Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 33

Rute na Naomi

Rute na Naomi

Pamene m’dziko la Isiraeli munali njala yaikulu, mzimayi wina waciisiraeli, Naomi, anakukila ku dziko la Moabu na mwamuna wake pamodzi ndi ana awo aŵili aamuna. M’kupita kwa nthawi mwamuna wa Naomi anamwalila. Ana ake anakwatila akazi acimoabu, maina awo anali Rute na Olipa. Mwa tsoka lanji, ana a Naomi aŵiliwo nawonso anamwalila.

Naomi anamva kuti njala inasila ku Isiraeli, conco anaganiza zobwelela kwawo. Rute na Olipa anapita naye, koma m’njila Naomi anawauza kuti: ‘Munali akazi abwino kwa ana anga, komanso azipongozi abwino kwa ine. Koma nifuna kuti mukakwatiwenso. Bwelelani kwanu ku Moabu.’ Koma atsikanawo anati: ‘Timakukondani! Ndipo sitifuna kukusiyani.’ Naomi anapitiliza kuwauza kuti abwelele. Pothela pake Olipa anabwelela, koma osati Rute. Naomi anauza Rute kuti: ‘Olipa akubwelela kwa anthu ako ndi milungu yako. Pita naye pamodzi.’ Koma iye anati: ‘Sinidzakusiyani. Anthu anu adzakhala anthu anga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.’ Uganiza kuti Naomi anamvela bwanji pamene Rute anakamba zimenezi?

Rute na Naomi anafika ku Isiraeli itangoyamba nyengo yokolola balele. Tsiku lina, Rute anapita kukakunkha balele m’munda mwa munthu wina dzina lake Boazi, mwana wa Rahabi. Boazi anamva kuti Rute anali Mmoabu, ndipo anali wokhulupilika kwa Naomi. Boazi anauza anchito ake kuti azisiyako balele kuti Rute azikunkha.

M’madzulo, Naomi anafunsa Rute kuti: ‘Kodi lelo wakunkha m’munda wa ndani?’ Rute anati: ‘M’munda wa munthu wina dzina lake Boazi.’ Naomi anamuuza kuti: ‘Boazi ni m’bululu wa amuna anga. Pitiliza kukunkha m’munda mwake na atsikana ena. Udzakhala wotetezeka kumeneko.’

Rute anapitiliza kukunkha m’munda wa Boazi mpaka nthawi yokolola inasila. Boazi anaona kuti Rute anali wolimbika pa nchito, komanso anali mkazi waulemu. M’masiku amenewo, ngati mwamuna wamwalila wopanda ana aamuna, wacibale wake anali kukwatila mkazi wake wa masiyeyo. Conco Boazi anakwatila Rute. Anabala mwana dzina lake Obedi, amene anadzakhala ambuye ake a Mfumu Davide. Anzake a Naomi anakondwela maningi. Iwo anati: ‘Poyamba, Yehova anakupatsa Rute amene wakhala akukucitila zabwino, ndipo lomba uli na mdzukulu. Yehova atamandike.’

“Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana, koma pali bwenzi limene limamatilila kuposa m’bale wako.”—Miyambo 18:24