Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 25

Chihema Cholambiriramo

Chihema Cholambiriramo

Mose ali kuphiri la Sinai, Yehova anamuuza kuti akonze tenti yapadera yolambiriramo ndipo ankaitchula kuti chihema. Yehova anauza Mose kuti: ‘Uza anthu kuti akupatse zinthu zimene angakwanitse kuti upangire chihema.’ Aisiraeli anapereka golide, siliva, mkuwa, miyala yamtengo wapatali komanso zodzikongoletsera. Anaperekanso ubweya wa nkhosa, nsalu, zikopa zanyama komanso zinthu zina. Anthuwo anapereka zinthu zambiri mpaka Mose anachita kuwauza kuti: ‘Basi zakwana. Musabweretsenso zina.’

Mose anagwiritsa ntchito zinthuzi n’kupanga chihema. Aisiraeli ankalambirira Mulungu m’chihemachi ndipo anachikonza m’njira yoti azitha kuchinyamula akamayenda.

Amuna ndi akazi ambiri aluso anagwira nawo ntchito yomanga chihemachi. Yehova anawapatsa nzeru zowathandiza pogwira ntchitoyi. Ena ankapanga nsalu komanso kuzikongoletsa. Panalinso ena amene ankapanga zinthu pogwiritsa ntchito miyala, golide kapena mitengo.

Anthuwo anapanga chihema potsatira malangizo amene Yehova anawapatsa. Anapanga nsalu yokongola imene inagawa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa. M’Malo Oyera Koposa munali bokosi lotchedwa likasa la pangano. Bokosili linapangidwa ndi golide komanso matabwa a mtengo wa mthethe. M’Malo Oyera munali choikapo nyali chagolide, tebulo ndi malo aakulu operekera nsembe. Ndipo pabwalo la chihema panali beseni ndi malo enanso operekera nsembe zopsereza.

Aisiraeli anamaliza kupanga chihemachi patangotha chaka chimodzi kuchokera pamene anatuluka mu Iguputo. Apa tsopano anali ndi malo olambirira Yehova. Likasa la pangano linkakumbutsa Aisiraeli kuti analonjeza zoti azimvera Yehova. Kodi umadziwa kuti pangano n’chiyani? Ndi lonjezo lapadera limene anthu amauzana.

Yehova anasankha Aroni ndi ana ake aamuna kuti azigwira ntchito kuchihema n’kumapereka nsembe. Aroni yekha, yemwe anali mkulu wa ansembe ndi amene ankaloledwa kulowa m’Malo Oyera Koposa. Iye ankachita zimenezi kamodzi chaka chilichonse pokapereka nsembe ya machimo ake, a banja lake komanso a Aisiraeli onse.

Ulemerero wa Yehova unadzadza m’chihemacho ndipo mtambo unkakhala pamwamba pake. Mtambowo ukakhala pamwamba pa chihema, Aisiraeli ankakhalabe pamalo omwewo. Koma ukachoka, ankadziwa kuti ayenera kunyamuka. Choncho ankaphwasula chihema chija n’kumatsatira mtambowo ndipo ankakachimanga pamalo ena.

“Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: ‘Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.’”​—Chivumbulutso 21:3