Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 26

Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani

Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani

Aisiraeli atachoka paphiri la Sinai anadutsa m’chipululu cha Parana n’kukafika pamalo otchedwa Kadesi. Ali pamalowa, Yehova anauza Mose kuti: ‘Sankha amuna 12 kuchokera mu fuko lililonse kuti apite kukaona dziko la Kanani limene ndikufuna kukupatsani.’ Ndiyeno Mose anasankha amuna 12 n’kuwauza kuti: ‘Pitani ku Kanani mukaone ngati dzikolo ndi labwino kulimamo mbewu. Mukaonenso ngati anthu ake ali amphamvu kapena ofooka komanso ngati amakhala m’misasa kapena m’mizinda.’ Zitatere, anthuwo anauyamba ulendo wopita ku Kanani ndipo pa gululi panali Yoswa ndi Kalebe.

Patatha masiku 40, anthuwa anabwerera ndipo anatenga zipatso za nkhuyu, makangaza ndi mphesa. Iwo anati: ‘Dziko lake ndi labwino kwambiri koma anthu ake ndi amphamvu ndipo amakhala m’mizinda ya mipanda italiitali.’ Ndiyeno Kalebe anati: ‘Komabe tikhoza kuwagonjetsatu. Tiyeni tipite.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake Kalebe ananena zimenezi? Chifukwa chakuti iye ndi Yoswa ankakhulupirira kwambiri Mulungu. Koma anthu ena 10 aja anati: ‘Ayi tisapite. Anthu ake ndi akuluakulu komanso amphamvu moti ife timangooneka ngati tiziwala.’

Aisiraeli atamva zimenezi anakhumudwa kwambiri. Anayamba kudandaula kuti: ‘Tiyeni tisankhe mtsogoleri wina ndipo tibwerere ku Iguputo. Zoona tipite n’kukaphedwa?’ Koma Yoswa ndi Kalebe anati: ‘Anthuni, tiyeni timvere Yehova ndipo tisachite mantha. Yehova atiteteza.’ Komabe Aisiraeliwo sanamvere, moti mpaka ankafuna kupha Yoswa ndi Kalebe.

Kodi Yehova anatani? Iye anauza Mose kuti: ‘Aisiraeli ndawachitira zinthu zambirimbiri koma sakundimverabe. Chifukwa cha zimenezi, akhala m’chipululumu kwa zaka 40 ndipo onse afera momwemu. Amene akalowe m’dziko limene ndalonjeza ndi ana awo okha limodzi ndi Yoswa ndi Kalebe.’

“N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”​—Mateyu 8:26