Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 43

Chimo ya Mfumu Davide

Chimo ya Mfumu Davide

Pamene Sauli anamwalila, Davide anakhala Mfumu, ali na zaka 30. Atalamulila kwa zaka, tsiku lina ali pa mtenje wa nyumba yake, anaona mkazi wokongola. Davide atafufuza anapeza kuti mkaziyo anali Bati-seba, ndipo mwamuna wake anali Uriya msilikali. Davide anaitanitsa Bati-seba kuti abwele ku nyumba yake. Kenako anagona naye. Ndipo mkaziyo anakhala na mimba. Davide anayesa kubisa chimo lake. Anauza mkulu wa asilikali ake kuti akaike Uriya kutsogolo ku nkhondo. Anati ena akabwelele m’mbuyo kuti iye akaphedwe. Uriya ataphedwa ku nkhondo, Davide anakwatila Bati-seba.

Koma Yehova anaona zoipa zonse zimene Davide anacita. Kodi iye anacitapo ciani? Yehova anatuma mneneli Natani kuti apite kwa Davide. Iye anati kwa Davide: ‘Munthu wina wolemela anali na nkhosa zambili, ndipo panalinso wina wosauka amene anali na kankhosa kamodzi cabe kakang’ono, kamene anali kukakonda kwambili. Koma munthu wolemela uja analanda munthu wosauka kankhosa kamodzi kameneko.’ Davide anatamva izi anakwiya kwambili, ndipo anati: ‘Munthu wolemelayo afunika kuphedwa!’ Pamenepo Natani anauza Davide kuti: ‘Munthu wolemelayo ndiwe amene!’ Davide anamva cisoni kwambili, ndipo anauza Natani kuti: ‘Nacimwila Yehova.’ Chimo limenelo linabweletsa mavuto ambili kwa Davide na banja lake. Yehova anamulanga Davide. Koma cifukwa anali woona mtima ndi wodzicepetsa, anamulola kukhalabe na moyo.

Davide anafuna kumangila Yehova kacisi. Koma Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti akamange kacisi. Conco, Davide anayamba kusonkhanitsila Solomo zomangila. Ndipo anati: ‘Kacisi wa Yehova afunika kukhala wokongola ngako. Solomo ni wamng’ono, koma nidzam’thandiza kusonkhanitsa zinthu zomangila kacisi.’ Davide anapeleka ndalama zambili kuti zithandize pa nchito yomanga. Ndipo anapeza anchito aluso. Anasonkhanitsanso golide, siliva, na mapulanga amtengo wamkungudza ocokela ku Turo na ku Sidoni. Atatsala pang’ono kumwalila, Davide anapatsa Solomo mapulani akamangidwe ka kacisi. Ndipo anati: ‘Yehova ananiuza kuti nikulembele mapulani akamangidwe ka kacisi. Yehova adzakuthandiza. Usacite mantha. Limba mtima, ugwile nchitoyi mwamphamvu.’

“Wobisa macimo ake zinthu sizidzamuyendela bwino, koma woulula n’kuwasiya adzacitilidwa cifundo.”—Miyambo 28:13