Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 37

Yehova Analankhula ndi Samueli

Yehova Analankhula ndi Samueli

Eli anali Mkulu wa Ansembe ndipo anali ndi ana awiri amene ankatumikira ngati ansembe kuchihema. Mayina awo anali Hofeni ndi Pinehasi. Anawa sankamvera malamulo a Yehova ndipo ankachitira anthu zoipa. Aisiraeli akabweretsa nsembe zoti apereke kwa Yehova iwo ankatengapo nyama yabwino n’kukadya. Eli anamva zimene ana akewa ankachita koma sanawathandize. Kodi Yehova anangoilekerera nkhaniyi?

Pa nthawiyo Samueli anali wamng’ono koma sanatengere makhalidwe oipawo ndipo Yehova ankasangalala naye. Tsiku lina atagona anamva munthu akumuitana. Iye anadzuka n’kupita kwa Eli ndipo atafika anati: ‘Ndabwera.’ Koma Eli anati: ‘Inetu sindinakuitane. Pita ukagone.’ Samueli atabwerera anamvanso kuitana kachiwiri. Ulendo wachitatu, Eli anazindikira kuti amene akumuitana ndi Yehova. Ndiyeno anamuuza kuti, akakamuitananso akayankhe kuti: ‘Lankhulani Yehova. Ine mtumiki wanu ndikumva.’

Samueli atapita kukagona anamvanso kuitana kuti: ‘Samueli! Samueli!’ Iye anayankha kuti: ‘Lankhulani. Ine mtumiki wanu ndikumva.’ Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ukamuuze Eli kuti ndimulanga iyeyo ndi banja lake. Akudziwa zoipa zimene ana ake akuchita kuchihema koma akungowalekerera.’ Kutacha, Samueli anakatsegula zitseko za chihema ngati mmene ankachitira nthawi zonse. Iye ankaopa kuuza mkulu wa ansembe zimene Yehova ananena. Koma Eli anamuitana n’kumufunsa kuti: ‘Mwana wanga, kodi Yehova anakuuza kuti chiyani? Ndiuze chilichonse.’ Zitatero, Samueli anauza Eli zonse zimene Yehova ananena.

Yehova anapitirizabe kutsogolera Samueli. Anthu a m’dziko lonse la Isiraeli ankadziwa kuti Yehova anasankha Samueli kuti akhale mneneri komanso woweruza.

“Kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”​—Mlaliki 12:1