Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 25

Cihema Colambililako

Cihema Colambililako

Pamene Mose anali mu Phili la Sinai, Yehova anamuuza kuti akapange tenti yapadela yochedwa cihema, kuti Aisiraeli azilambililako Mulungu. Anafunikila kumainyamula pa ulendo wawo.

Yehova anati: ‘Uza anthu kuti apeleke zimene angakwanitse, zothandizila kupanga cihema colambililako.’ Conco, Aisiraeli anapeleka golide, siliva, mkuwa, miyala yamtengo wapatali, komanso zokongoletsela monga mphete na zibangili. Anapelekanso ubweya, nsalu zokongola, vikumba va nyama, na vinthu vina vambili. Anapeleka mowolowa manja cakuti Mose anacita kuwauza kuti: ‘Basi zakwanila! Musabweletsenso zina.’

Amuna ndi akazi ambili amaluso anathandiza kupanga cihema cimeneci. Yehova anawapatsa nzelu pa nchito imeneyi. Ena anali kupanga kotoni, kuwomba nsalu, kapena kusokelapo zokongoletsa nsalu. Enanso anali kuyala miyala, kupanga ziwiya zagolide, komanso zosema zamtengo.

Anthuwo anapanga cihema ndendende mmene Yehova anawauzila. Anapanganso cinsalu cokongola colekanitsa zipinda ziŵili za cihemaco, Cipinda Coyela, na Cipinda Coyela Koposa. Mu Cipinda Coyela Koposa, munali likasa la cipangano lopangidwa na mtengo wakesha na golide. Mu Cipinda Coyela, munali coikapo nyali cagolide, thebulo, na guwa lopelekelapo nsembe zofukiza. M’bwalo munali beseni yamkuwa na guwa la nsembe lalikulu. Likasa la cipangano linali kukumbutsa Aisiraeli za lonjezo lawo lakuti adzamvela Yehova. Kodi udziŵa kuti cipangano n’ciani? Ni lonjezo lapadela.

Yehova anasankha Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe pa cihema. Nchito yawo inali kusamalila cihema, na kupeleka nsembe kwa Yehova. Aroni cabe, mkulu wa ansembe, ndiye anali kuloledwa kuloŵa mu Cipinda Coyela Koposa. Anali kuloŵamo kamodzi pacaka kukapeleka nsembe yophimba macimo ake, a banja lake, komanso a mtundu wonse wa Isiraeli.

Aisiraeli anatsiliza kupanga cihemaco patatha caka cimodzi atatuluka mu Iguputo. Lomba, anali na malo olambililako Yehova.

Yehova anadzaza cihemaco na ulemelelo wake, ndipo pamwamba pake panali mtambo. Mtambowo ukaonekela pamwamba pa cihema, Aisiraeli anali kukhalabe pamalopo. Koma mtambowo ukanyamuka, anali kudziŵa kuti ni nthawi yosamuka. Anali kumasula cihemaco akulondola mtambo uja.

“Kenako ndinamva mawu ofuula kucokela kumpando wacifumu, akuti: ‘Taonani! Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.’”—Chivumbulutso 21:3