Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 30

Rahabi Abisa Azondi

Rahabi Abisa Azondi

Azondi aciisiraeli atafika ku mzinda wa Yeriko, anakhala ku nyumba kwa mzimayi wina, dzina lake Rahabi. Mfumu ya Yeriko itamva zimenezo, inatuma asilikali ku nyumba kwa Rahabi. Koma Rahabi anabisa azondi aŵili amenewo pa mtenje, ndipo anauza asilikaliwo kuti ‘alondoleni aloŵela uku.’ Koma kumene anaŵauzako kunali kolakwika. Ndiyeno anauza azondiwo kuti: ‘N’dzakuthandizani cifukwa nidziŵa kuti Yehova ali ku mbali yanu, na kuti mudzagonjetsa dzikoli. Conde, nilonjezeni kuti mudzapulumutsa a m’banja langa.’

Azondiwo anauza Rahabi kuti: ‘Tikulonjeza kuti aliyense amene adzakhala mkati mwa nyumba yako adzapulumuka.’ Ndipo iwo anamuuza kuti: ‘Mangilila nthambo yofiila pawindo ya nyumba yako, ndipo a m’banja lako adzapulumuka.’

Rahabi anatulutsa azondi aja pawindo poseŵenzetsa nthambo. Iwo anapita kukabisala ku mapili kwa masiku atatu asanabwelele kwa Yoswa. Ndiyeno, Aisiraeli anawoloka Mtsinje wa Yorodano na kukonzekela kulanda dziko la Kanani. Mzinda wa Yeriko ndiwo unali woyamba kugonjetsedwa. Yehova anauza Aisiraeli kuyenda mozungulila mzindawo kamodzi patsiku kwa masiku 6. Koma pa tsiku la 7, anazungulila mzindawo maulendo 7. Kenako, ansembe analiza malipenga awo, ndipo asilikali anafuula mokweza kwambili. Pamenepo mpanda wa mzinda wa Yeriko unaundumuka wonse kugwela pansi! Koma nyumba ya Rahabi, imene inali pa mpandawo, siinagwe. Rahabi komanso a m’banja lake anapulumuka cifukwa cokhulupilila Yehova.

‘N’cimodzi-modzinso ndi Rahabi. Kodi Rahabi . . . sanaonedwe ngati wolungama cifukwa ca nchito zake, powalandila bwino azondi aja ndi kuwabweza kwawo powasonyeza njila ina?’—Yakobo 2:25