Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 40

Davide na Goliyati

Davide na Goliyati

Yehova anauza Samueli kuti: ‘Pita ku nyumba ya Jese. Mmodzi wa ana ake adzakhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli.’ Conco, Samueli anapita ku nyumba kwa Jese. Ataona mwana wamkulu wa Jese, mu mtima mwake anati: ‘Mnyamata uyu ndiye amene wasankhidwa.’ Koma Yehova anauza Samueli kuti sanali ameneyo. Yehova anati: ‘Nimayang’ana mtima wa munthu, osati maonekedwe ake.’

Jese anabweletsa ana ake ena 6 kwa Samueli. Koma Samueli anati: ‘Yehova sanasankhe aliyense pa awa. Kodi ulibe ana ena?’ Jese anati: ‘Nili na mnyamata wina wamng’ono kwambili, Davide. Wapita kukalishila nkhosa.’ Pamene Davide anabwela, Yehova anauza Samueli kuti ‘Uyu ndiye amene nam’sankha!’ Samueli anathila mafuta pa mutu pa Davide, kum’dzoza kukhala mfumu ya Aisiraeli ya kutsogolo.

M’kupita kwa nthawi, Aisiraeli anali pa nkhondo na Afilisiti, amene anali na ciphona cochedwa Goliyati. Tsiku na tsiku, ci Goliyati cinali kunyoza Aisiraeli. Cinali kufuula kuti: ‘Sankhani munthu amene angamenyane na ine. Ngati adzanigonjetsa, tidzakhala akapolo anu. Koma ngati nidzamugonjetsa, imwe mudzakhala akapolo athu.’

Davide anapeleka cakudya ca abale ake amene anali ku nkhondo, ku msasa wa asilikali aciisiraeli. Ndipo anamvela zimene ci Goliyati cinali kukamba. Iye anati: ‘Ine ningamugonjetse!’ Koma Mfumu Sauli anati: ‘Iwe ndiwe mwana.’ Koma Davide anati: ‘Yehova adzanithandiza.’

Sauli anauza Davide kuti avale covala cake causilikali, koma Davide anati: ‘Siningakwanitse kumenya nkhondo na ivi.’ Davide anatenga gulaye wake na kupita ku mtsinje. Kumeneko anasankha miyala isanu yosalala n’kuiika m’kacola kake. Kenako Davide anathamangila kwa Goliyati. Ciphona cija cinayamba kuufula kuti: ‘Bwela, kamwana iwe. Nidzakupanga cakudya ca mbalame na nyama zakuchile.’ Koma Davide sanacite mantha. Iye anafuula kuti: ‘Iwe ubwela kwa ine na lupanga na mkondo, koma ine nibwela kwa iwe m’dzina la Yehova. Sukulimbana na ise, ukulimbana na Mulungu. Aliyense pano adzaona kuti lupanga na mkondo si kanthu kwa Yehova. Adzapeleka nonsenu m’manja mwathu!’

Pamenepo Davide anaika mwala m’gulaye wake, na kuuponya na mphamvu zake zonse. Mwa thandizo la Yehova, mwala uja unangoti phofo, n’kuloŵelatu pa mphumi pa Goliyati. Basi ci Goliyati wuu pansi khu! n’kufelatu. Afilisiti poona conco anabalalika kuthaŵa. Kodi iwe umadalila Yehova mmene Davide anacitila?

“Kwa anthu n’zosathekadi, koma sizili conco kwa Mulungu, pakuti zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.”—Maliko 10:27