Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 32

Mtsogoleri Watsopano ndi Azimayi Awiri Olimba Mtima

Mtsogoleri Watsopano ndi Azimayi Awiri Olimba Mtima

Atatsogolera anthu a Yehova kwa zaka zambiri, Yoswa anamwalira ali ndi zaka 110. Pa nthawi imene iye anali moyo, Aisiraeli ankalambira Yehova. Koma atangomwalira, iwo anayamba kulambira mafano ngati mmene anthu a ku Kanani ankachitira. Chifukwa cha zimenezi, Yehova analola kuti mfumu ina ya ku Kanani dzina lake Yabini izipondereza Aisiraeli. Anthuwa anapempha kuti Yehova awathandize. Choncho Yehova anawapatsa mtsogoleri wina dzina lake Baraki. Iye anathandiza Aisiraeli kuti ayambirenso kulambira Yehova.

Ndiyeno mneneri wina wamkazi dzina lake Debora anatumizira Baraki uthenga wochokera kwa Yehova. Uthengawo unali wakuti: ‘Tenga amuna 10,000, ndipo upite kukakumana ndi asilikali a Yabini kumtsinje wa Kisoni. Kumeneko ukagonjetsa Sisera mkulu wa asilikali a Yabini.’ Baraki anauza Debora kuti: ‘Ndipita ngati iweyo ungapite nane.’ Iye anati: ‘Ndipita nawe. Koma dziwa kuti si iweyo amene ukaphe Sisera. Yehova wanena kuti amene akamuphe ndi mzimayi.’

Debora anapita limodzi ndi Baraki ndi asilikali a Barakiyo kuphiri la Tabori kukakonzekera nkhondo. Sisera atamva zimenezi, anasonkhanitsa magaleta ndi asilikali ake. Debora anauza Baraki kuti: ‘Lero Yehova akuthandiza kuti upambane pa nkhondoyi.’ Baraki ndi asilikali ake 10,000 anatsika m’phiri muja kukakumana ndi Sisera ndi asilikali ake amphamvu.

Ndiyeno Yehova anachititsa kuti mtsinje wa Kisoni usefukire. Choncho magaleta a Sisera ankangolowa m’matope. Sisera ataona kuti zavuta, anangotsika pagaleta lake n’kuyamba kuthawa. Baraki ndi asilikali ake anagonjetsa adani awo koma Sisera anathawa ndipo anakabisala mutenti ya mzimayi wina dzina lake Yaeli. Mzimayiyo anam’patsa mkaka kuti amwe ndiponso anamufunditsa bulangete. Sisera anagona tulo. Zitatero, Yaeli anayenda mwakachetechete n’kukamukhoma m’mutu ndi chikhomo cha tenti. Sisera anafera pomwepo.

Baraki anafika akusakasaka Sisera. Yaeli anatuluka mutenti yake n’kumuuza kuti: ‘Lowani mom’muno ndikuonetseni munthu amene mukufunayo.’ Baraki atalowa anaona Sisera atagona poteropo atafa. Baraki ndi Debora anaimba nyimbo yotamanda Yehova chifukwa chothandiza Aisiraeli pogonjetsa adani awo. Kwa zaka 40 zotsatira, Aisiraeli anali pa mtendere.

“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”​—Salimo 68:11