Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 41

Davide ndi Sauli

Davide ndi Sauli

Davide atangopha Goliyati, Mfumu Sauli inamuuza kuti akhale mkulu wa asilikali. Davide anapambana nkhondo zambiri ndipo anatchuka kwabasi. Akamabwera kunkhondo, akazi ankavina komanso kuimba kuti: ‘Sauli wapha adani masauzande koma Davide wapha masauzande makumimakumi.’ Izi zinapsetsa mtima Sauli moti anayamba kufuna kupha Davide.

Davide ankadziwa kuimba zeze. Tsiku lina akuimbira Sauli nyimbo, Sauliyo anaponya mkondo wake kuti amuphe. Davide anazinda ndipo mkondowo unafikira pakhoma. Kungoyambira pamenepo, Sauli ankayesetsa kuti amuphe basi. Izi zinachititsa kuti Davide athawire kuchipululu.

Sauli anatenga asilikali 3,000 n’kumakasakasaka Davide. Ndiyeno tsiku lina analowa kuphanga limene kunali Davide ndi anzake. Anzake a Davidewo anati: ‘Uwutu ndi mwayi wako kuti uphe Sauli.’ Davide anangoyenda chokwawa n’kukadula kansalu pa chovala cha Sauli koma Sauliyo sanadziwe chilichonse. Zitatero, Davide anadandaula kwambiri kuti sanalemekeze mfumu yodzozedwa ndi Mulungu. Iye sanalole kuti anzakewo aphe Sauli. Kenako Sauli atatuluka m’phangamo, Davide anafuula n’kumuuza kuti anali ndi mpata woti amuphe koma anangomusiya. Kodi Sauli anasintha maganizo?

Ayi ndithu. Anapitirizabe kusakasaka Davide. Tsiku lina usiku, Davide ndi m’bale wake dzina lake Abisai anapita pamalo amene Sauli anagona ndi asilikali ake. Anapeza kuti Abineri amene ankalondera mfumu nayenso anali atagona. Ndiyeno Abisai anati: ‘Mwayitu suposa apa. Bwanji ndimuphe?’ Koma Davide anati: ‘Ayi. Ameneyutu adzalangidwa ndi Yehova. Tiye tingotenga mkondo wake ndi mtsuko wake wa madziwu tizipita.’

Kenako Davide anakakwera paphiri lina lapafupi n’kufuula kuti: ‘Iwe Abineri! Ungogona osateteza mfumuyo? Kodi mkondo wake ndi madzi ake zili kuti?’ Sauli atazindikira mawu a Davide anati: ‘Mpata woti undiphe unaupeza koma wandikomera mtima. Ndazindikira tsopano kuti iwe udzakhaladi mfumu ya Isiraeli.’ Apa tsopano Sauli anabwerera kwawo. Koma sikuti anthu onse a m’banja la Sauli ankadana ndi Davide.

“Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere. Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.”​—Aroma 12:18, 19