Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 32

Mtsogoleli Watsopano na Azimayi Aŵili Olimba Mtima

Mtsogoleli Watsopano na Azimayi Aŵili Olimba Mtima

Yoswa atatsogolela anthu a Yehova kwa zaka zambili, anamwalila ali na zaka 110. Pa nthawi yonse imene iye anali moyo, Aisiraeli anali kulambila Yehova. Koma pamene Yoswa anamwalila, iwo anayamba kulambila mafano, mofanana na Akanani. Cifukwa cakuti Aisiraeli analeka kutsatila Yehova, iye analola mfumu ya Akanani Yabini kuwavutitsa kwambili. Aisiraeli anacondelela Yehova kuti awathandize. Conco, Yehova anawapatsa mtsogoleli watsopano, Baraki, kuti awathandize kubwelela kwa Yehova.

Debora mneneli wamkazi, anaitana Baraki. Anafuna kumuuza uthenga wocokela kwa Yehova. Anati kwa iye: ‘Tenga amuna 10,000, ukamenyane na gulu lankhondo la Yabini ku mtsinje wa Kisoni. Kumeneko udzagonjetsa Sisera, mkulu wa gulu lankhondo la Yabini.’ Koma Baraki anayankha Debora kuti: ‘Nidzapita ngati imwe mudzapita na ine.’ Iye anayankha kuti: ‘Nidzapita nawe. Koma dziŵa kuti sindiwe amene udzapha Sisera. Yehova wakamba kuti mkazi ni amene adzamupha.’

Pamenepo, Debora na Baraki, anatenga asilikali na kukwela m’phili la Tabori kuti akakonzekele nkhondo. Sisera atamva zimenezi, anasonkhanitsa magaleta na asilikali ake, na kupita m’cigwa munsi mwa Phili la Tabori. Debora anauza Baraki kuti: ‘Lelo ni tsiku limene Yehova adzakumenyela nkhondo kuti upambane.’ Baraki na asilikali ake 10,000 anatsika m’phili kukamenyana na gulu la asilikali oyofya a Sisera.

Koma Yehova anapangitsa kuti mtsinje wa Kisoni usefukile na madzi. Basi magaleta a nkhondo a Sisera analephela, anajomba m’matika. Sisera poona izi, anasiya galeta lake n’kuthaŵa. Koma Baraki na asilikali ake anagonjetsa asilikali a Sisera, koma Sisera anathaŵa! Anakabisala mu tenti ya mzimayi wina, Yaeli. Mzimayi ameneyu anam’patsa mkaka kuti amwe, kenako anamufunda bulangete. Cifukwa colema, Sisera anagwa m’tulo. Ndiyeno Yaeli anaŵendelela Sisera na kum’khomelela cimphompho m’mutu, kapena kuti cikhomo. Sisera anafela pamenepo.

Baraki anafika akufuna-funa Sisera. Koma Yaeli anatuluka mu tenti yake nomuuza kuti: ‘Bwelani muno. Nikuonetseni munthu amene musakila.’ Baraki ataloŵa anapeza Sisera ali thasa wakufa kale. Baraki na Debora anaimbila Yehova nyimbo yomutamanda pomenyela nkhondo Aisiraeli na kugonjetsa adani awo. Pa zaka 40 zokonkhapo, Aisiraeli anakhala pa mtendele.

“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—Salimo 68:11