Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 42

Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika

Yonatani, Munthu Wolimba Mtima Komanso Wokhulupilika

Yonatani, mwana woyamba wa Sauli, anali msilikali wolimba mtima. Davide anati Yonatani anali wa liŵilo kuposa ciwombankhanga, komanso wamphamvu kuposa mkango. Tsiku lina, Yonatani anaona asilikali 20 acifilisiti ali pa phili. Anauza womunyamulila zida kuti: ‘Tidzamenyana nawo kokha ngati Yehova watipatsa cizindikilo. Ngati Afilisiti atiuza kuti tipite, ndiye kuti tiyenela kumenyana nawo.’ Kenako Afilisiti anafuula kuti: ‘Bwelani timenyane!’ Conco, amuna aŵiliwo anakwela phili na kugonjetsa asilikaliwo.

Cifukwa Yonatani anali mwana woyamba wa Sauli, ndiye akanatenga ufumu kwa atate ake. Yonatani anali kudziŵa kuti Yehova anasankha Davide kukhala mfumu yotsatila ya Aisiraeli. Koma sanam’citile nsanje. Yonatani na Davide anakhala mabwenzi apamtima. Iwo analonjezana kuti adzatetezana. Yonatani anapatsa Davide covala cake, lupanga, uta, na lamba monga cizindikilo ca ubwenzi wawo.

Pamene Davide anali kuthaŵa Sauli, Yonatani anapita kwa Davide n’kumuuza kuti: ‘Khala wamphamvu ndipo limba mtima. Yehova anakusankha kukhala mfumu. Ngakhale atate anga adziŵa bwino zimenezi.’ Kodi ungakonde kukhala na bwenzi labwino monga Yonatani?

Kangapo konse, Yonatani anaika moyo wake paciswe kuti athandize bwenzi lake. Anadziŵa kuti Mfumu Sauli anali kufuna kupha Davide. Conco, anauza atate ake kuti: ‘Mukapha Davide mudzacimwa. Iye sanacite colakwa ciliconse.’ Koma Sauli anamukwiila kwambili Yonatani. Patapita zaka, Sauli na Yonatani onse anafa pa nkhondo.

Yonatani atamwalila, Davide anapita kukafuna-funa Mefiboseti, mwana wa Yonatani. Atam’peza anamuuza kuti: ‘Cifukwa atate ako anali bwenzi langa lapamtima, nidzakusamalila moyo wako wonse. Udzakhala m’nyumba yanga yacifumu ndi kudya pa thebulo langa.’ Davide sanamuiŵale bwenzi lake Yonatani.

“Mukondane monga mmene inenso ndakukondelani. Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.”—Yohane 15:12, 13