anamupatsa dzina loti Mose n’kumakhala naye ngati mwana wake. Mose analeredwa ngati mwana wa mfumu ndipo akanatha kupeza chilichonse chimene ankafuna. Koma iye sanaiwale Yehova. Ankadziwa kuti anali wachiisiraeli osati wa ku Iguputo ndipo anasankha kuti azitumikira Yehova.

Ali ndi zaka 40, Mose ankafuna kuthandiza Aisiraeli anzake. Choncho ataona munthu wa ku Iguputo akumenya munthu wachiisiraeli, Mose anamenya munthu wa ku Iguputoyo mpaka kumupha. Ndiyeno anakwirira munthu wakufayo mumchenga. Farao atadziwa zimenezi, ankafuna kupha Mose. Choncho Mose anathawira ku Midiyani. Kumeneko, Yehova anali naye.

“Mwa chikhulupiriro, Mose . . . anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu.”​—Aheberi 11:24, 25