Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 41

Davide na Sauli

Davide na Sauli

Pamene Davide anapha Goliyati, Mfumu Sauli anam’sankha kukhala mkulu wa asilikali ake. Davide anapambana nkhondo zambili, ndipo anachuka ngako. Anali kuti Davide akabwelako ku nkhondo, azimayi anali kuvina uku akuimba, amvekele: ‘Sauli wakantha masauzande, koma Davide wakantha masauzande ambilimbili!’ Sauli anacitila nsanje Davide, ndipo anayamba kufuna kumupha.

Davide anali kudziŵa bwino kuliza zeze. Tsiku lina Davide ali kuimbila mfumu Sauli zeze, mfumuyo inaponya mkondo wake kuti imulase. Mwamsanga Davide analewa, ndipo mkondo uja unalasa pa cipupa. Sauli anayesanso maulendo ambili kuti aphe Davide. Pothela pake, Davide anathaŵila ku cipululu kukabisala.

Koma Sauli anatenga asilikali okwana 3,000, na kupita kukamusakila Davide. Mwatsoka, Sauli analoŵa ku phanga kumene kunali Davide na asilikali ake. Asilikali a Davide anamuŵeleŵesha kuti: ‘Uyu ndiye mwayi wanu kuti muphe Sauli.’ Davide anaŵendelela Sauli na kudula kansalu ku covala cake cacifumu. Sauli sanadziŵe ciliconse. Pambuyo pake, cinamuŵaŵa kwambili Davide kuti sanalemekeze mfumu yodzozedwa ya Yehova. Conco, sanalole kuti asilikali ake aphe Sauli. Koma anafuulila Sauli na kumuuza kuti akanafuna akanamupha. Kodi Sauli anasintha maganizo ake ofuna kupha Davide?

Iyai sanasinthe. Sauli anapitiliza kusakila Davide. Tsiku lina usiku Davide na mwana wa m’bale wake, Abisai, anamyomyolokela mu msasa wa asilikali a Sauli. Ngakhale Abineri mlonda wa Sauli, anali mtulo. Abisai anaŵeleŵesha kuti: ‘Uyu ndiye mwayi wathu! Niloleni nimugwaze.’ Koma Davide anati: ‘Yehova ndiye adzakantha Sauli. Tiye titenge cabe mkondo na cikho cake tipite.’

Davide anakwela m’phili la pafupi, ndipo msasa wa asilikali a Sauli unali kuonekela pansi. Ndiyeno anafuula kuti: ‘Abineri, n’cifukwa ciani sunateteze mfumu yako? Kodi cikho na mkondo wa Sauli zili kuti?’ Sauli anawadziŵa mawu a Davide, ndipo anati: ‘Ukanandipha lelo, koma sunatelo. Nidziŵa kuti udzakhala mfumu ya Isiraeli.’ Sauli anabwelela ku nyumba yake yacifumu. Koma si onse a m’banja la Sauli amene anali kumuzonda Davide.

“Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendele ndi anthu onse, monga mmene mungathele. Okondedwa, musabwezele coipa, koma siyilani malo mkwiyo wa Mulungu.” —Aroma 12:18, 19