Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 21

Mlili wa Namba 10

Mlili wa Namba 10

Mose analonjeza Farao kuti sadzabwelanso kwa iye. Koma pocoka, anauza Farao kuti: ‘Pakati pa usiku, mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Aiguputo adzafa. Kuyambila mwana wa Farao mpaka ana a akapolo ake, onse adzafa.’

Ndiyeno Yehova anauza Aisiraeli kuti akonze cakudya capadela. Anati: ‘Iphani mwana wa nkhosa wamphongo kapena wa mbuzi wa caka cimodzi. Mupake magazi ake pa mafelemu a pa makomo anu. Muwoche nyama yake, muidye pamodzi na mkate wopanda cofufumitsa. Muzidya mutavala nsapato zanu, kukonzekela ulendo. Usiku wa lelo nidzakumasulani.’ Ganizila cabe cimwemwe cimene Aisiraeli anali naco!

Pakati pa usiku, mngelo wa Yehova anapita pa nyumba iliyonse mu Iguputo. Ndipo anapha mwana wamwamuna woyamba pa nyumba iliyonse imene sanawaze magazi pakhomo. Koma mngeloyo anali kupitilila nyumba zimene zinali zowaza magazi. Pa banja lililonse la Aiguputo, kaya lolemela kapena losauka, panali malilo. Koma kwa Aisiraeli sikunafe mwana olo mmodzi.

Ngakhale mwana wa Farao anaphedwa. Apa lomba Farao anakhaula. Ndipo anauza Mose na Aroni kuti: ‘Nyamukani, khamani cokani. Pitani mukatumikile Mulungu wanuyo. Tengani na nyama zanu, pitani!’

Mwezi wathunthu ukuŵala usiku, Aisiraeli anacoka mu Iguputo, mwa dongosolo la mabanja awo na mafuko awo. Amuna aciisraeli analipo 600,000. Panalinso akazi ambili pamodzi ndi ana awo. Komanso, anthu ena ambili anapita nawo pamodzi kuti nawonso akalambile Yehova. Apa lomba Aisiraeli anamasuka!

Kuti Aisiraeli azikumbukila mmene Yehova anawapulumutsila, anali kukonza cakudya capadela caka ciliconse. Cakudya cimeneco cinali kuchedwa Pasika.

“Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”—Aroma 9:17