Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 18

Anaona Chitsamba Chikuyaka

Anaona Chitsamba Chikuyaka

Mose anakhala ku Midiyani za 40. Iye anakwatira n’kukhala ndi ana. Tsiku lina akudyetsa nkhosa pafupi ndi phiri la Sinai, anaona zinthu zodabwitsa. Anaona chitsamba chikuyaka koma sichinkapsa. Atayandikira kuti aone zimene zikuchitika, anamva mawu ochokera m’chitsambacho akuti: ‘Mose! Usayandikire. Vula nsapato zakozo chifukwa malo amene waimawo ndi oyera.’ Yehova ndi amene ankamulankhula ndipo anagwiritsa ntchito mngelo.

Mose anachita mantha kwambiri moti anaphimba nkhope yake. Yehova anamuuza kuti: ‘Ndaona kuti Aisiraeli akuvutika kwambiri. Ndikufuna kuwapulumutsa ku Iguputo n’kuwapititsa kudziko labwino. Iweyo uwatsogolere pochoka ku Iguputo.’ Mose ayenera kuti anadabwa kwambiri ndi zimenezi.

Iye anafunsa kuti: ‘Nanga akakandifunsa kuti wakutuma ndani, ndikayankha kuti chiyani?’ Mulungu anamuuza kuti: ‘Ukawauze kuti Yehova Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo ndi amene wakutuma.’ Kenako Mose anati: ‘Nanga akakapanda kundikhulupirira?’ Zitatero, Yehova anamuuza kuti aponye ndodo yake pansi. Nthawi yomweyo ndodoyo inasanduka njoka. Koma ataigwira kumchira, inasandukanso ndodo. Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ukakachita zimenezi, akakhulupirira kuti ndakutumadi.’

Koma Mose anati: ‘Pajatu ine ndimavutika kulankhula.’ Ndiyeno Yehova anamulonjeza kuti: ‘Ineyo ndizikakuuza zoyenera kunena ndipo ndikupatsa Aroni kuti azikakuthandiza.’ Mose atadziwa kuti Yehova amuthandiza, anatenga mkazi ndi ana ake n’kuyamba ulendo wopita ku Iguputo.

“Musade nkhawa za mmene mukalankhulire kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule.”—Mateyu 10:19