Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 23

Lonjezo kwa Yehova

Lonjezo kwa Yehova

Patapita miyezi pafupi-fupi iŵili pambuyo potuluka mu Iguputo, Aisiraeli anafika pa Phili la Sinai na kumanga msasa. Yehova anauza Mose kuti akwele m’phili. Mmenemo iye anamuuza kuti: ‘N’napulumutsa Aisiraeli. Ngati adzamvela mawu anga na kusunga malamulo anga, adzakhala anthu anga apadela.’ Mose anaseluka m’phili, na kukauza Aisiraeli zimene Yehova anakamba. Kodi iwo anati ciani? Iwo anayankha kuti: ‘Zonse zimene Yehova wakamba tidzacita zimenezo.’

Mose anakwelanso m’phili muja. Mmenemo, Yehova anamuuza kuti: ‘Pakapita masiku atatu, nidzakamba na iwe. Ukauze anthu kuti asayese kukwela m’Phili la Sinai.’ Mose anaseluka na kukauza Aisiraeli kuti akonzekele kukamvetsela kwa Yehova.

Patapita masiku atatu, Aisiraeli anaona mphenzi na mtambo wakuda bii pa phili. Anamvelanso kugunda kwamphamvu kwa mabingu na kulila kwa lipenga. Pamenepo Yehova anatsikila pa philipo m’moto. Aisiraeli anali nje-nje-nje cifukwa ca mantha. Phili lonse linagwedezeka mwamphamvu, ndipo linaphimbika mu ciutsi. Kulila kwa lipenga kunakwelela-kwelela. Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ine ndine Yehova. Musalambile milungu ina iliyonse.’

Mose anabwelelanso m’phili, ndipo Yehova anam’patsa malamulo a mmene anthuwo ayenela kulambilila Mulungu, na mmene ayenela kukhalila. Mose analemba malamulowo na kuyaŵelenga kwa Aisiraeli. Iwo analonjeza kuti: ‘Zonse zimene Yehova wakamba tidzacita zimenezo.’ Inde, iwo anapanga lonjezo kwa Mulungu. Koma kodi anasunga lonjezo lawo?

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—Mateyu 22:37