Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 38

Yehova Anapatsa Mphamvu Samsoni

Yehova Anapatsa Mphamvu Samsoni

Aisiraeli ambili anayambanso kulambila mafano. Conco, Yehova analolela kuti Afilisiti alamulile dziko lawo. Koma panali Aisiraeli ena amene anali kukonda Yehova. Mmodzi wa iwo anali Manowa. Iye na mkazi wake analibe ana. Tsiku lina Yehova anatumiza mngelo kwa mkazi wa Manowa. Mngeloyo anamuuza kuti: ‘Udzakhala na mwana wamwamuna. Iye adzapulumutsa Aisiraeli m’manja mwa Afilisiti. Ndipo adzakhala Mnazili.’ Kodi udziŵa kuti Anazili anali a ndani? Anali atumiki a Yehova apadela. Anazili sanali kuloledwa kugela tsitsi lawo.

M’kupita kwa nthawi, mwana wa Manowa anabadwa, ndipo anam’patsa dzina lakuti Samsoni. Pamene Samsoni anakula, Yehova anam’patsa mphamvu zambili. Anakwanitsa kupha mkango na manja. Pa nthawi ina, Samsoni anapha Afilisiti 30 yekha. Afilisiti anali kumuzonda, ndipo anafunafuna njila zomuphela. Tsiku lina, Samsoni atagona usiku ku Gaza, Afilisiti anapita kukamuyembekezela pageti, kuti pocoka m’maŵa akamuphe. Koma pakati pa usiku, Samsoni anauka na kupita ku geti ya mzinda, na kunyula getiyo ku mpanda. Anainyamula getiyo pa mapewa n’kukwela nayo pamwamba pa phili, pafupi na Heburoni!

Pambuyo pake Afilisiti anapita kwa Delila, cisumbali ca Samsoni, na kumuuza kuti: ‘Tidzakupatsa ndalama za siliva masauzande ngati ungatiuze cinsinsi ca mphamvu za Samsoni. Tifuna tikamugwile kuti tikamuike mu jele.’ Delila anali kufuna ndalama, conco anavomela. Poyamba, Samsoni anakana kumuululila Delila cinsinsi ca mphamvu zake. Koma sanaleke kumuvutitsa na kumunyengelela kuti amuuze cinsinsi cake. Mpaka anaulula kuti: ‘Sin’nagelepo tsitsi langa cifukwa ndine Mnazili. Ngati ningagele tsitsi, mphamvu zanga zikhoza kutha.’ Pamenepa Samsoni analakwitsa zinthu kwambili, siconco?

Mwamsanga Delila anapita kukauza Afilisiti kuti: ‘Nadziŵa cinsinsi cake!’ Ndiyeno Delila anagoneka Samsoni m’tulo pa mendo pake, na kuuza munthu wina kuti amugele tsitsi. Kenako Delila anafuula kuti: ‘Samsoni, Afilisiti afika!’ Samsoni anagalamuka, koma anapeza kuti alibenso mphamvu. Afilisiti anamugwila, kumuboola maso, na kum’ponya m’ndende.

Tsiku lina Afilisiti ofika m’masauzande anasonkhana m’kacisi wa mulungu wawo Dagoni na kufuula kuti, ‘mulungu wathu anapeleka Samsoni m’manja mwathu! M’bweletseni kuno Samsoni! Tiyeni timuseŵeletse.’ Anamuimika pakati pa mapilala aŵili a kacisi, na kuyamba kumuseka. Koma Samsoni anapemphela kuti: ‘Inu Yehova, conde nipatseninso mphamvu zanga.’ Apa n’kuti tsitsi la Samsoni litakulanso. Pamenepo anakankha mapilala aŵili a kacisi na mphamvu zake zonse. Ndipo kacisi yense anaundumuka, n’kupha anthu onse anali mkati. Nayenso Samsoni anafa.

“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13