Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 39

Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli

Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli

Yehova anapatsa Aisiraeli oweruza kuti aziwatsogolera. Koma iwo ankafuna atakhala ndi mfumu. Ndiyeno anauza Samueli kuti: ‘Anthu a mitundu yonse ali ndi mafumu. Ifenso tikufuna tikhale ndi mfumu.’ Zimenezi sizinamusangalatse Samueli, choncho anapemphera kwa Yehova za nkhaniyi. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Anthuwa sanakane iweyo koma akukana ine. Uwauze kuti n’zotheka kuti akhale ndi mfumu koma adziwe kuti mfumuyo izidzafuna zambiri kuchokera kwa iwo.’ Koma anthuwo anati: ‘Zilibe kanthu, ife tikufuna mfumu basi.’

Yehova anamuuza Samueli kuti Sauli ndi amene akhale mfumu yoyamba. Choncho Samueli anadzoza Sauli pomuthira mafuta pamutu pamene Sauliyo anapita ku Rama kukamuona.

Kenako, Samueli anaitana Aisiraeli onse kuti awaonetse mfumu yawo. Koma Sauli sankapezeka. Ukudziwa kumene anali? Iye anali atabisala pakati pa katundu. Ndiyeno atamupeza, anamuimiritsa pakati pa anthu. Sauli anali wooneka bwino kwambiri komanso wamtali kuposa aliyense. Samueli anati: ‘Yehova wasankha ameneyu.’ Anthuwo anafuula kuti: ‘Mfumu ikhale ndi moyo wautali!’

Poyamba Sauli ankamvera Samueli komanso Yehova koma kenako anasiya. Mwachitsanzo, mfumu sinkayenera kupereka nsembe. Koma nthawi ina, ngakhale kuti Samueli anali atauza Mfumu Sauli kuti amudikire, iye anaona kuti akuchedwa. Choncho anapereka nsembe. Ndiye kodi Samueli anatani? Iye anamuuza kuti: ‘Simunachite bwino, apatu simunamvere Yehova.’ Koma Sauli sanaphunzirepo kanthu.

Nthawi ina, Sauli atapita kukamenyana ndi a Amaleki, Samueli anamuuza kuti akawononge chilichonse m’dzikolo. Koma iye anasiya mfumu yakumeneko dzina lake Agagi, osaipha. Yehova anauuza Samueli kuti: ‘Sauli wasiya kunditsatira ndipo sakundimvera.’ Samueli atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri ndipo anapita kukauza Sauli kuti: ‘Chifukwa simukumvera Yehova, iye asankha mfumu ina.’ Pamene Samueli ankatembenuka kuti azipita, Sauli anagwira malaya ake akunja ndipo anang’ambika. Zitatero, Samueli anamuuza kuti: ‘Yehova wang’amba ufumu ndi kuuchotsa kwa inu.’ Izi zinatanthauza kuti Yehova adzapereka ufumuwo kwa munthu amene amamukonda komanso kumumvera.

‘Kumvera kumaposa nsembe.’​—1 Samueli 15:22