Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 28

Bulu wa Balamu Akamba

Bulu wa Balamu Akamba

Aisiraeli anakhala m’cipululu kwa zaka pafupi-fupi 40. Iwo anagonjetsa mizinda yambili yolimba. Lomba, pamene anamanga msasa m’cigwa ca Moabu kum’maŵa kwa Mtsinje wa Yorodano, inali nthawi yakuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Balaki mfumu ya Moabu, anacita mantha kuti Aisiraeli adzam’landa dziko lake. Conco, iye anaitana munthu wina dzina lake Balamu, kuti abwele ku Moabu adzatembelele Aisiraeli.

Koma Yehova anauza Balamu kuti: ‘Usayese kutembelela Aisiraeli.’ Conco, Balamu anakana kuyendako. Mfumu Balaki inamuitana kaciŵili na kum’lonjeza kuti idzam’patsa ciliconse cimene angafune. Koma Balamu anakanabe. Lomba Mulungu anamuuza kuti: ‘Ungayende, koma ukakambe cabe zimene n’dzakuuza.’

Balamu anakwela bulu wake na kunyamuka ulendo wa ku Moabu. Colinga cake cinali cokatembelela Aisiraeli, ngakhale kuti Yehova anamuletsa. Mngelo wa Yehova anaonekela panjila katatu konse. Balamu sanali kumuona mngeloyo, koma bulu wake ndiye anali kumuona. Poyamba, bulu uja anapatuka panjila na kuloŵa m’munda. Kucoka apo, buluyo anakadzipanikiza kum’panda wamiyala, na kufyantha phazi la Balamu ku m’pandawo. Potsilizila pake, buluyo anangokhala pansi panjila. Pa nthawi zonsezi, Balamu anali kumenya buluyo na mtengo.

Balamu atamenya bulu wake kacitatu, Yehova anapangitsa buluyo kukamba. Buluyo anafunsa Balamu kuti: ‘N’cifukwa ciani mukungonimenya?’ Balamu anayankha kuti: ‘Cifukwa wanicititsa kukhala citsilu. N’kanakhala na lupanga n’kanakupha.’ Lomba buluyo anati: ‘Mwakhala mukunikwela kwa zaka zambili. Kodi n’nayamba nacitapo zimenezi kwa imwe?’

Pamenepo, Yehova anapangitsa Balamu kuona mngelo. Mngeloyo anati: ‘Yehova anakuletsa kutembelela Aisiraeli.’ Balamu anayankha kuti: ‘Nalakwa. Nidzangobwelela ku nyumba.’ Koma mngelo anamuuza kuti: ‘Ungapite ku Moabu, koma ukakambe cabe zimene Yehova adzakuuza.’

Kodi Balamu anaphunzilapo kanthu? Iyai. Atafika ku Moabu, Balamu anayesa kutembelela Aisiraeli katatu konse, koma nthawi iliyonse Yehova anam’pangitsa kuwadalitsa. Potsilizila pake, Aisiraeli anagonjetsa dziko la Moabu, ndipo Balamu anaphedwa. Sembe Balamu anamvela Yehova poyamba, kodi zinthu sizikanamuyendela bwino?

“Cenjelani ndi kusilila kwa nsanje kwamtundu uliwonse, cifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka cotani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15